Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Deuteronomo 20:1-20

20  “Mukapita kunkhondo kukamenyana ndi adani anu, musachite nawo mantha mukaona kuti ali ndi mahatchi ndi magaleta ankhondo,+ ndiponso mukaona kuti adani anuwo ndi ochuluka kwambiri kuposa inu. Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani m’dziko la Iguputo ali ndi inu.+  Mukayandikira kuti mumenyane nawo, wansembe azifika pafupi nanu ndi kulankhula ndi anthu+  kuti, ‘Mverani Aisiraeli inu. Lero mukuyandikira adani anu kuti mumenyane nawo. Mitima yanu isachite mantha.+ Musaope ndipo musathawe mwamantha kapena kunjenjemera chifukwa cha iwo,+  chifukwa Yehova Mulungu wanu akuyenda limodzi nanu kuti akumenyereni nkhondo ndi kukupulumutsani kwa adani anu.’+  “Atsogoleri+ nawonso azilankhula ndi anthuwo kuti, ‘Kodi pali amene wamanga nyumba yatsopano koma sanaitsegulire? Achoke ndi kubwerera kunyumba yakeyo, kuopera kuti angafe pankhondo, ndipo munthu wina angatsegulire nyumbayo.+  Kodi pali amene walima munda wa mpesa koma sanayambe kukolola zipatso zake? Achoke ndi kubwerera kunyumba yake, kuopera kuti angafe pankhondo ndipo munthu wina angakolole za m’munda wakewo.+  Kodi pali amene analonjeza mkazi kuti adzamukwatira ndipo sanamutenge? Achoke ndi kubwerera kunyumba yake,+ kuopera kuti angafe pankhondo ndipo mwamuna wina angatenge mkaziyo.’  Ndiyeno atsogoleri apitirize kulankhula ndi anthuwo kuti, ‘Kodi pali wamantha ndi wosalimba mtima?+ Achoke ndi kubwerera kunyumba yake, kuti angachititse mantha mitima ya abale ake ngati mmene wachitira mtima wake.’+  Atsogoleriwo akamaliza kulankhula ndi anthu, azisankha akulu a magulu ankhondo oti akhale patsogolo pa anthuwo. 10  “Mukayandikira mzinda kuti mumenyane nawo, muzilengeza kumzindawo mfundo za mtendere.+ 11  Ndiyeno ngati mzindawo wakupatsani yankho la mtendere ndipo akutsegulirani zipata zake, pamenepo anthu onse opezeka mmenemo azikhala anu kuti azikugwirirani ntchito yaukapolo. Iwo azikutumikirani.+ 12  Koma ngati mzindawo sukukhazikitsa mtendere ndi inu,+ ndipo ukuchita nanu nkhondo, moti inuyo mwauzungulira, 13  Yehova Mulungu wanu adzaupereka ndithu m’manja mwanu, ndipo zikatero muzipha mwamuna aliyense ndi lupanga.+ 14  Koma musaphe akazi, ana aang’ono,+ ziweto+ ndi chilichonse chopezeka mumzindawo. Muzifunkha+ zinthu zonse za mumzindawo ndipo muzidya zimene mwafunkha kwa adani anu amene Yehova Mulungu wanu wakupatsani.+ 15  “Muzichita zimenezi ndi mizinda yonse yakutali kwambiri ndi inu imene siili pakati pa mizinda ya mitundu iyi. 16  Mizinda yokhayi ya anthu awa a mitundu ina imene Yehova Mulungu wanu akukupatsani monga cholowa, ndi imene simuyenera kusiyamo chilichonse chopuma chili chamoyo,+ 17  chifukwa muyenera kuwawononga ndithu. Mukawononge Ahiti, Aamori, Akanani, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi,+ monga mmene Yehova Mulungu wanu anakulamulirani. 18  Mukawawononge kuti asakakuphunzitseni kuchita zinthu zawo zonse zonyansa zimene achitira milungu yawo, kuti mungachimwire Yehova Mulungu wanu.+ 19  “Mukazungulira mzinda kwa masiku ambiri mwa kumenyana nawo kuti muulande, musawononge mitengo yake mwa kuisamulira nkhwangwa. Muyenera kudya zipatso za mitengoyo, chotero simuyenera kuidula.+ Kodi mtengo wa m’munda ndi munthu kuti muwuukire? 20  Mungathe kuwononga mtengo wokhawo umene mukuudziwa kuti subereka zipatso zakudya. Mtengo woterowo mungaudule ndi kumangira mpanda wozungulira+ mzinda wa adani umene ukuchita nanu nkhondo, kufikira mzindawo utagwa.

Mawu a M'munsi