Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Chivumbulutso 12:1-17

12  Kenako chizindikiro chachikulu+ chinaoneka kumwamba. Ndicho mkazi+ atavala dzuwa, ndipo mwezi unali kunsi kwa mapazi ake. Kumutu kwake kunali chisoti chachifumu chokhala ndi nyenyezi 12,  ndipo mkaziyo anali ndi pakati. Iye analira pomva ululu chifukwa cha zowawa za pobereka.  Chizindikiro chinanso chinaoneka kumwamba, ndipo ndinaona chinjoka chachikulu+ chofiira, chokhala ndi mitu 7 ndi nyanga 10, ndipo pamitupo panali zisoti zachifumu 7.  Mchira+ wake unakokolola gawo limodzi mwa magawo atatu a nyenyezi zakumwamba n’kuzigwetsera kudziko lapansi.+ Ndipo chinjokacho chinangoimabe pamaso pa mkazi uja, amene anali pafupi kubereka,+ kuti akabereka chidye+ mwana wakeyo.  Mkaziyo anabereka mwana wamwamuna,+ mnyamata amene adzakusa mitundu yonse ndi ndodo yachitsulo.+ Ndipo mwana wakeyo anatengedwa msangamsanga n’kupititsidwa kwa Mulungu ndi kumpando wake wachifumu.+  Koma mkaziyo anathawira kuchipululu,+ kumene Mulungu anamukonzera malo, kuti akadyetsedwe masiku 1,260.+  Ndipo kumwamba kunabuka nkhondo: Mikayeli+ ndi angelo ake anamenyana ndi chinjoka. Chinjokacho ndi angelo ake chinamenya nkhondo,  koma sichinapambane, ndipo malo awo sanapezekenso kumwamba.  Choncho chinjokacho+ chinaponyedwa pansi, njoka yakale ija, iye wotchedwa Mdyerekezi+ ndi Satana, amene akusocheretsa dziko lonse lapansi+ kumene kuli anthu. Iye anaponyedwa kudziko lapansi,+ ndipo angelo akenso anaponyedwa naye limodzi. 10  Ndipo ndinamva mawu ofuula kumwamba, akuti: “Tsopano chipulumutso,+ mphamvu,+ ufumu wa Mulungu wathu,+ ndi ulamuliro wa Khristu+ wake zafika, chifukwa woneneza abale athu waponyedwa pansi. Iyeyo anali kuwaneneza usana ndi usiku pamaso pa Mulungu wathu.+ 11  Iwo anamugonjetsa+ chifukwa cha magazi a Mwanawankhosa,+ ndiponso chifukwa cha mawu a umboni wawo.+ Ndipo iwo sanaone kuti miyoyo yawo ndi yofunika,+ ngakhale pamene anali pa ngozi yoti akhoza kufa. 12  Pa chifukwa chimenechi, kondwerani kumwamba inu ndi inu okhala kumeneko!+ Tsoka+ dziko lapansi ndi nyanja,+ chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, ndipo ali ndi mkwiyo waukulu podziwa kuti wangotsala ndi kanthawi kochepa.”+ 13  Tsopano chinjoka chitaona kuti achigwetsera kudziko lapansi,+ chinazunza mkazi amene anabereka mwana wamwamuna uja. 14  Koma mkaziyo anapatsidwa mapiko awiri a chiwombankhanga chachikulu kuti aulukire kuchipululu,+ kumalo ake aja. Kumeneko n’kumene akudyetsedwa+ kwa nthawi imodzi, nthawi ziwiri, ndi hafu ya nthawi,+ kutali ndi njoka ija. 15  Kenako njokayo inalavula madzi+ ngati mtsinje kuchokera m’kamwa mwake, kulavulira mkazi uja, kuti amizidwe ndi mtsinjewo.+ 16  Koma dziko lapansi linathandiza mkaziyo.+ Dzikolo linatsegula pakamwa pake ndi kumeza mtsinje umene chinjoka chija chinalavula kuchokera m’kamwa mwake. 17  Ndipo chinjokacho chinakwiya ndi mkazi uja, moti chinapita kukachita nkhondo ndi otsala a mbewu yake, amene amasunga malamulo a Mulungu, amenenso ali ndi ntchito yochitira umboni+ za Yesu.

Mawu a M'munsi