Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Chivumbulutso 1:1-20

1  Chivumbulutso+ choperekedwa ndi Yesu Khristu, chimene Mulungu anamupatsa,+ kuti aonetse akapolo ake+ zinthu zimene ziyenera kuchitika posachedwapa.+ Yesuyo anatumiza mngelo wake+ kuti adzapereke Chivumbulutsocho mwa zizindikiro+ kwa kapolo wake Yohane.+  Yohaneyo anachitira umboni mawu a Mulungu,+ ndiponso umboni umene Yesu Khristu anapereka,+ kutanthauza zonse zimene anaona.  Wodala+ ndi munthu amene amawerenga mokweza,+ ndiponso anthu amene akumva mawu a ulosi umenewu,+ komanso amene akusunga zolembedwamo,+ pakuti nthawi yoikidwiratu ili pafupi.+  Ine Yohane, ndikulembera mipingo 7+ ya m’chigawo cha Asia. Kukoma mtima kwakukulu, ndi mtendere zikhale nanu kuchokera kwa “Iye amene alipo, amene analipo, ndi amene akubwera,”+ ndiponso kuchokera kwa mizimu 7+ yokhala pamaso pa mpando wake wachifumu.  Komanso, kuchokera kwa Yesu Khristu, “Mboni Yokhulupirika,”+ “Woyamba kubadwa kuchokera kwa akufa,”+ ndiponso “Wolamulira wa mafumu a dziko lapansi.”+ Kwa iye amene amatikonda,+ amenenso anatimasula ku machimo athu ndi magazi ake enieniwo,+  n’kutipanga kukhala mafumu+ ndi ansembe+ kwa Mulungu wake ndi Atate wake, kwa iyeyo kukhale ulemerero ndi mphamvu kwamuyaya.+ Ame.  Taonani! Akubwera ndi mitambo,+ ndipo diso lililonse lidzamuona,+ ngakhalenso anthu amene anamulasa.+ Ndipo mafuko onse a padziko lapansi adzadziguguda pachifuwa ndi chisoni chifukwa cha iye.+ Ame.  “Ine ndine Alefa ndi Omega,”*+ akutero Yehova Mulungu, “Iye amene alipo, amene analipo, ndi amene akubwera,+ Wamphamvuyonse.”+  Ine Yohane, m’bale wanu ndi wogawana nanu masautso+ a Yesu,+ mu ufumu+ ndi m’kupirira,+ ndinali pachilumba cha Patimo chifukwa cholankhula za Mulungu ndi kuchitira umboni za Yesu.+ 10  Mwa mzimu,+ ndinapezeka kuti ndili+ m’tsiku la Ambuye,+ ndipo kumbuyo kwanga ndinamva mawu amphamvu+ ngati kulira kwa lipenga. 11  Mawuwo anali akuti: “Zimene uone, lemba+ mumpukutu ndi kuutumiza kumipingo 7+ yotsatirayi: wa ku Efeso,+ wa ku Simuna,+ wa ku Pegamo,+ wa ku Tiyatira,+ wa ku Sade,+ wa ku Filadefiya,+ ndi wa ku Laodikaya.”+ 12  Ndinacheuka kuti ndione, kuti ndani amene anali kundilankhula. Nditacheuka, ndinaona zoikapo nyale 7 zagolide.+ 13  Pakati pa zoikapo nyalezo, panali wina wooneka ngati mwana wa munthu+ atavala chovala chofika kumapazi, atamanga lamba wagolide pachifuwa. 14  Komanso, mutu ndi tsitsi lake zinali zoyera+ ngati ubweya wa nkhosa woyera, zoyera kwambiri kuti mbee! Ndipo maso ake anali ngati lawi la moto.+ 15  Mapazi ake anali ngati mkuwa woyengedwa+ bwino ukamanyezimira m’ng’anjo, ndipo mawu+ ake anali ngati mkokomo wa madzi ambiri. 16  M’dzanja lake lamanja anali ndi nyenyezi 7.+ M’kamwa mwake munali kutuluka lupanga lalitali, lakuthwa konsekonse.+ Nkhope yake inali yowala ngati dzuwa limene likuwala kwambiri.+ 17  Nditamuona, ndinagwa pamapazi ake ngati kuti ndafa. Ndipo anandigwira ndi dzanja lake lamanja ndi kundiuza kuti: “Usachite mantha.+ Ine ndine Woyamba+ ndi Wotsiriza,+ 18  ndiponso wamoyo.+ Ndinali wakufa,+ koma taona, ndili ndi moyo kwamuyaya,+ ndipo ndili ndi makiyi a imfa+ ndi a Manda.*+ 19  Choncho lemba zimene waona, zimene zikuchitika panopa, ndi zimene zidzachitike pambuyo pa zimenezi.+ 20  Koma za chinsinsi chopatulika cha nyenyezi 7,+ zimene waona m’dzanja langa lamanja, ndi za chinsinsi cha zoikapo nyale 7 zagolide,+ tanthauzo lake ndi ili: Nyenyezi 7, zikuimira angelo* a mipingo 7, ndipo zoikapo nyale 7, zikuimira mipingo 7.+

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Zakumapeto 5.
Kapena kuti, “amithenga.”