Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Chivumbulutso 7:1-17

7  Zimenezi zitatha, ndinaona angelo+ anayi ataimirira m’makona anayi a dziko lapansi. Iwo anali atagwira mwamphamvu mphepo zinayi+ za dziko lapansi, kuti mphepo iliyonse isawombe padziko lapansi, panyanja, kapena pamtengo uliwonse.+  Ndinaonanso mngelo wina akukwera kuchokera kotulukira dzuwa,+ ali ndi chidindo cha Mulungu+ wamoyo. Iye anafuula mokweza mawu, kwa angelo anayiwo, amene anapatsidwa mphamvu zowononga dziko lapansi ndi nyanja.  Anafuula kuti: “Musawononge dziko lapansi, kapena nyanja, kapena mitengo, kufikira titadinda chidindo+ pamphumi+ za akapolo a Mulungu wathu.”  Ndiyeno ndinamva chiwerengero cha amene anadindidwa chidindo. Anthu okwana 144,000,+ ochokera m’fuko lililonse+ la ana a Isiraeli,+ anadindidwa chidindo:  Mu fuko la Yuda,+ anadindamo anthu 12,000. Mu fuko la Rubeni,+ 12,000. Mu fuko la Gadi,+ 12,000.  Mu fuko la Aseri,+ 12,000. Mu fuko la Nafitali,+ 12,000. Mu fuko la Manase,+ 12,000.  Mu fuko la Simiyoni,+ 12,000. Mu fuko la Levi,+ 12,000. Mu fuko la Isakara,+ 12,000.  Mu fuko la Zebuloni,+ 12,000. Mu fuko la Yosefe,+ 12,000. Ndipo mu fuko la Benjamini,+ anadindamo anthu 12,000.+  Zimenezi zitatha, nditayang’ana ndinaona khamu lalikulu la anthu,+ limene palibe munthu aliyense amene anatha kuliwerenga, lochokera m’dziko lililonse,+ fuko lililonse, mtundu uliwonse,+ ndi chinenero chilichonse.+ Iwo anali ataimirira pamaso pa mpando wachifumu+ ndi pamaso pa Mwanawankhosa, atavala mikanjo yoyera+ ndiponso atanyamula nthambi za kanjedza+ m’manja mwawo. 10  Iwo anapitirizabe kufuula ndi mawu okweza, kuti: “Chipulumutso chathu chachokera kwa Mulungu wathu,+ amene wakhala pampando wachifumu,+ ndi kwa Mwanawankhosa.”+ 11  Pamenepo angelo+ onse anaimirira mozungulira mpando wachifumu, limodzi ndi akulu,+ ndi zamoyo zinayi zija.+ Ndipo onse anagwada ndi kuwerama mpaka nkhope zawo pansi, pamaso pa mpando wachifumuwo ndi kulambira Mulungu.+ 12  Iwo anali kunena kuti: “Ame! Mulungu wathu wanzeru, wamphamvu+ ndi wa nyonga, atamandidwe, apatsidwe ulemerero ndi ulemu, ndipo ayamikiridwe kwamuyaya. Ame.”+ 13  Ndiyeno mmodzi wa akulu+ aja anandifunsa kuti: “Kodi amene avala mikanjo yoyerawa+ ndi ndani, ndipo achokera kuti?” 14  Nthawi yomweyo, ndinamuyankha kuti: “Mbuyanga, mukudziwa ndinu.” Ndipo iye anati: “Amenewa ndi amene atuluka m’chisautso chachikulu,+ ndipo achapa mikanjo yawo ndi kuiyeretsa+ m’magazi+ a Mwanawankhosa. 15  N’chifukwa chake ali pamaso+ pa mpando wachifumu wa Mulungu. Iwo akumuchitira utumiki wopatulika+ usana ndi usiku m’kachisi wake, ndipo wokhala pampando wachifumuyo+ adzatambasulira hema+ wake pamwamba pawo kuti awateteze. 16  Iwo sadzamvanso njala kapena ludzu. Dzuwa kapena kutentha kulikonse sikudzawawotcha,+ 17  chifukwa Mwanawankhosa,+ amene ali pambali pa mpando wachifumu, adzawaweta+ ndi kuwatsogolera ku akasupe a madzi+ a moyo. Ndipo Mulungu adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo.”+

Mawu a M'munsi