Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Deuteronomo 33:1-29

33  Tsopano ili ndi dalitso+ limene Mose, munthu wa Mulungu woona,+ anadalitsa nalo ana a Isiraeli iye asanafe.  Ndipo anati: “Yehova anafika kuchokera ku Sinai,+ Anathwanima pa iwo kuchokera ku Seiri.+ Anawala kuchokera kudera lamapiri la Parana,+ Ndipo anali ndi miyandamiyanda ya oyera ake,+ Kudzanja lake lamanja kunali ankhondo ake.+   Iye analinso kukonda anthu ake.+ Oyera awo onse ali m’manja mwanu.+ Iwowa anakhala pansi, pamapazi panu.+ Anayamba kulandira ena mwa mawu anu.+   (Mose anatipatsa chilamulo,+ Chimene mpingo wa Yakobo uli nacho monga chawo.)+   Mulungu anakhala mfumu mu Yesuruni,*+ Pamene atsogoleri a anthu anasonkhana pamodzi,+ Chiwerengero chonse cha mafuko a Isiraeli.+   Rubeni akhale ndi moyo, asafe ayi,+ Ndipo anthu ake asakhale ochepa.”+  Popitiriza, iye anapereka dalitso lotsatirali kwa Yuda,+ kuti: “Inu Yehova, imvani mawu a Yuda,+ M’bweretseni kwa anthu ake. Manja ake amenya nkhondo pofuna kulanditsa zinthu zake. Mukhaletu mthandizi wake kwa adani ake.”+  Ndipo kwa Levi anati:+ “Tumimu ndi Urimu+ wanu ndizo za munthu wokhulupirika kwa inu,+ Amene munamuyesa pa Masa.+ Munayamba kulimbana naye pafupi ndi madzi a Meriba.+   Munthu amene anauza bambo ndi mayi ake kuti, ‘Sindinawaone.’ Ngakhale abale ake sanawavomereze,+ Ndipo ana ake sanawadziwe. Pakuti anasunga mawu anu,+ Ndipo anapitiriza kusunga pangano lanu.+ 10  Amenewa azilangiza Yakobo pa zigamulo zanu,+ Ndi Isiraeli m’chilamulo chanu.+ Azipereka nsembe zofukiza kuti muzinunkhiza fungo lake,+ Ndi nsembe yathunthu paguwa lanu lansembe.+ 11  Inu Yehova dalitsani mphamvu zake,+ Ndipo mukondwere ndi ntchito ya manja ake.+ Muvulaze koopsa ziuno za amene akumuukira,+ Ndi amene amadana naye kwambiri, kuti asamuukire.”+ 12  Kwa Benjamini anati:+ “Wokondedwa+ wa Yehova akhale m’chitetezo cha Mulungu,+ Pamene akumutchinjiriza tsiku lonse,+ Ndipo iye akhale pakati pa mapewa ake.”+ 13  Ndipo kwa Yosefe anati:+ “Dziko lake lipitirize kudalitsidwa ndi Yehova.+ Lidalitsidwe ndi zinthu zabwino kwambiri zakumwamba, mame,+ Ndi madzi akuya a pansi pa nthaka.+ 14  Lidalitsidwenso ndi zinthu zabwino kwambiri, zochokera ku dzuwa,+ Ndi zinthu zabwino kwambiri, zokolola za miyezi yosiyanasiyana,+ 15  Lidalitsidwe ndi zinthu zabwino koposa, za m’mapiri a kum’mawa,+ Ndi zinthu zabwino kwambiri za m’mapiri amene adzakhalapo mpaka kalekale. 16  Lidalitsidwe ndi zinthu zabwino kwambiri za padziko lapansi, ndi chuma chake chonse,+ Komanso movomerezedwa ndi Iye amene anaonekera m’chitsamba chaminga.+ Zimenezi zikhale pamutu pa Yosefe,+ Paliwombo pa munthu wopatulidwa pakati pa abale ake.+ 17  Ulemerero wake ndi wofanana ndi wa mwana wa ng’ombe wamphongo woyamba kubadwa,+ Ndipo nyanga zake ndi nyanga za ng’ombe yam’tchire yamphongo.*+ Nyanga zimenezo adzakankha nazo anthu.+ Adzakankha nazo anthu onse pamodzi mpaka kukafika kumalekezero a dziko lapansi. Nyanga zimenezo ndi anthu masauzande makumimakumi a fuko la Efuraimu,+ Ndiponso anthu  masauzande a fuko la Manase.” 18  Kwa Zebuloni anati:+ “Kondwera Zebuloni iwe, pa maulendo ako,+ Ndiponso iwe Isakara, m’mahema ako.+ 19  Adzaitanira mitundu ya anthu kuphiri. Kumeneko adzapereka nsembe zachilungamo.+ Pakuti adzayamwa chuma chochuluka cha m’nyanja,+ Ndi chuma chobisika cha mumchenga.” 20  Ndipo kwa Gadi anati:+ “Wodala ndi iye wofutukula malire a dera la Gadi.+ Iye adzakhala ngati mkango,+ Ndipo adzakhadzula dzanja, adzang’amba mutu paliwombo.+ 21  Adzatenga gawo labwino kwambiri kukhala lake,+ Pakuti gawo loperekedwa ndi wopereka  malamulo linasungidwa kumeneko.+ Ndipo atsogoleri a anthu adzasonkhana. Iye adzachitadi chilungamo cha Yehova, Ndi zigamulo zokhudza Isiraeli.” 22  Kwa Dani anati:+ “Dani ndi mwana wa mkango.+ Adzadumpha kuchokera ku Basana.”+ 23  Ndipo kwa Nafitali anati:+ “Nafitali wakhutira chifukwa chovomerezedwa ndi Yehova, Ndipo madalitso Ake amuchulukira. Tenga chigawo cha kumadzulo ndi kum’mwera.”+ 24  Kwa Aseri anati:+ “Aseri ndi wodalitsidwa ndi ana aamuna.+ Akhale wovomerezeka ndi abale ake,+ Woponda phazi lake m’mafuta.+ 25  Chitsulo ndi mkuwa ndizo zokhomera chipata chako,+ Udzayenda mtima uli phee, masiku onse a moyo wako. 26  Palibe wina wofanana ndi Mulungu woona+ wa Yesuruni,+ Amene amayenda m’mlengalenga pokuthandiza,+ Amene amayenda pamitambo mu ulemerero wake.+ 27  Mulungu wakale lomwe ndiwo malo ako obisalamo,+ Ndipo iwe uli m’manja amene adzakhalapo mpaka kalekale.+ Adzapitikitsa mdani pamaso pako,+ Ndipo adzanena kuti, ‘Awononge!’+ 28  Isiraeli adzakhala motetezeka,+ Kasupe wa Yakobo adzakhala mosatekeseka,+ M’dziko lokhala ndi chakudya ndi vinyo watsopano.+ Ndipo kumwamba kwake kudzagwetsa mame.+ 29  Ndiwe wodala Isiraeli iwe!+ Ndani angafanane ndi iwe,+ Anthu amene  akupulumutsidwa  ndi Yehova,+ Chishango chako chokuthandiza,+ Amenenso ndi lupanga lako lopambana?+ Adani ako adzakhala mwamantha chifukwa cha iwe,+ Ndipo iwe udzayendayenda pamalo awo okwezeka.”+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa De 32:15.
Mwina nyama imeneyi inali yooneka ngati njati.