Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Chivumbulutso 20:1-15

20  Ndipo ndinaona mngelo akutsika kuchokera kumwamba ali ndi kiyi wa paphompho+ ndi unyolo waukulu m’dzanja lake.  Kenako anagwira chinjoka,+ njoka yakale ija,+ amene ndi Mdyerekezi+ ndiponso Satana,+ ndi kumumanga zaka 1,000.  Ndipo anamuponyera m’phompho+ ndi kutseka pakhomo pa phompholo n’kuikapo chidindo kuti asasocheretsenso mitundu ya anthu kufikira zitatha zaka 1,000. Pambuyo pake, adzamasulidwa kanthawi kochepa.+  Kenako ndinaona mipando yachifumu+ ndi amene anakhalapo. Iwo anapatsidwa mphamvu yoweruza.+ Ndiyeno ndinaona miyoyo ya amene anaphedwa ndi nkhwangwa chifukwa cha kuchitira umboni za Yesu, ndi kulankhula za Mulungu. Ndinaonanso anthu amene sanalambire chilombo+ kapena chifaniziro chake,+ ndipo sanalandire chizindikiro pamphumi pawo ndi padzanja pawo.+ Iwo anakhalanso ndi moyo ndipo analamulira monga mafumu+ limodzi ndi Khristu zaka 1,000.  (Akufa+ enawo sanakhalenso ndi moyo kufikira zitatha zaka 1,000.)+ Uku ndi kuuka koyamba+ kwa akufa.  Wodala+ ndi woyera+ ndiye aliyense wouka nawo pa kuuka koyamba. Pa iwo, imfa yachiwiri+ ilibe ulamuliro.+ Koma adzakhala ansembe+ a Mulungu ndi a Khristu, ndipo adzalamulira monga mafumu limodzi naye zaka 1,000.+  Tsopano zikadzangotha zaka 1,000, Satana adzamasulidwa m’ndende yake,  ndipo adzatuluka kukasocheretsa mitundu ya anthu kumakona onse anayi a dziko lapansi. Mitunduyo ndiyo Gogi ndi Magogi, ndipo adzaisonkhanitsa pamodzi kunkhondo. Kuchuluka kwawo kudzakhala ngati mchenga wa kunyanja.+  Iwo adzayenda n’kufalikira mpaka kumbali zonse za dziko lapansi, kenako adzazungulira msasa wa oyera,+ ndi mzinda wokondedwa.+ Koma moto udzatsika kuchokera kumwamba ndi kuwapsereza.+ 10  Mdyerekezi,+ amene anali kuwasocheretsa, adzaponyedwa m’nyanja yamoto ndi sulufule, mmene muli kale chilombo+ ndi mneneri wonyenga uja.+ Ndipo iwo adzazunzidwa usana ndi usiku kwamuyaya. 11  Kenako ndinaona mpando wachifumu waukulu woyera, ndi amene anakhalapo.+ Dziko lapansi ndi kumwamba zinathawa+ pamaso pake, ndipo malo a zimenezi sanapezekenso. 12  Ndiye ndinaona akufa, olemekezeka ndi onyozeka,+ ataimirira pamaso pa mpando wachifumuwo, ndipo mipukutu inafunyululidwa. Koma mpukutu wina unafunyululidwa, ndiwo mpukutu wa moyo.+ Ndipo akufa anaweruzidwa malinga ndi zolembedwa m’mipukutuyo, mogwirizana ndi ntchito zawo.+ 13  Nyanja inapereka akufa amene anali mmenemo. Nayonso imfa ndi Manda zinapereka akufa+ amene anali mmenemo. Aliyense wa iwo anaweruzidwa malinga ndi ntchito zake.+ 14  Ndipo imfa+ ndi Manda zinaponyedwa m’nyanja yamoto.+ Nyanja yamoto imeneyi ikuimira imfa yachiwiri.+ 15  Komanso, aliyense amene sanapezeke atalembedwa m’buku la moyo+ anaponyedwa m’nyanja yamoto.+

Mawu a M'munsi