Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Deuteronomo 31:1-30

31  Pamenepo Mose anapita ndi kukauza Aisiraeli onse mawu awa,  kuti: “Tsopano ndili ndi zaka 120.+ Sindidzaloledwanso kupitiriza ntchito yanga yokutsogolerani,+ pakuti Yehova wandiuza kuti, ‘Suwoloka Yorodano uyu.’+  Yehova Mulungu wanu akuwoloka patsogolo panu kuti akutsogolereni.+ Iye ndiye adzawononga mitundu imeneyi pamaso panu, ndipo inu mudzaipitikitse.+ Yoswa ndiye adzakutsogolerani ndi kukuwolotsani,+ monga mmene Yehova wanenera.  Ndipo Yehova adzachitira mitundu imeneyi zimene anachitira Sihoni+ ndi Ogi,+ mafumu a Aamori, ndiponso zimene anachitira dziko lawo, pamene anawawononga.+  Yehova wapereka mitunduyi kwa inu,+ ndipo muichitire mogwirizana ndi malamulo onse amene ndakupatsani.+  Limbani mtima ndipo chitani zinthu mwamphamvu.+ Musawaope kapena kuchita nawo mantha,+ chifukwa Yehova Mulungu wanu ndi amene akuyenda patsogolo panu. Iye sadzakutayani kapena kukusiyani ngakhale pang’ono.”+  Pamenepo Mose anaitana Yoswa ndi kumuuza pamaso pa Aisiraeli onse kuti: “Limba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu,+ chifukwa ndiwe amene udzalowetsa anthu awa m’dziko limene Yehova analumbirira makolo awo kuti adzawapatsa.+ Ndipo iwe ndi amene udzawapatsa dzikolo monga cholowa chawo.  Yehova ndi amene akuyenda patsogolo panu. Iye adzapitiriza kuyenda nanu.+ Sadzakutayani kapena kukusiyani ngakhale pang’ono. Choncho musaope kapena kuchita mantha.”+  Pamenepo Mose analemba chilamulo chimenechi+ ndi kuchipereka kwa ansembe, ana a Levi,+ onyamula likasa la pangano la Yehova.+ Anachiperekanso kwa akulu onse a Isiraeli. 10  Ndiyeno Mose anawalamula kuti: “Kumapeto kwa zaka 7 zilizonse, pa nthawi yoikidwiratu m’chaka chopuma,+ pachikondwerero cha misasa,+ 11  pamene Aisiraeli onse afika kudzaona nkhope ya Yehova+ Mulungu wanu pamalo amene iye adzasankhe,+ muziwerenga chilamulo ichi pamaso pa Aisiraeli onse m’makutu mwawo.+ 12  Sonkhanitsani anthu,+ amuna, akazi, ana ndi alendo okhala m’mizinda yanu, kuti amvetsere ndi kuphunzira,+ pakuti ayenera kuopa Yehova Mulungu wanu+ ndi kutsatira mosamala mawu onse a m’chilamulo ichi. 13  Ana awo amene sadziwa chilamulo ichi azimvetsera,+ ndipo aphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu masiku onse amene mudzakhala panthaka imene mukupita kukaitenga kukhala yanu,+ mutawoloka Yorodano.” 14  Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Taona, nthawi ya kufa kwako yayandikira.+ Itana Yoswa, ndipo muime m’chihema chokumanako kuti ndimuike kukhala mtsogoleri.”+ Choncho Mose ndi Yoswa anapita ndi kukaima m’chihema chokumanako.+ 15  Ndiyeno Yehova anaonekera kuchihemako, mumtambo woima njo ngati chipilala, ndipo mtambowo unaima pakhomo la chihema.+ 16  Tsopano Yehova anauza Mose kuti: “Iweyo ugona pamodzi ndi makolo ako,+ ndipo anthu awa adzaimirira+ ndi kuchita chiwerewere pakati pawo ndi milungu yachilendo ya m’dziko limene akupita.+ Iwo adzandisiya+ ndi kuphwanya pangano limene ndinapangana nawo.+ 17  Pamenepo mkwiyo wanga udzawayakira tsiku limenelo,+ ndipo ndidzawasiya+ ndi kuwabisira nkhope yanga,+ motero adzakhala chinthu choyenera kuwonongedwa. Masoka ndi zowawa zambiri zidzawagwera,+ ndipo pa tsiku limenelo adzanena kuti, ‘Masoka amenewatu akutigwera chifukwa chakuti Mulungu wathu sali pakati pathu.’+ 18  Koma ine ndidzawabisira nkhope yanga pa tsiku limenelo chifukwa cha zoipa zonse zimene achita, chifukwa chotembenukira kwa milungu ina.+ 19  “Tsopano dzilembereni nyimbo iyi+ ndi kuwaphunzitsa ana a Isiraeli.+ Muiike m’kamwa mwawo kuti nyimbo imeneyi ikhale mboni yanga pamaso pa ana a Isiraeliwo.+ 20  Pakuti ndidzawalowetsa m’dziko limene ndinalumbirira makolo awo,+ dziko loyenda mkaka ndi uchi.+ Kumeneko iwo adzadya+ ndi kukhuta, ndipo adzatukuka+ ndi kutembenukira kwa milungu ina.+ Adzatumikira milungu imeneyo ndi kundichitira chipongwe, ndipo adzaphwanya pangano langa.+ 21  Ndiyeno masoka ndi zowawa zambiri zikadzawagwera,+ nyimboyi idzawayankha monga mboni, chifukwa siyenera kuchoka pakamwa pa mbadwa zawo, pakuti ndikudziwa mtima+ umene akuyamba kukhala nawo lero ndisanawalowetse m’dziko limene ndawalumbirira.” 22  Chotero Mose analemba nyimboyi pa tsiku limeneli kuti aphunzitse ana a Isiraeli.+ 23  Ndiyeno Mulungu anaika Yoswa mwana wa Nuni+ kukhala mtsogoleri, ndipo anamuuza kuti: “Limba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu,+ chifukwa iwe ndi amene udzalowetsa ana a Isiraeli m’dziko limene ndawalumbirira,+ ndipo ine ndidzapitiriza kukhala nawe.” 24  Mose atangomaliza kulemba mawu onse a chilamulo ichi m’buku,+ 25  anayamba kupereka malamulo kwa Alevi onyamula likasa la pangano la Yehova,+ kuti: 26  “Tengani buku ili la chilamulo,+ muliike pambali pa likasa+ la pangano la Yehova Mulungu wanu, kuti likhale mboni ya Mulungu yokutsutsani.+ 27  Pakuti ineyo ndikudziwa bwino khalidwe lanu lopanduka+ ndi kuuma khosi kwanu.+ Ngati lero pamene ndili moyo pamodzi nanu mwasonyeza khalidwe lopandukira Yehova,+ ndiye kuli bwanji pambuyo pa imfa yanga! 28  Sonkhanitsani akulu onse a mafuko anu ndi atsogoleri anu,+ kuti ndilankhule mawu awa m’makutu mwawo, ndipo nditenge kumwamba ndi dziko lapansi kukhala mboni zanga pamaso pawo.+ 29  Pakuti ndikudziwa bwino kuti pambuyo pa imfa yanga, mosakayikira mudzachita zinthu zokuwonongetsani+ ndipo mudzapatuka ndi kusiya njira imene ndakulamulani kuyendamo. Pamapeto pake tsoka+ lidzakugwerani, chifukwa mudzachita zoipa pamaso pa Yehova ndi kumulakwira ndi ntchito za manja anu.”+ 30  Chotero Mose anayamba kulankhula mawu onse a nyimbo iyi, mpingo wonse wa Isiraeli ukumva,+ ndipo anati:

Mawu a M'munsi