Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Deuteronomo 30:1-20

30  “Ndiyeno zikadzachitika kuti mawu onsewa akwaniritsidwa pa inu, madalitso+ ndi matemberero+ amene ndakuikirani pamaso panu, ndipo mwakumbukira mawu amenewa mumtima mwanu+ muli pakati pa mitundu yonse kumene Yehova Mulungu wanu adzakubalalitsirani,+  moti mwabwerera kwa Yehova Mulungu wanu+ ndi kumvera mawu ake ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse,+ mogwirizana ndi zonse zimene ndikukulamulani lero, inuyo ndi ana anu,  Yehova Mulungu wanu adzabweza kwawo anthu a mtundu wanu amene anagwidwa ndi kupita kudziko lina,+ ndipo adzakumverani chifundo+ n’kukusonkhanitsaninso pamodzi kuchokera pakati pa anthu onse kumene Yehova Mulungu wanu anakubalalitsirani.+  Anthu a mtundu wanu obalalitsidwawo akadzakhala kumalekezero kwa thambo, Yehova Mulungu wanu adzakusonkhanitsani ndi kukutengani kumeneko.+  Choncho Yehova Mulungu wanu adzakulowetsanidi m’dziko limene makolo anu analitenga kukhala lawo, ndipo inu mudzalitenga kukhala lanu. Pamenepo, adzakuchitirani zabwino ndi kukuchulukitsani kuposa makolo anu.+  Yehova Mulungu wanu adzachita mdulidwe wa mitima yanu+ ndi mitima ya ana anu,+ kuti muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, kuti mukhale ndi moyo.+  Ndipo Yehova Mulungu wanu adzaikadi matemberero onsewa pa adani anu, ndi onse odana ndi inu amene anakuzunzani.+  “Koma iwe udzatembenuka ndi kumvera mawu a Yehova ndi kutsatira malamulo ake onse amene ndikukupatsa lero.+  Ndipo Yehova Mulungu wako adzakuchititsa kukhala ndi zinthu zosefukira pa ntchito iliyonse ya manja ako,+ chipatso cha mimba yako, chipatso cha ziweto zako+ ndi chipatso cha nthaka yako.+ Pamenepo udzatukuka+ chifukwa Yehova adzakondweranso nawe kuti akuchitire zabwino, monga mmene anakondwera ndi makolo ako.+ 10  Adzachita zimenezi popeza udzamvera mawu a Yehova Mulungu wako ndi kusunga malamulo ake ndi mfundo zake zolembedwa m’buku ili la chilamulo,+ chifukwa udzabwerera kwa Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse ndi moyo wako wonse.+ 11  “Lamulo limene ndikukupatsa lero si lovuta kwa iwe kulitsatira, ndipo si lapatali.+ 12  Silili kumwamba kuti unene kuti, ‘Ndani adzakwera kumwamba ndi kukatitengera lamulolo kuti ife tilimve ndi kulitsatira?’+ 13  Ndiponso silili tsidya lina la nyanja kuti unene kuti, ‘Ndani adzawoloka kupita tsidya lina la nyanja kukatitengera lamulolo kuti ife tilimve ndi kulitsatira?’ 14  Pakuti mawu a chilamulowo ali pafupi kwambiri ndi iwe, ali m’kamwa mwako ndi mumtima mwako+ kuti uwatsatire.+ 15  “Taona, ine ndikuika pamaso pako lero moyo ndi zinthu zabwino, imfa ndi zinthu zoipa.+ 16  [Ngati udzamvera malamulo a Yehova Mulungu wako,] amene ndikukupatsa lero ndi kukonda Yehova Mulungu wako,+ kuyenda m’njira zake ndi kusunga malamulo ake,+ mfundo zake ndi zigamulo zake,+ pamenepo udzakhaladi ndi moyo+ ndi kuchulukana. Ndipo Yehova Mulungu wako adzakudalitsa m’dziko limene ukupita kukalitenga kukhala lako.+ 17  “Koma mtima wako ukatembenukira kwina ndipo sukumvera,+ moti wanyengeka, n’kugwadira milungu ina ndi kuitumikira,+ 18  ndikukuuzani lero kuti mudzatheratu.+ Simudzatalikitsa masiku anu panthaka imene mukupita kukaitenga kukhala yanu mutawoloka Yorodano. 19  Ndaika moyo ndi imfa, dalitso+ ndi temberero+ pamaso panu.+ Kumwamba ndi dziko lapansi ndi mboni pa zochita zanu.+ Choncho inuyo ndi mbadwa zanu+ musankhe moyo kuti mukhalebe ndi moyo.+ 20  Musankhe moyo mwa kukonda Yehova Mulungu wanu,+ kumvera mawu ake ndi kum’mamatira,+ chifukwa iye ndiye wokupatsani moyo ndi masiku ambiri+ kuti mukhale panthaka imene Yehova analumbira kwa makolo anu, Abulahamu, Isaki ndi Yakobo kuti adzawapatsa.”+

Mawu a M'munsi