Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Deuteronomo 19:1-21

19  “Yehova Mulungu wako akadzawononga mitundu+ ya m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa, iwe n’kuwalandadi dzikolo ndi kukhala m’mizinda yawo ndi m’nyumba zawo,+  udzadzipatulire mizinda itatu pakati pa dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa kuti likhale lako.+  Udzadzilambulire njira yopita kumizindayo ndipo udzagawe dziko limene Yehova Mulungu wako wakupatsa kuti likhale lako. Dzikolo udzaligawe m’zigawo zitatu. Wopha munthu azithawira kumizinda imeneyo.+  “Nkhani ya munthu wopha mnzake amene angathawire kumeneko kuti akhale ndi moyo, izikhala yotere: Akapha munthu mosadziwa ndipo sanali kudana naye,+  kapena akapita ndi mnzake kuthengo kukafuna nkhuni, ndipo wakweza dzanja lake kuti adule mtengo ndi nkhwangwa koma nkhwangwayo yaguluka mumpini wake+ n’kukantha mnzake ndi kumupha, wopha mnzakeyo azithawira ku umodzi mwa mizinda imeneyi kuti akhale ndi moyo.+  Akapanda kutero, wobwezera magazi+ angathamangitse wopha munthuyo ndi kum’peza, chifukwa mtunda ndi wautali. Pamenepo angamukanthe ndi kumupha chifukwa chakuti mtima wake ndi wodzaza ndi ukali, ngakhale kuti wopha mnzake mwangoziyo sanayenere kufa+ chifukwa sanali kudana naye.  N’chifukwa chake ndikukulamula kuti, ‘Udzipatulire mizinda itatu.’+  “Yehova Mulungu wanu akadzafutukula dera lanu malinga ndi zimene analumbirira makolo anu,+ n’kukupatsani dziko lonse limene analonjeza makolo anu kuti adzawapatsa,+  chifukwa chakuti mwasunga malamulo onsewa amene ndikukupatsani lero mwa kuwatsatira, kuti muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi kuyenda m’njira zake nthawi zonse,+ pamenepo mudzawonjezere mizinda inanso itatu pa mizinda imeneyi,+ 10  kuti musakhetse magazi a munthu wosalakwa+ pakati pa dziko lanu limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani monga cholowa, kotero kuti musakhale ndi mlandu wa magazi.+ 11  “Koma pakakhala munthu wodana+ ndi mnzake amene wabisalira ndi kuukira mnzakeyo panjira n’kumukantha ndipo wafa,+ iye n’kuthawira ku umodzi mwa mizinda imeneyi, 12  akulu a mumzinda wakwawo azitumiza anthu kukam’tenga kumeneko, ndipo azim’pereka m’manja mwa wobwezera magazi kuti afe ndithu.+ 13  Diso lako lisamumvere chisoni+ ndipo uzichotsa mlandu wa magazi a munthu wosalakwa mu Isiraeli+ kuti zinthu zikuyendere bwino. 14  “Usasunthe zizindikiro za malire a mnzako,+ makolo anu ataika kale malire a cholowa chimene udzalandira, m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa kuti ulitenge kukhala lako. 15  “Munthu akachita tchimo, mboni imodzi si yokwanira kutsimikizira kuti wachitadi cholakwacho kapena tchimo lililonse.+ Muzitsimikizira nkhaniyo mutamva umboni wapakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu.+ 16  Munthu akakonzera mnzake chiwembu mwa kupereka umboni wonama wakuti waphwanya lamulo,+ 17  anthu awiri otsutsanawo aziima pamaso pa Yehova, pamaso pa ansembe ndi oweruza amene aziweruza masiku amenewo.+ 18  Pamenepo oweruza azifufuza nkhaniyo mosamala.+ Mboniyo ikapezeka kuti ndi yonama ndipo yaneneza m’bale wake mlandu wonama, 19  muziichitira zimene inafuna kuti zichitikire m’bale wakezo,+ ndipo muzichotsa woipayo pakati panu.+ 20  Chotero ena onse adzamva ndi kuchita mantha, ndipo sadzachitanso choipa chilichonse ngati chimenechi pakati panu.+ 21  Diso lako lisamumvere chisoni.+ Pazikhala moyo kulipira moyo, diso kulipira diso, dzino kulipira dzino, dzanja kulipira dzanja, phazi kulipira phazi.+

Mawu a M'munsi