Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Deuteronomo 13:1-18

13  “Mneneri+ kapena wolota maloto+ akauka pakati panu n’kukupatsani chizindikiro kapena chodabwitsa cholosera zam’tsogolo,+  ndipo chizindikiro kapena chodabwitsa chimenecho chachitikadi,+ chimene anachita ponena kuti, ‘Tiyeni titsatire milungu ina imene simunaidziwe, ndipo tiitumikire,’  musamvere mawu a mneneriyo kapena wolotayo,+ chifukwa Yehova Mulungu wanu akukuyesani+ kuti adziwe ngati mukukonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.+  Muzitsatira Yehova Mulungu wanu, muzimuopa, muzisunga malamulo ake, muzimvera mawu ake, muzim’tumikira ndi kum’mamatira.+  Ndipo mneneri+ kapena wolota malotoyo muzimupha,+ chifukwa walankhula mopandukira Yehova Mulungu wanu amene anakutulutsani m’dziko la Iguputo ndi kukuwombolani m’nyumba yaukapolo. Munthu ameneyo walankhula zimenezo kuti akupatutseni panjira imene Yehova Mulungu wanu anakulamulani kuyendamo.+ Choncho muzichotsa woipayo pakati panu.+  “M’bale wako, amene ndi mwana wamwamuna wa mayi ako, kapena mwana wako wamwamuna, mwana wako wamkazi, mkazi wako wokondedwa kapena bwenzi lako lapamtima,+ akayesa kukupatutsa mwamseri pokuuza kuti, ‘Tiye tikatumikire milungu ina,’+ milungu imene iwe kapena makolo ako sanaidziwe,  milungu ina mwa milungu ya anthu okuzungulirani, okhala pafupi nanu kapena okhala kutali, kuchokera kumalekezero ena a dziko kukafika kumalekezero ena,  usavomereze zofuna zake kapena kumumvera.+ Diso lako lisamumvere chifundo ndipo usamumvere chisoni+ kapena kum’bisa kuti um’teteze.  Koma umuphe ndithu.+ Dzanja lako lizikhala loyamba kum’ponya miyala kuti afe, ndipo anthu ena onse azibwera pambuyo.+ 10  Uzim’ponya miyala kuti afe,+ chifukwa anali kufuna kukupatutsa ndi kukuchotsa kwa Yehova Mulungu wako, amene anakutulutsa m’dziko la Iguputo, m’nyumba yaukapolo.+ 11  Pamenepo Aisiraeli onse adzamva ndi kuchita mantha, ndipo sadzachita chinthu choipa chilichonse chofanana ndi chimenechi pakati panu.+ 12  “Mu umodzi mwa mizinda yanu, imene Yehova Mulungu wanu wakupatsani kuti mukhalemo, mukadzamva kuti, 13  ‘Pakati panu papezeka anthu opanda pake+ amene akufuna kupatutsa anthu mumzinda wawo,+ ponena kuti: “Tiyeni tikatumikire milungu ina,” milungu imene inu simunaidziwe,’ 14  muzifunafuna, kufufuza ndi kufunsitsa za nkhani imeneyo.+ Mukapeza kuti ndi zoonadi, choipa chimenechi chachitikadi pakati panu, 15  muzipha ndithu anthu a mumzindawo ndi lupanga.+ Muziwononga+ ndi lupanga mzindawo ndi chilichonse chimene chili mmenemo, kuphatikizapo ziweto zake. 16  Zofunkha zake zonse muzizisonkhanitsa pakati pa bwalo la mzindawo. Pamenepo muzitentha mzindawo+ ndi zofunkha zake zonse monga nsembe yathunthu yoperekedwa kwa Yehova Mulungu wanu. Ndipo mzindawo uzikhala bwinja mpaka kalekale.+ Usadzamangidwenso. 17  Ndipo kanthu kalikonse koyenera kuwonongedwa* kasamamatire kudzanja lanu,+ kuti mkwiyo woyaka moto wa Yehova usiye kukuyakirani+ ndipo akuchitireni chifundo ndi kukumverani chisoni,+ kutinso akuchulukitseni, monga mmene analumbirira makolo anu.+ 18  Motero muzimvera mawu a Yehova Mulungu wanu, mwa kusunga malamulo ake+ onse amene ndikukupatsani lero, kuti muzichita zinthu zoyenera pamaso pa Yehova Mulungu wanu.+

Mawu a M'munsi

Mawu akuti “kanthu kalikonse koyenera kuwonongedwa” angalembedwenso kuti “kanthu kalikonse kotembereredwa.”