Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Danieli 9:1-27

9  M’chaka choyamba cha Dariyo mwana wa Ahasiwero,+ wa mtundu wa Amedi,+ amene anaikidwa kukhala mfumu ya ufumu wa Akasidi,+  m’chaka choyamba cha ulamuliro wake, ineyo Danieli ndinazindikira chiwerengero cha zaka za kuwonongedwa kwa Yerusalemu+ kuti zidzakhala zaka 70.+ Ndinazindikira zimenezi mwa kuwerenga mawu amene Yehova anauza mneneri Yeremiya olembedwa m’mabuku.  Ndinayang’ana+ kwa Yehova Mulungu woona kuti ndimufunefune mwa kupemphera,+ kumuchonderera, kusala kudya, kuvala ziguduli* ndi kudzithira phulusa.  Pamenepo ndinayamba kupemphera kwa Yehova Mulungu wanga ndi kuvomereza machimo athu kuti: “Inu Yehova Mulungu woona, Mulungu wamkulu ndi wochititsa mantha. Anthu amene amakukondani ndi kusunga malamulo anu mumawasungira pangano ndi kuwasonyeza kukoma mtima kosatha.  Ife tachimwa, talakwa, tachita zinthu zoipa ndipo takupandukirani. Tapatuka ndiponso tasiya malamulo anu ndi zigamulo zanu.+  Sitinamvere atumiki anu aneneri, amene analankhula m’dzina lanu kwa mafumu athu, akalonga athu, makolo athu, ndi anthu onse a m’dziko lathu.  Inu Yehova ndinu wolungama, koma ife manyazi aphimba nkhope zathu lero.+ Manyazi aphimba nkhope za amuna a mu Yuda, anthu a ku Yerusalemu ndi anthu onse a ku Isiraeli, amene ali pafupi ndiponso amene ali kumayiko onse akutali kumene munawabalalitsira chifukwa cha zinthu zosakhulupirika zimene anakuchitirani.  “Inu Yehova, manyazi aphimba nkhope zathu, za mafumu athu, akalonga athu ndi makolo athu chifukwa takuchimwirani.+  Inu Yehova Mulungu wathu, ndinu wachifundo ndi wokhululuka, koma ife takupandukirani. 10  Sitinamvere mawu anu, inu Yehova Mulungu wathu, mwa kuyenda motsatira malamulo anu amene munatiikira kudzera mwa atumiki anu, aneneri. 11  Anthu onse a mu Isiraeli aphwanya malamulo anu ndipo apatuka mwa kusamvera mawu anu.+ Choncho inu mwatitsanulira temberero ndi malumbiro amene analembedwa m’chilamulo cha Mose, mtumiki wa Mulungu woona, pakuti takuchimwirani. 12  Inu munachitadi zimene munachenjeza kuti mudzatichitira,+ ifeyo ndi atsogoleri athu.+ Munatigwetsera tsoka lalikulu ndipo tsoka limene lagwera Yerusalemu silinachitikeponso padziko lonse lapansi.+ 13  Masoka onse amene analembedwa m’chilamulo cha Mose atigwera,+ ndipo ife sitinakhazike pansi mtima wanu, inu Yehova Mulungu wathu, mwa kusiya zolakwa zathu+ ndi kusonyeza kuti tikumvetsa kuti ndinu wokhulupirika.+ 14  “Inu Yehova, munakhala tcheru kuti mutigwetsere tsoka ndipo pamapeto pake munatigwetseradi tsokalo,+ pakuti inu Yehova Mulungu wathu ndinu wolungama pa ntchito zanu zonse zimene mwachita, koma ife sitinamvere mawu anu. 15  “Tsopano inu Yehova Mulungu wathu, amene munatulutsa anthu anu m’dziko la Iguputo ndi dzanja lamphamvu, amenenso munadzipangira dzina kufikira lero, ife tachimwa,+ tachita zinthu zoipa. 16  Inu Yehova, nthawi zonse mumachita zinthu zolungama.+ Chonde, chotsani mkwiyo wanu waukulu pa Yerusalemu, phiri lanu loyera.+ Pakuti chifukwa cha machimo athu ndi zolakwa za makolo athu, Yerusalemu ndi anthu anu takhala chinthu chotonzedwa ndi anthu onse otizungulira. 17  Tsopano inu Mulungu wathu, imvani pemphero la mtumiki wanu ndi kuchonderera kwake. Malo anu opatulika amene awonongedwa+ akomereni mtima, inu Yehova, chifukwa cha dzina lanu. 18  Mulungu wanga, tcherani khutu lanu kuti mumve. Tsegulani maso anu kuti muone kuwonongeka kwathu ndi kwa mzinda wotchedwa ndi dzina lanu.+ Ifeyo tikukuchondererani, osati chifukwa cha zochita zathu zolungama,+ koma chifukwa cha chifundo chanu chachikulu.+ 19  Imvani, inu Yehova. Tikhululukireni, inu Yehova. Timvereni ndipo muchitepo kanthu, inu Yehova. Inu Mulungu wanga, chifukwa cha dzina lanu musazengereze,+ pakuti mzinda wanu ndi anthu anu amatchedwa ndi dzina lanu.”+ 20  Pamene ndinali kulankhula, kupemphera ndi kuvomereza machimo anga+ ndi machimo a anthu a mtundu wanga Aisiraeli,+ ndiponso pamene ndinali kupempha pamaso pa Yehova Mulungu wanga kuti andikomere mtima komanso kuti akomere mtima phiri loyera la Mulungu wanga,+ 21  inde, pamene ndinali kulankhula zimenezi m’pemphero, munthu uja Gabirieli,+ amene ndinamuona m’masomphenya nditatopa kwambiri poyamba paja,+ ndinamuona akubwera kwa ine pa nthawi yopereka nsembe yamadzulo, yoperekedwa ngati mphatso. 22  Iye anandithandiza kuti ndimvetse pondiuza kuti: “Iwe Danieli, tsopano ndabwera kuti ndikuthandize kumvetsa zinthu zonsezi.+ 23  Pamene unali kuyamba kupemphera ndinalandira uthenga, choncho ndabwera kudzakufotokozera za uthengawo chifukwa iwe ndiwe munthu wokondedwa kwambiri.+ Tsopano khala tcheru,+ ndipo umvetsetse zinthu zimene ukuona. 24  “Pali milungu 70 imene yaikidwa yokhudza anthu a mtundu wako ndi mzinda wanu woyera, ndi cholinga choti athetse kuphwanya malamulo,+ athetse machimo,+ aphimbe cholakwa,+ abweretse chilungamo kuti chikhalepo mpaka kalekale,+ adinde chidindo+ pa masomphenya ndi maulosi, ndiponso kuti adzoze Malo Opatulikitsa.+ 25  Choncho iwe uyenera kudziwa ndi kuzindikira kuti kuchokera pamene mawu adzamveka onena kuti Yerusalemu akonzedwe ndi kumangidwanso, kufika pamene Mesiya Mtsogoleri adzaonekere, padzadutsa milungu 7, komanso milungu 62.+ Yerusalemu adzakonzedwa ndi kumangidwanso, ndipo adzakhala ndi bwalo ndi ngalande yachitetezo. Zimenezi zidzachitika mu nthawi zovuta. 26  “Pambuyo pa milungu 62 imeneyi, Mesiya adzaphedwa+ ndipo sadzasiya kalikonse.+ “Gulu lankhondo la mtsogoleri amene akubwera lidzawononga+ mzindawo ndi malo oyera.+ Malo oyera amenewo adzafafanizidwa ndi madzi osefukira, ndipo padzakhala nkhondo mpaka kumapeto. Mulungu wagamula kuti padzakhale chiwonongeko.+ 27  “Mesiyayo* adzasungira anthu ambiri pangano kwa mlungu umodzi,+ kenako pakatikati pa mlunguwo adzathetsa nsembe zanyama ndi nsembe zina zoperekedwa ngati mphatso.+ “Wowonongayo+ adzabwera pamapiko a zinthu zonyansa, ndipo zimene Mulungu wagamula zidzakhuthulidwanso pa chowonongedwacho+ kufikira chitafafanizidwa.”

Mawu a M'munsi

Ena amati “masaka.”
Mawu ake enieni, “Iye.”