Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Chivumbulutso 21:1-27

21  Tsopano ndinaona kumwamba+ kwatsopano ndi dziko lapansi+ latsopano, pakuti kumwamba+ kwakale ndi dziko lapansi lakale+ zinali zitachoka, ndipo kulibenso nyanja.+  Ndinaonanso mzinda woyera,+ Yerusalemu Watsopano, ukutsika kuchokera kumwamba+ kwa Mulungu, utakonzedwa ngati mkwatibwi+ wokongoletsedwera mwamuna wake.+  Kenako ndinamva mawu ofuula kuchokera kumpando wachifumu, akuti: “Taonani! Chihema+ cha Mulungu chili pakati pa anthu. Iye adzakhala pamodzi nawo,+ ndipo iwo adzakhala anthu ake.+ Zoonadi, Mulunguyo adzakhala nawo.+  Iye adzapukuta misozi+ yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso.+ Sipadzakhalanso kulira,+ kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”+  Ndipo wokhala pampando wachifumu anati: “Taonani! Zinthu zonse zimene ndikupanga n’zatsopano.”+ Ananenanso kuti: “Lemba, pakuti mawu awa ndi odalirika ndi oona.”  Anandiuzanso kuti: “Zakwaniritsidwa! Ine ndine Alefa ndi Omega, chiyambi ndi mapeto.+ Aliyense womva ludzu, ndidzamupatsa madzi a m’kasupe wa moyo kwaulere.+  Aliyense wopambana pa nkhondo adzalandira zimenezi monga cholowa. Ineyo ndidzakhala Mulungu wake,+ ndipo iye adzakhala mwana wanga.  Koma amantha, opanda chikhulupiriro,+ odetsedwa amenenso amachita zinthu zonyansa,+ opha anthu,+ adama,+ ochita zamizimu, opembedza mafano,+ ndi onse abodza,+ gawo lawo lidzakhala m’nyanja yoyaka moto+ ndi sulufule.+ Nyanja imeneyi ikuimira imfa yachiwiri.”+  Ndipo kunabwera mmodzi wa angelo 7 aja, amene anali ndi mbale 7 zodzaza ndi miliri 7 yotsiriza. Iye anandiuza kuti: “Bwera kuno ndikuonetse mkwatibwi, mkazi wa Mwanawankhosa.”+ 10  Choncho, mu mphamvu ya mzimu, ananditengera kuphiri lalikulu ndi lalitali,+ ndipo anandionetsa mzinda woyera,+ Yerusalemu, ukutsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu,+ 11  uli ndi ulemerero wa Mulungu.+ Unali wonyezimira ngati mwala wamtengo wapatali kwambiri, ngati mwala wa yasipi wowala mbee! ngati galasi. 12  Mzindawo unali ndi mpanda waukulu ndi wautali,+ ndipo unali ndi zipata 12. Pazipatazo panali angelo 12, ndipo panalembedwa mayina a mafuko 12 a ana a Isiraeli. 13  Kum’mawa kwa mzindawo kunali zipata zitatu, kumpoto zipata zitatu, kum’mwera zipata zitatu, ndipo kumadzulo kwake zipata zitatu.+ 14  Mpanda wa mzindawo unalinso ndi miyala yomangira maziko+ yokwana 12, ndipo pamiyalayo panali mayina 12 a atumwi 12+ a Mwanawankhosa. 15  Tsopano amene anali kundilankhula uja ananyamula bango+ lagolide loyezera, kuti ayeze mzindawo, zipata zake, ndi mpanda wake.+ 16  Mzindawo unali ndi mbali zinayi zofanana kutalika kwake. M’litali mwake n’chimodzimodzi ndi m’lifupi mwake. Mngeloyo anayeza mzindawo+ ndi bangolo, ndipo anapeza kuti unali masitadiya 12,000* kuuzungulira. M’litali mwake, m’lifupi mwake, ndi msinkhu wake, n’zofanana. 17  Anayezanso mpanda wake, ndipo unali wautali mikono 144,* malinga ndi muyezo wa munthu, umene ulinso wofanana ndi muyezo wa mngelo. 18  Mpandawo unali womangidwa ndi mwala wa yasipi,+ ndipo mzindawo unali womangidwa ndi golide woyenga bwino woonekera ngati galasi. 19  Maziko+ a mpanda wa mzindawo anawakongoletsa ndi miyala yamtengo wapatali ya mitundu yonse:+ maziko oyamba anali amwala wa yasipi, achiwiri wa safiro, achitatu wa kalikedo, achinayi wa emarodi, 20  achisanu wa sadonu, a 6 wa sadiyo, a 7 wa kulusolito, a 8 wa belulo, a 9 wa topazi, a 10 wa kulusopurazo, a 11 wa huwakinto, ndipo a 12, wa ametusito.* 21  Komanso zitseko za pazipata 12 zija zinali ngale 12. Chitseko chilichonse chinali ngale imodzi. Ndipo msewu waukulu wa mumzindawo unali wopangidwa ndi golide woyenga bwino woonekera ngati galasi. 22  Sindinaone kachisi mumzindawo,+ pakuti Yehova+ Mulungu Wamphamvuyonse ndiye anali kachisi+ wake, komanso Mwanawankhosa ndiye kachisi wake.+ 23  Mzindawo sunafunikirenso kuwala kwa dzuwa kapena kwa mwezi, pakuti ulemerero wa Mulungu unauwalitsa,+ ndipo nyale yake inali Mwanawankhosa.+ 24  Mitundu ya anthu idzayenda mwa kuwala kwake,+ ndipo mafumu a dziko lapansi adzabweretsa ulemerero wawo mumzindawo.+ 25  Zipata zake sizidzatsekedwa n’komwe masana,+ ndipo usiku sudzakhalako.+ 26  Iwo adzabweretsa ulemerero ndi ulemu wa mitundu ya anthu mumzindawo.+ 27  Koma chilichonse chosapatulika, ndi aliyense wochita zonyansa+ ndiponso wabodza,+ sadzalowa mumzindawo.+ Amene adzalowemo ndi okhawo olembedwa mumpukutu wa moyo, umene ndi wa Mwanawankhosa.+

Mawu a M'munsi

Makilomita pafupifupi 2,200. Onani mawu a m’munsi pa Chv 14:20.
Mamita pafupifupi 64.
Yonseyi ndi miyala yamtengo wapatali yamitundu yosiyanasiyana, ndipo ina ndi yokhala ndi mitundu ingapo yosiyana m’mwala umodzi.