Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Chivumbulutso 11:1-19

11  Ndiyeno ndinapatsidwa bango lokhala ngati ndodo+ ndipo ndinauzidwa kuti: “Nyamuka, kayeze nyumba yopatulika ya pakachisi+ wa Mulungu, guwa lansembe, ndi amene akulambira mmenemo.  Koma bwalo lakunja+ kwa nyumba yopatulika ya pakachisi ulisiye, usaliyeze m’pang’ono pomwe chifukwa laperekedwa kwa anthu a mitundu ina.+ Ndipo iwo adzapondaponda mzinda woyera+ kwa miyezi 42.+  Ndiyeno ndidzachititsa mboni zanga ziwiri+ kunenera+ kwa masiku 1,260, zitavala ziguduli.”+  Mboni zimenezi zikuimiridwa ndi mitengo iwiri ya maolivi,+ ndi zoikapo nyale ziwiri,+ ndipo mbonizo zaimirira pamaso pa Ambuye wa dziko lapansi.+  Ngati wina aliyense akufuna kuzivulaza, moto umatuluka m’kamwa mwawo ndi kupsereza adani awo.+ Ngati wina angafune kuzivulaza, ayenera kuphedwa mwanjira imeneyi.  Mboni zimenezi zili ndi ulamuliro wotseka kumwamba+ kuti mvula isagwe m’masiku onse amene zikunenera. Zilinso ndi ulamuliro pamadzi, woti ziwasandutse magazi. Komanso zili ndi ulamuliro wokantha dziko lapansi ndi mliri wamtundu uliwonse, maulendo ambirimbiri mogwirizana ndi mmene zingafunire.  Zikamaliza kuchitira umboni wawo, chilombo chotuluka muphompho+ chidzachita nazo nkhondo, ndipo chidzazigonjetsa ndi kuzipha.+  Mitembo yawo idzagona pamsewu waukulu mumzinda waukulu, umene mophiphiritsira ukutchedwa Sodomu+ ndi Iguputo, kumenenso Ambuye wawo anapachikidwa.+  Mitundu ya anthu, mafuko, zinenero, ndi mayiko,+ adzayang’anitsitsa mitembo yawo masiku atatu ndi hafu,+ ndipo sadzalola kuti mitemboyo iikidwe m’manda. 10  Okhala padziko lapansi adzakondwera+ kwambiri ndi imfa yawoyo. Iwo adzatumizirana+ mphatso, chifukwa aneneri awiriwa anazunza okhala padziko lapansi. 11  Masiku atatu ndi hafu+ aja atatha, mzimu wa moyo wochokera kwa Mulungu unalowa mwa mboni zija.+ Ndiyeno mbonizo zinaimirira, ndipo amene anali kuziona anagwidwa ndi mantha aakulu. 12  Kenako mbonizo zinamva mawu ofuula+ ochokera kumwamba akuziuza kuti: “Kwerani kuno.”+ Ndipo zinakwera kumwamba mumtambo, moti adani awo anaziona. 13  Mu ola limenelo, kunachitika chivomezi chachikulu, ndipo gawo limodzi mwa magawo khumi+ a mzindawo linagwa. Anthu 7,000 anaphedwa ndi chivomezicho, ndipo ena onse anachita mantha n’kupereka ulemerero kwa Mulungu wakumwamba.+ 14  Tsoka+ lachiwiri linapita. Koma tsoka lachitatu linali kubwera mofulumira. 15  Mngelo wa 7 analiza lipenga+ lake. Ndipo kumwamba kunamveka mawu osiyanasiyana, akunena mokweza kuti: “Ufumu wa dziko wakhala ufumu wa Ambuye wathu ndi wa Khristu wake.+ Iye adzalamulira monga mfumu kwamuyaya.”+ 16  Ndipo akulu 24 aja,+ amene anali atakhala pamipando yawo yachifumu pamaso pa Mulungu, anagwada n’kuwerama mpaka nkhope zawo pansi,+ ndipo analambira Mulungu+ 17  ndi mawu akuti: “Tikukuyamikani+ inu Yehova, Mulungu Wamphamvuyonse, Inu amene mulipo ndi amene munalipo, chifukwa mwatenga mphamvu yanu yaikulu ndi kuyamba kulamulira monga mfumu.+ 18  Koma mitundu ya anthu inakwiya, ndipo mkwiyo wanu unafika. Inafikanso nthawi yoikidwiratu yakuti akufa aweruzidwe, nthawi yopereka mphoto+ kwa akapolo anu aneneri,+ ndiponso kwa oyerawo, ndi oopa dzina lanu, olemekezeka ndi onyozeka omwe.+ Komanso, nthawi yowononga+ amene akuwononga dziko lapansi.” 19  Nyumba yopatulika ya pakachisi wa Mulungu imene ili kumwamba+ inatsegulidwa, ndipo likasa la pangano lake linaonekera m’nyumba yake yopatulika+ ya pakachisi. Pamenepo kunachitika mphezi, kunamveka mawu, kunagunda mabingu, kunachita chivomezi, ndipo kunagwa matalala ambiri zedi.

Mawu a M'munsi