Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Chivumbulutso 3:1-22

3  “Kwa mngelo+ wa mpingo wa ku Sade, lemba kuti: Izi ndi zimene akunena iye amene ali ndi mizimu 7+ ya Mulungu, ndi nyenyezi 7.+ ‘Ndikudziwa ntchito zako, kuti uli ndi dzina lakuti uli moyo, pamene ndiwe wakufa.+  Khala maso,+ ndipo limbikitsa+ otsala amene atsala pang’ono kufa, chifukwa ndapeza kuti ntchito zako sizinachitidwe mokwanira pamaso pa Mulungu wanga.+  Choncho, pitiriza kukumbukira zimene unalandira+ ndi zimene unamva. Pitiriza kuzitsatira,+ ndipo ulape.+ Ndithudi, ukapanda kudzuka,+ ndidzabwera ngati mbala,+ ndipo sudzadziwa ngakhale pang’ono ola limene ndidzafike kwa iwe.+  “‘Ngakhale zili choncho, uli ndi mayina+ angapo mu Sade a anthu amene sanaipitse+ malaya awo akunja. Amenewa adzayenda ndi ine atavala malaya oyera,+ chifukwa ndi oyenerera.+  Choncho amene wapambana pa nkhondo+ adzavekedwa malaya akunja oyera.+ Ndipo sindidzafafaniza dzina lake m’buku la moyo,+ koma ndidzavomereza dzina lake pamaso pa Atate wanga,+ ndi pamaso pa angelo ake.+  Amene ali ndi makutu amve zimene mzimu ukunena+ ku mipingo.’  “Kwa mngelo+ wa mpingo wa ku Filadefiya, lemba kuti: Izi ndi zimene akunena woyerayo,+ amene ali woona,+ yemwe ali ndi kiyi wa Davide.+ Iye amene amati akatsegula palibe wina amene angatseke, ndipo akatseka palibe wina amene angatsegule.  ‘Ndikudziwa ntchito zako.+ Taona! Ndakutsegulira khomo+ pamaso pako, limene wina sangalitseke. Ndikudziwa kuti uli ndi mphamvu zochepa, ndiponso kuti unasunga mawu anga. Ndikudziwanso kuti wakhala wokhulupirika ku dzina langa.+  Taona! Anthu ochokera m’sunagoge wa Satana, amene amanama+ kuti ndi Ayuda+ pamene si Ayuda, ndidzawachititsa kuti abwere kudzagwada ndi kuwerama+ pamapazi ako. Ndipo ndidzawachititsa kudziwa kuti ndimakukonda. 10  Popeza unasunga mawu onena za kupirira kwanga,+ inenso ndidzakusunga+ pa ola la kuyesedwa, limene likubwera padziko lonse lapansi kumene kuli anthu. Ndidzakusunga pa ola limene likubwera kudzayesa okhala padziko lapansi.+ 11  Ndikubwera mofulumira.+ Gwirabe mwamphamvu chimene uli nacho,+ kuti wina asakulande mphoto* yako.+ 12  “‘Wopambana pa nkhondo, ndidzamuika kukhala mzati+ m’kachisi+ wa Mulungu wanga,+ ndipo sadzachokamonso. Ndidzamulemba dzina la Mulungu wanga, ndiponso dzina la mzinda wa Mulungu wanga, Yerusalemu watsopano,+ wotsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu wanga. Ndidzamulembanso dzina langa latsopano.+ 13  Amene ali ndi makutu amve zimene mzimu+ ukunena ku mipingo.’ 14  “Kwa mngelo wa mpingo wa ku Laodikaya,+ lemba kuti: Izi ndi zimene akunena Ame,+ mboni+ yokhulupirika+ ndi yoona,+ woyamba wa chilengedwe cha Mulungu.+ 15  ‘Ndikudziwa ntchito zako, kuti si iwe wozizira kapena wotentha. Ndikanakonda ukanakhala wozizira kapena wotentha. 16  Choncho, chifukwa choti ndiwe wofunda, osati wotentha+ kapena wozizira,+ ndikulavula m’kamwa mwanga. 17  Iwe ukunena kuti: “Ndine wolemera,+ ndapeza chuma chambiri ndipo sindikusowa kanthu,” koma sukudziwa kuti ndiwe wovutika, womvetsa chisoni, wosauka, wakhungu,+ ndi wamaliseche. 18  Chotero, ndikukulangiza kuti ugule kwa ine golide+ woyengedwa ndi moto, kuti ukhale wolemera. Ugulenso malaya akunja oyera uvale, kuti maliseche ako asaonekere+ chifukwa ungachite manyazi. Ndiponso ugule mankhwala opaka m’maso+ ako kuti uone. 19  “‘Onse amene ndimawakonda, ndimawadzudzula ndi kuwalanga.+ Choncho, khala wodzipereka ndipo ulape.+ 20  Taona! Ndaima pakhomo,+ ndipo ndikugogoda. Wina akamva mawu anga ndi kutsegula chitseko,+ ndidzalowa m’nyumba mwake ndipo iye ndi ine tidzadyera limodzi chakudya chamadzulo. 21  Wopambana pa nkhondo+ ndidzamulola kukhala nane pampando wanga wachifumu,+ monga mmene ine ndinakhalira+ ndi Atate wanga pampando wawo wachifumu+ nditapambana pa nkhondo. 22  Amene ali ndi makutu amve zimene mzimu+ ukunena ku mipingo.’”+

Mawu a M'munsi

 Mawu ake enieni, “chisoti chachitsulo chooneka ngati nkhata.”