Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Deuteronomo 32:1-52

32  “Tamverani kumwamba inu, ndiloleni ndilankhule. Ndipo dziko lapansi limve mawu a pakamwa panga.+   Malangizo anga adzagwa ngati mvula,+ Mawu anga adzatsika ngati mame,+ Ngati mvula yowaza pa udzu,+ Ngatinso mvula yamphamvu pazomera.+   Pakuti ndidzalengeza dzina la Yehova.+ Vomerezani ukulu wa Mulungu wathu!+   Iye ndi Thanthwe, ndipo ntchito yake ndi yangwiro,+ Njira zake zonse ndi zolungama.+ Mulungu wokhulupirika,+ amene sachita chosalungama.+ Iye ndi wolungama ndi wowongoka.+   Iwo achita okha zinthu zowawonongetsa,+ Si ana ake, chilemacho n’chawo.+ Iwo ndiwo m’badwo wopotoka maganizo ndi wokhotakhota!+   Kodi mukupitiriza kuchitira Yehova mwa njira imeneyi,+ Anthu opusa ndi opanda nzeru inu?+ Kodi iye si Atate wanu amene anakulengani,+ Amene anakupangani ndi kukuchititsani kukhazikika?+   Kumbukirani masiku akale,+ Ganizirani zaka za mibadwomibadwo ya m’mbuyomu. Funsa bambo ako ndipo akuuza,+ Amuna achikulire pakati panu, ndipo akufotokozera.+   Pamene Wam’mwambamwamba anapereka cholowa kwa mitundu,+ Pamene analekanitsa ana a Adamu,+ Anaika malire a anthu+ Poganizira chiwerengero cha ana a Isiraeli.+   Pakuti gawo la Yehova ndilo anthu ake.+ Yakobo ndiye gawo la cholowa chake.+ 10  Anam’peza m’dziko lachipululu,+ M’chipululu chopanda  kanthu, molira  zilombo zakutchire.+ Pamenepo anayamba kum’zungulira,+ kum’samalira,+ Kum’teteza monga mwana wa diso lake.+ 11  Monga mmene chiwombankhanga chimagwedezera mwamphamvu chisa chake, Mmene chimaulukira pamwamba pa ana ake,+ Mmene chimatambasulira mapiko ake, ndi kutenga anawo, N’kuwanyamula pamapiko ake,+ 12  Yehova yekha anapitiriza kumutsogolera,+ Ndipo panalibe mulungu wachilendo kuwonjezera pa iye.+ 13  Anapitiriza kumuyendetsa pamapiri a dziko lapansi,+ Moti anadya zokolola za m’minda.+ Anapitirizanso kumudyetsa uchi wochokera m’thanthwe,+ Ndi mafuta ochokera m’mwala wa nsangalabwi.+ 14  Anamudyetsanso mafuta a mkaka wa ng’ombe ndi mkaka wa nkhosa,+ Pamodzi ndi mafuta a nkhosa. Anamudyetsa nkhosa zamphongo za ku Basana, mbuzi zamphongo,+ Pamodzi ndi tirigu wabwino koposa ngati mafuta okuta impso.+ Ndipo anali kumwa magazi a mphesa monga vinyo.+ 15  Yesuruni*+ atayamba kunenepa, anayamba kupanduka.+ Iwe wanenepa, wakulupala, wakhuta mopitirira muyezo.+ Pamenepo iye anasiya Mulungu amene anam’panga,+ Ndi kunyoza Thanthwe+ la chipulumutso chake. 16  Anayamba kuputa nsanje+ yake ndi milungu yachilendo.+ Anapitiriza kumukhumudwitsa ndi zinthu zonyansa.+ 17  Iwo anali kupereka nsembe kwa ziwanda, osati kwa Mulungu.+ Anapereka nsembe kwa milungu imene sanaidziwe,+ Milungu yatsopano yongobwera kumene,+ Imene makolo anu akale sanaidziwe. 18  Munaiwala Thanthwe limene linakuberekani,+ Ndipo munayamba kuiwala Mulungu amene anachititsa kuti mukhalepo kudzera mwa zowawa za pobereka.+ 19  Yehova ataona zimenezi anayamba kuwanyoza,+ Chifukwa chakuti ana ake aamuna ndi aakaziwo anam’sautsa. 20  Choncho iye anati, ‘Ndiwabisire nkhope yanga,+ Ndione kuti ziwathera bwanji. Pakuti iwo ndi m’badwo wokonda zoipa,+ Ana osakhulupirika.+ 21  Iwo andichititsa nsanje ndi milungu yachabe.+ Andisautsa ndi mafano awo opanda pake.+ Ndipo ine ndidzawachititsa nsanje ndi anthu achabe,+ Ndidzawakhumudwitsa ndi mtundu wopusa.+ 22  Pakuti pa kukwiya kwanga moto wayaka,+ Ndipo udzayaka mpaka kukafika ku Manda,* malo a pansi penipeni.+ Udzanyeketsa dziko lapansi ndi zipatso zake,+ Ndi kuyatsa maziko a mapiri.+ 23  Ndidzawonjezera masoka awo,+ Mivi yanga ndidzaithera pa iwo.+ 24  Adzalefuka ndi njala+ ndi kuwonongeka ndi matenda otentha thupi koopsa,+ Ndi chiwonongeko chowawa.+ Ndidzawatumizira zilombo za mano ataliatali,+ Pamodzi ndi njoka zapoizoni za m’fumbi.+ 25  Kunja lupanga lidzawasandutsa anamfedwa,+ Ndipo mkati mwa nyumba, mantha adzawasandutsa anamfedwa.+ Zimenezi zidzawaphera anyamata ndi anamwali,+ Mwana woyamwa pamodzi ndi munthu wa imvi.+ 26  Ndikananena kuti: “Ndidzawabalalitsa,+ Ndidzachititsa anthu kuti asatchule n’komwe za iwo,”+ 27  Ngati ndikanati sindikuopa kusautsidwa ndi mdani,+ Kuti adani awo angamve molakwa,+ Kutinso anganene kuti: “Dzanja lathu lapambana,+ Ndipo si Yehova amene wachita zonsezi.”+ 28  Pakuti iwo ndi mtundu wopanda nzeru,+ Ndipo ndi osazindikira.+ 29  Akanakhala anzeru,+ akanaganizira mozama zimenezi.+ Akanalingalira kuti ziwathera bwanji.+ 30  Kodi munthu mmodzi angathamangitse bwanji anthu 1,000, Kapena anthu awiri angapitikitse bwanji anthu 10,000?+ N’zosatheka, pokhapokha Thanthwe lawo litawagulitsa,+ Komanso ngati Yehova atawapereka. 31  Pakuti thanthwe lawo silofanana ndi Thanthwe lathu,+ Ndipo adani athu angavomereze zimenezi.+ 32  Mtengo wawo wa mpesa ndi wochokera ku mtengo wa mpesa wa ku Sodomu, Ndi kuminda ya m’mapiri a ku Gomora.+ Zipatso zawo za mphesa ndi zakupha, Ndipo ndi zowawa.+ 33  Vinyo wawo ndi poizoni wa njoka zikuluzikulu, Ndiponso ndi poizoni wakupha wa mamba.+ 34  Kodi sindinasunge zimenezi, Ndi kuziikira chidindo m’nkhokwe yanga?+ 35  Kubwezera ndi kwanga, chilangonso ndi changa.+ Pa nthawi yoikidwiratu phazi lawo lidzaterereka poyenda,+ Pakuti tsiku la tsoka lawo layandikira,+ Ndipo zowagwera zikufika mofulumira.’+ 36  Pakuti Yehova adzaweruza anthu ake,+ Ndipo adzamva chisoni chifukwa cha atumiki ake,+ Chifukwa adzaona kuti thandizo lawachokera. Adzaona kuti pangokhala munthu wonyozeka ndi wopanda pake. 37  Pamenepo iye adzati, ‘Ili kuti milungu yawo,+ Thanthwe limene anathawirako,+ 38  Milungu imene inali kudya mafuta a nsembe zawo,+ Ndi kumwa vinyo wa nsembe zawo zachakumwa?+ Ibwere kudzakuthandizani.+ Ikhaletu malo anu obisalamo.+ 39  Onani tsopano kuti ndine Mulungu,+ Ndipo palibe milungu ina pamodzi ndi ine.+ Ndimapha ndiponso ndimapereka moyo.+ Ndavulaza koopsa,+ ndipo ine ndidzachiritsa,+ Palibe aliyense wonditsomphola m’dzanja langa.+ 40  Ndikukweza dzanja langa kumwamba polumbira,+ Ndipo ndikunena kuti: “Pali ine, Mulungu wamoyo wosatha,”+ 41  Ndikanoladi lupanga langa lonyezimira,+ Dzanja langa likagwira chiweruzo,+ Ndidzalipsira adani anga,+ Ndipo ndidzabwezera chilango kwa odana nane kwambiri.+ 42  Ndidzaledzeretsa mivi yanga ndi magazi,+ Magazi a anthu ophedwa ndi ogwidwa. Ndipo lupanga langa lidzadya nyama,+ Pamodzi ndi mitu ya atsogoleri a adani.’+ 43  Kondwerani, mitundu inu, pamodzi ndi anthu ake,+ Pakuti adzabwezera magazi a atumiki ake,+ Ndipo adzabwezera chilango kwa adani ake,+ Nadzaphimba machimo a dziko la anthu ake.” 44  Pamenepo Mose anabwera ndi kulankhula mawu onse a nyimbo iyi m’makutu mwa anthu onse,+ iye pamodzi ndi Hoseya* mwana wa Nuni.+ 45  Mose atamaliza kulankhula mawu onsewa kwa Aisiraeli onse, 46  anapitiriza kuwauza kuti: “Ganizirani mofatsa mawu onse amene ndikulankhula mokuchenjezani lero,+ ndipo muuze ana anu kuti aonetsetse kuti akuchita zimene mawu onse a chilamulo ichi akunena.+ 47  Pakuti amenewa si mawu opanda pake kwa inu,+ chifukwa mawu amenewa ndiwo moyo wanu.+ Mwa kutsatira mawu amenewa mudzatalikitsa masiku anu panthaka imene mukupita kukaitenga kukhala yanu, mutawoloka Yorodano.”+ 48  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose pa tsiku lomweli kuti: 49  “Kwera m’phiri ili la Abarimu,+ phiri la Nebo,+ limene lili m’dziko la Mowabu, moyang’anana ndi Yeriko, ndipo uone dziko la Kanani limene ndikupereka kwa ana a Isiraeli kuti likhale lawo.+ 50  Pamenepo ukafera m’phiri limene ukukwera ndi kugona ndi makolo ako,+ monga mmene Aroni m’bale wako anafera m’phiri la Hora+ ndi kugona ndi makolo ake. 51  Izi zili choncho chifukwa anthu inu munachita mosakhulupirika kwa ine+ pakati pa ana a Isiraeli, kumadzi a pa Meriba+ ku Kadesi, m’chipululu cha Zini. Ndiponso chifukwa chakuti anthu inu simunandilemekeze pakati pa ana a Isiraeli.+ 52  Pakuti udzaona dzikolo uli patali, koma sudzalowa m’dziko limene ndikupereka kwa ana a Isiraeli.”+

Mawu a M'munsi

Kutanthauza “Wolungama.” Limeneli ndi dzina laulemu la Isiraeli.
Onani Zakumapeto 5.
Dzina lakale la Yoswa.