Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Deuteronomo 15:1-23

15  “Kumapeto kwa zaka 7 zilizonse uzilengeza kuti anthu amene anakongola zinthu zako amasuka ku ngongoleyo.  Kumasula anthu angongoleko kuzichitika motere:+ munthu aliyense asafunse ngongole imene anabwereketsa mnzake. Asakakamize mnzake kapena m’bale wake kupereka ngongoleyo,+ chifukwa chilengezo choti anthu angongole amasuke chiyenera kuperekedwa pamaso pa Yehova.+  Mlendo+ ungam’kakamize kubweza ngongole, koma ngati m’bale wako wakongola chinthu chako chilichonse usam’kakamize kuchibweza.  Pakati panu pasapezeke munthu wosauka, chifukwa Yehova adzakudalitsa ndithu+ m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa kuti likhale cholowa chako.+  Adzakudalitsa ngati udzamveradi mawu a Yehova Mulungu wako ndi kutsatiradi malamulo onsewa amene ndikukupatsa lero.+  Yehova Mulungu wako adzakudalitsa ndithu monga mmene anakulonjezera ndipo mitundu yambiri idzakongola+ zinthu zako mwa kukupatsa chikole, pamene iwe sudzakongola kanthu. Udzalamulira mitundu yambiri koma mitundu sidzakulamulira.+  “Wina mwa abale ako akasauka pakati panu, mu umodzi mwa mizinda yanu, m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa, usamuumire mtima kapena kumuumitsira dzanja lako.+  Uzim’kongoza m’bale wako mowolowa manja,+ mulimonse mmene iye wafunira atakupatsa chikole, ndipo uzim’kongoza zimene akusowa.  Samala kuti usalankhule mawu achabe mumtima mwako+ kuti, ‘Chaka cha 7, chaka choti anthu angongole amasuke chayandikira,’+ kuti usaolowere manja m’bale wako wosaukayo,+ osam’patsa kalikonse. Pamenepo iye adzafuulira Yehova chifukwa cha zimene iweyo wam’chitira+ ndipo udzapezeka kuti wachimwa.+ 10  Mulimonse mmene zingakhalire uzim’patsa zimene akufunazo,+ ndipo mtima wako usakhale woumira pomupatsa zinthu zimenezo, chifukwa ukakhala wowolowa manja, Yehova Mulungu wako adzakudalitsa pa chilichonse chimene ukuchita ndi pa ntchito zako zonse.+ 11  Pakuti sipadzalephera kukhala wosauka m’dziko lako.+ N’chifukwa chake ndikukulamula kuti, ‘Uzikhala wowolowa manja kwa m’bale wako wovutika ndi wosauka m’dziko lanu.’+ 12  “Ngati anakugulitsa m’bale wako, Mheberi wamwamuna kapena wamkazi,+ ndipo wakutumikira zaka 6, m’chaka cha 7 uzim’masula ndi kumulola kuchoka.+ 13  Ndipo ukam’masula ndi kumulola kuchoka, usamulole kuchoka chimanjamanja.+ 14  Uzim’patsako ndithu zina mwa nkhosa zako, mbewu zochokera pamalo ako opunthira, mafuta ochokera pamalo oyengera ndi vinyo wochokera moponderamo mphesa. Uzim’patsa malinga ndi mmene Yehova Mulungu wako wakudalitsira.+ 15  Uzikumbukira kuti unali kapolo m’dziko la Iguputo ndipo Yehova Mulungu wako anakuwombola.+ N’chifukwa chake lero ndikukulamula zinthu zimenezi. 16  “Koma kapoloyo akakuuza kuti, ‘Ine sindikusiyani!’ chifukwa chakuti amakukonda komanso amakonda banja lako, popeza unali kukhala naye bwino,+ 17  uzitenga choboolera ndi kuboola khutu lake ali pakhomo, mpaka chobooleracho chigunde chitseko ndipo azikhala kapolo wako moyo wake wonse.+ Uzichitanso zimenezi ndi kapolo wako wamkazi. 18  Zisakhale zovuta kwa iwe kum’masula kuti achoke,+ chifukwa wakutumikira zaka 6, moti malipiro ake akanafanana ndi malipiro a anthu awiri aganyu,+ ndipo Yehova Mulungu wako wakudalitsa pa chilichonse chimene wachita.+ 19  “Mwana aliyense wamphongo woyamba kubadwa wa ng’ombe kapena wa nkhosa uzim’patulira Yehova Mulungu wako.+ Usagwiritse ntchito mwana woyamba kubadwa wa ng’ombe, kapena kumeta ubweya wa mwana woyamba kubadwa wa nkhosa.+ 20  Chaka ndi chaka iweyo ndi banja lako muzidya mwana woyamba kubadwa wa ng’ombe kapena wa nkhosa pamaso pa Yehova Mulungu wako, pamalo amene Yehova adzasankhe.+ 21  Akakhala ndi vuto, monga kulumala kapena khungu, kapena chilema chilichonse chachikulu, usamam’pereke nsembe kwa Yehova Mulungu wako.+ 22  Uzimudyera mumzinda wanu ngati mmene umadyera insa ndi mbawala yamphongo.+ Nayenso munthu wodetsedwa komanso munthu woyera azidya.+ 23  Koma magazi ake okha usadye.+ Uziwathira pansi ngati madzi.+

Mawu a M'munsi