Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Deuteronomo 27:1-26

27  Mose pamodzi ndi akulu a Isiraeli anapitiriza kuuza anthuwo kuti: “Muzisunga lamulo lililonse limene ndikukupatsani lero.+  Mukawoloka Yorodano+ ndi kulowa m’dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, muimike miyala ikuluikulu ndi kuipaka utoto woyera.  Ndiyeno mukawoloka,+ mulembe pamiyalapo mawu onse a chilamulochi+ kuti mulowe m’dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, dziko loyenda mkaka ndi uchi, malinga ndi zimene Yehova Mulungu wa makolo anu wakuuzani.+  Choncho mukawoloka Yorodano, muimike miyala imeneyi paphiri la Ebala,+ monga mmene ndakulamulirani lero, ndipo muipake utoto woyera.+  Mumangirenso Yehova Mulungu wanu guwa lansembe kumeneko, guwa lansembe lamiyala. Musaseme miyalayo ndi chipangizo chilichonse chachitsulo.+  Muzigwiritsa ntchito miyala yathunthu pomangira Yehova Mulungu wanu guwa lansembe, ndipo muzipereka nsembe zopsereza kwa Yehova Mulungu wanu paguwalo.+  Muzipereka nsembe zachiyanjano+ ndi kuzidyera pamenepo,+ ndipo muzikondwera pamaso pa Yehova Mulungu wanu.+  Mulembe mawu onse a chilamulochi pamiyalayo,+ muwalembe moonekera bwino.”+  Kenako Mose ndi ansembe achilevi analankhula ndi Aisiraeli onse kuti: “Aisiraeli inu, khalani chete ndi kumvetsera. Lero mwakhala anthu a Yehova Mulungu wanu.+ 10  Choncho muzimvera mawu a Yehova Mulungu wanu ndi kusunga malamulo+ ndi malangizo ake,+ amene ndikukupatsani lero.” 11  Tsiku limenelo Mose anapitiriza kulankhula ndi anthuwo kuti: 12  “Amene adzaimirira ndi kudalitsa anthu paphiri la Gerizimu+ mukawoloka Yorodano ndi awa: Simiyoni, Levi, Yuda, Isakara, Yosefe ndi Benjamini. 13  Amene adzaimirira kuti avomere pamene matemberero+ akutchulidwa paphiri la Ebala+ ndi awa: Rubeni, Gadi, Aseri, Zebuloni, Dani ndi Nafitali. 14  Pamenepo Alevi azinena mawu awa mokweza kuuza mwamuna aliyense wa Isiraeli+ kuti: 15  “‘Wotembereredwa ndi munthu aliyense wopanga chifaniziro chosema+ kapena chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo chosungunula+ ndi kuchibisa. Chifanizirocho ndi chinthu chonyansa kwa Yehova,+ Mulungu wopanga manja a mmisiri wa matabwa ndi zitsulo.’+ (Anthu onse ayankhe kuti, ‘Zikhale momwemo!’)*+ 16  “‘Wotembereredwa ndi munthu wonyoza bambo ake kapena mayi ake.’+ (Anthu onse ayankhe kuti, ‘Zikhale momwemo!’) 17  “‘Wotembereredwa ndi munthu wosuntha chizindikiro cha malire a mnzake.’+ (Anthu onse ayankhe kuti, ‘Zikhale momwemo!’) 18  “‘Wotembereredwa ndi munthu wosocheretsa wakhungu.’+ (Anthu onse ayankhe kuti, ‘Zikhale momwemo!’) 19  “‘Wotembereredwa ndi munthu wopotoza+ chiweruzo+ cha mlendo wokhala pakati panu,+ mwana wamasiye* ndi mkazi wamasiye.’+ (Anthu onse ayankhe kuti, ‘Zikhale momwemo!’) 20  “‘Wotembereredwa ndi munthu wogona ndi mkazi wa bambo ake, chifukwa wavula bambo akewo.’+ (Anthu onse ayankhe kuti, ‘Zikhale momwemo!’) 21  “‘Wotembereredwa ndi munthu wogona nyama iliyonse.’+ (Anthu onse ayankhe kuti, ‘Zikhale momwemo!’) 22  “‘Wotembereredwa ndi munthu wogona ndi mlongo wake, mwana wamkazi wa bambo ake kapena mwana wamkazi wa mayi ake.’+ (Anthu onse ayankhe kuti, ‘Zikhale momwemo!’) 23  “‘Wotembereredwa ndi mwamuna wogona ndi apongozi ake.’+ (Anthu onse ayankhe kuti, ‘Zikhale momwemo!’) 24  “‘Wotembereredwa ndi munthu wobisalira mnzake ndi kumupha.’+ (Anthu onse ayankhe kuti, ‘Zikhale momwemo!’) 25  “‘Wotembereredwa ndi munthu wolandira chiphuphu kuti akanthe ndi kupheratu munthu, kuti akhetse magazi a munthu wosachimwa.’+ (Anthu onse ayankhe kuti, ‘Zikhale momwemo!’) 26  “‘Wotembereredwa ndi munthu amene sadzatsatira mawu a m’chilamulo ichi ndipo sadzawagwiritsa ntchito.’+ (Anthu onse ayankhe kuti, ‘Zikhale momwemo!’)

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “Ame!” m’Chiheberi.
Mawu ake enieni, “mwana wamwamuna wopanda bambo.”