Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Chivumbulutso 6:1-17

6  Ndinaona Mwanawankhosa+ atamatula chidindo chimodzi mwa zidindo 7 zija,+ ndipo ndinamva chamoyo chimodzi mwa zamoyo zinayi zija+ chikulankhula ndi mawu ngati kugunda kwa bingu kuti: “Bwera!”+  Nditayang’ana, ndinaona hatchi* yoyera.+ Wokwerapo+ wake ananyamula uta.+ Iye anapatsidwa chisoti chachifumu,+ ndi kupita kukagonjetsa adani ake+ ndipo anapambana pa nkhondo yolimbana nawo.+  Atamatula chidindo chachiwiri, ndinamva chamoyo chachiwiri+ chikunena kuti: “Bwera!”  Pamenepo, hatchi ina inatulukira. Imeneyi inali yofiira ngati moto. Wokwerapo wake analoledwa kuchotsa mtendere padziko lapansi, kuti anthu aphane. Iye anapatsidwanso lupanga lalikulu.+  Atamatula+ chidindo chachitatu, ndinamva chamoyo chachitatu+ chikunena kuti: “Bwera!” Ndipo nditayang’ana, ndinaona hatchi yakuda. Wokwerapo wake anali ndi sikelo+ m’dzanja lake.  Kenako ndinamva mawu ngati ochokera pakati+ pa zamoyo zinayi zija.+ Mawuwo anali akuti: “Kilogalamu imodzi ya tirigu, mtengo wake ukhala dinari imodzi,+ ndipo makilogalamu atatu a balere, mtengo wake ukhala dinari imodzi. Koma musawononge mafuta a maolivi ndi vinyo.”+  Atamatula chidindo chachinayi, ndinamva mawu a chamoyo chachinayi+ chikunena kuti: “Bwera!”  Nditayang’ana, ndinaona hatchi yotuwa. Wokwerapo wake dzina lake anali Imfa. Ndipo Manda+ anali kumutsatira pafupi kwambiri. Iwo anapatsidwa ulamuliro pa gawo limodzi la magawo anayi a dziko lapansi, kuti aphe anthu ndi lupanga lalitali,+ njala,+ mliri wakupha, ndi zilombo+ za padziko lapansi.  Atamatula chidindo chachisanu, ndinaona pansi pa guwa lansembe+ pali miyoyo+ ya amene anaphedwa+ chifukwa cha mawu a Mulungu, ndiponso chifukwa cha ntchito yochitira umboni+ imene anali nayo. 10  Iwo anafuula ndi mawu okweza akuti: “Mudzalekerera kufikira liti, Inu Ambuye Wamkulu Koposa,+ woyera ndi woona,+ osaweruza+ ndi kubwezera okhala padziko lapansi chifukwa cha magazi+ athu?” 11  Aliyense wa iwo anapatsidwa mkanjo woyera,+ ndipo anauzidwa kuti apumulebe kanthawi pang’ono, kufikira chitakwanira chiwerengero cha akapolo anzawo, ndi abale awo amene anali pafupi kuphedwa+ monga mmene iwonso anaphedwera. 12  Atamatula chidindo cha 6, ndinaona kuti kunachitika chivomezi chachikulu. Dzuwa linada ngati chiguduli*+ choluka ndi ubweya wa mbuzi yakuda, ndipo mwezi wonse unafiira ngati magazi.+ 13  Nyenyezi zakumwamba zinagwera kudziko lapansi, ngati mmene mkuyu wogwedezeka ndi mphepo yamphamvu umagwetsera nkhuyu zake zosapsa. 14  Ndipo kumwamba kunakanganuka ngati mpukutu umene akuupinda,+ ndipo phiri lililonse ndi chilumba chilichonse zinachotsedwa m’malo awo.+ 15  Mafumu a dziko lapansi, nduna, akuluakulu a asilikali, olemera, amphamvu, kapolo aliyense ndi mfulu aliyense, anabisala m’mapanga ndi m’matanthwe+ a m’mapiri. 16  Iwo anali kuuza mapiri ndi matanthwe mosalekeza kuti: “Tigwereni,+ tibiseni kuti tisaonekere kwa Iye amene wakhala pampando wachifumu,+ ndiponso kuti tibisike ku mkwiyo wa Mwanawankhosa,+ 17  chifukwa tsiku lalikulu+ la mkwiyo wawo+ lafika, ndipo ndani angaimirire pamaso pawo?”+

Mawu a M'munsi

Ena amati “hosi” kapena “kavalo.”
Ena amati “saka.”