Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Deuteronomo 2:1-37

2  “Ndiyeno tinatembenuka ndi kulowera kuchipululu kudzera njira ya ku Nyanja Yofiira, monga mmene Yehova anandiuzira.+ Ndipo tinayenda masiku ambiri m’dera lapafupi ndi phiri la Seiri.  Kenako Yehova anandiuza kuti,  ‘Mwayenda kwa nthawi yaitali m’dera lapafupi ndi phirili.+ Tembenukani ndi kulowera kumpoto.  Auze anthuwo kuti: “Mukudutsa m’malire a dziko la abale anu,+ ana a Esau,+ amene akukhala m’Seiri.+ Iwo adzachita nanu mantha,+ choncho muyenera kukhala osamala kwambiri.  Musalimbane nawo, chifukwa sindikupatsani dziko lawo, ngakhale kachigawo kokwana phazi limodzi lokha. Ndinapereka phiri la Seiri kwa Esau kuti likhale malo ake.+  Mudzadya chakudya chimene mudzagula kwa iwo ndi ndalama, ndipo mudzamwa madzi amene mudzagula kwa iwo ndi ndalama.+  Yehova Mulungu wanu wakudalitsani pa chilichonse chimene dzanja lanu likuchita.+ Iye akudziwa za kuyenda kwanu kudutsa m’chipululu chachikulu ichi. Yehova Mulungu wanu wakhala nanu zaka 40 zimenezi,+ ndipo simunasowe kanthu.”’+  Chotero tinalambalala abale athu, ana a Esau,+ amene akukhala m’Seiri, ndipo sitinayende njira ya Araba,+ Elati ndi Ezioni-geberi.+ “Kenako tinatembenuka ndi kudutsa njira ya m’chipululu cha Mowabu.+  Pamenepo Yehova anandiuza kuti, ‘Usavutitse Amowabu kapena kuchita nawo nkhondo, chifukwa sindidzakupatsa mbali iliyonse ya dziko lawo kuti likhale lako. Ndinapereka Ari+ kwa ana a Loti kuti akhale malo awo.+ 10  (Kale munali kukhala Aemi,+ anthu amphamvu kwambiri ndiponso ochuluka. Iwo anali ataliatali ngati Aanaki.+ 11  Arefai+ anali kuonedwanso ngati Aanaki,+ ndipo Amowabu anali kutcha Arefaiwo kuti Aemi. 12  Kale Ahori+ anali kukhala m’Seiri, ndipo ana a Esau+ anawalanda dzikolo ndi kuwapha. Atatero, ana a Esauwo anayamba kukhala m’dzikolo,+ monga mmene ana a Isiraeli ayenera kuchitira m’dziko lawo, limene Yehova adzawapatsa ndithu.) 13  Choncho nyamukani ndi kudutsa chigwa* cha Zeredi.’ Pamenepo tinadutsadi chigwa cha Zeredi.+ 14  Ndipo masiku amene tinayenda kuchokera ku Kadesi-barinea mpaka kuwoloka chigwa cha Zeredi anali zaka 38, kufikira m’badwo wa amuna otha kupita kunkhondo utatha pakati panu, monga mmene Yehova analumbirira kwa iwo.+ 15  Dzanja+ la Yehova linali pa iwo kuwasautsa ndi kuwachotsa pakati panu, kufikira onse atatha.+ 16  “Ndiyeno amuna onse otha kupita kunkhondo atatha kufa pakati pa anthu,+ 17  Yehova analankhulanso ndi ine, kuti, 18  ‘Lero udutsa m’dera la Mowabu, pafupi ndi Ari,+ 19  ndipo uyandikire pafupi ndi ana a Amoni. Usawavutitse kapena kumenyana nawo, chifukwa sindidzakupatsa mbali iliyonse ya dziko la ana a Amoni kuti likhale lako. Dziko limeneli ndinalipereka kwa ana a Loti kuti likhale lawo.+ 20  Dzikoli linali kudziwika kuti ndi la Arefai.+ (Kale munali kukhala Arefai ndipo Aamoni anali kutcha Arefaiwo kuti Azamuzumi. 21  Anthu amenewa anali amphamvu kwambiri ndiponso ochuluka. Analinso ataliatali ngati Aanaki.+ Yehova anawafafaniza+ kuwachotsa pamaso pa ana a Amoni kuti ana a Amoniwo atenge dzikolo ndi kukhalamo, 22  monga mmene anachitira ndi ana a Esau amene akukhala m’Seiri.+ Iye anafafaniza Ahori+ kuwachotsa pamaso pa ana a Esau, kuti ana a Esauwo atenge dzikolo ndi kukhalamo mpaka lero. 23  Aavi+ amene anali kukhala m’midzi mpaka kukafika ku Gaza,+ anawonongedwa ndi Akafitori+ ochokera ku Kafitori,+ kuwachotsa pamaso pawo kuti Akafitoriwo akhale m’dzikolo.) 24  “‘Nyamukani, muyende ndi kudutsa chigwa cha Arinoni.+ Taonani, ndapereka m’manja mwanu Sihoni,+ Mwamori, mfumu ya Hesiboni. Yambani kulanda dziko lake, ndipo menyanani naye nkhondo. 25  Lero ndichititsa anthu a mitundu ina okhala pansi pa thambo, amene adzamva za inu, kuchita nanu mantha kwambiri ndi kuyamba kukuopani. Chifukwa cha inu, iwo adzanthunthumira ndi kumva zopweteka zofanana ndi zowawa za pobereka.’+ 26  “Kenako, ndinatumiza amithenga a mawu amtendere+ kuchokera m’chipululu cha Kademoti,+ kupita kwa Sihoni+ mfumu ya Hesiboni, kuti, 27  ‘Ndilole ndidutse m’dziko lako. Ndidzangodutsa mumsewu. Sindidzatembenukira kudzanja lamanja kapena lamanzere.+ 28  Ndidzadya chakudya chimene udzandigulitsa ndi ndalama, ndipo ndidzamwa madzi amene udzandigulitsa ndi ndalama. Ndilole ndingodutsa m’dziko lako,+ 29  monga mmene ana a Esau amene akukhala m’Seiri+ ndi Amowabu+ amene akukhala mu Ari anachitira kwa ine. Ndidzadutsa m’dziko lako mpaka kukawoloka Yorodano, kulowa m’dziko limene Yehova Mulungu wathu anatipatsa.’+ 30  Koma Sihoni mfumu ya Hesiboni sanatilole kudutsa m’dziko lake, chifukwa Yehova Mulungu wanu anamulola kuti akhale wokanika+ ndi kuti aumitse mtima wake. Anatero kuti am’pereke m’manja mwanu monga mmene zilili lero.+ 31  “Zitatero, Yehova anandiuza kuti, ‘Taona, ndikupereka Sihoni ndi dziko lake kwa iwe. Yamba kulanda dziko lake.’+ 32  Sihoni atatuluka pamodzi ndi anthu ake onse kudzamenyana nafe nkhondo ku Yahazi,+ 33  Yehova Mulungu wathu anam’pereka kwa ife,+ ndipo tinam’gonjetsa+ limodzi ndi ana ake ndi anthu ake onse. 34  Tinalandanso mizinda yake yonse pa nthawi imeneyo ndi kuwononga mzinda wina uliwonse.+ Tinapha amuna, akazi ndi ana, ndipo sitinasiye munthu aliyense wamoyo. 35  Ziweto zokha n’zimene tinatenga monga zofunkha pamodzi ndi zofunkha za m’mizinda imene tinalanda.+ 36  Kuchokera ku Aroweli,+ mzinda umene uli m’mbali mwa chigwa cha Arinoni, ndiponso kuchokera kumzinda wa m’chigwa mpaka ku Giliyadi, panalibe mzinda womwe unali wa malinga aatali kwambiri kwa ife.+ Yehova Mulungu wathu anawapereka onsewo kwa ife. 37  Koma simunayandikire dziko la ana a Amoni,+ dera lonse la m’mbali mwa chigwa cha Yaboki,+ kapena mizinda ya m’dera lamapiri, kapenanso malo alionse amene Yehova Mulungu wathu sanatilamule kuti tiwalande.

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.