Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Aroma 9:1-33

9  Ndikunena zoona+ mwa Khristu, sindikunama ayi.+ Ine pamodzi ndi chikumbumtima changa tikuchitira umboni mwa mzimu woyera,  kuti ndili ndi chisoni chachikulu ndiponso mtima ukundipweteka nthawi zonse.+  Ndikanakonda kuti ineyo ndichotsedwe kwa Khristu monga wotembereredwa m’malo mwa abale anga,+ amene ali anthu a mtundu wanga.+  Amenewa ndi Aisiraeli,+ amene Mulungu anawatenga kukhala ana ake.+ Anawapatsanso ulemerero,+ mapangano,+ Chilamulo,+ utumiki wopatulika+ ndi malonjezo.+  Iwo ndi ana a makolo akale aja.+ Komanso Khristu monga munthu,+ anatuluka pakati pawo. Mulungu,+ amene ndiye wamkulu pa zinthu zonse, atamandike kwamuyaya. Ame.  Komabe, sizili ngati kuti mawu a Mulungu analephera.+ Pakuti si onse ochokera kwa Isiraeli amene alidi “Aisiraeli.”+  Ndiponso si onse amene ali ana chifukwa chongokhala mbewu ya Abulahamu.+ Koma Malemba amati, “Amene adzatchedwa ‘mbewu yako’ adzachokera mwa Isaki.”+  Izi zikutanthauza kuti, si ana akuthupi+ amene alidi ana a Mulungu,+ koma ana a lonjezo+ ndiwo amayesedwa mbewu.  Popeza lonjezo lija linati: “Ndidzabweranso nthawi ngati yomwe ino, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.”+ 10  Lonjezolo silinaperekedwe pa nthawi imeneyo yokha ayi, koma linaperekedwanso kwa Rabeka pamene anali ndi pakati pa mapasa+ a Isaki kholo lathu lija. 11  Mapasawo asanabadwe ndiponso asanachite chilichonse chabwino kapena choipa,+ kuti cholinga cha Mulungu powasankha chikhalebe chodalira Iye amene amaitana,+ osati chodalira ntchito, 12  Rabeka anauzidwa kuti: “Wamkulu adzakhala kapolo wa wamng’ono.”+ 13  Monga mmene Malemba amanenera kuti: “Ndinakonda Yakobo, koma Esau ndinadana naye.”+ 14  Ndiye tinene kuti chiyani? Kodi Mulungu alibe chilungamo?+ Ayi si zimenezo! 15  Pakuti iye anauza Mose kuti: “Amene ndikufuna kumusonyeza chifundo, ndidzamusonyeza chifundo, ndipo ndidzamvera chisoni aliyense amene ndikufuna kumumvera chisoni.”+ 16  Chotero, sizidalira munthu wofunayo kapena amene akuthamanga, koma Mulungu,+ amene ali ndi chifundo.+ 17  Pakuti ponena za Farao, Lemba linati: “Ndakusiya ndi moyo kuti ndikusonyeze mphamvu zanga, ndi kuti dzina langa lilengezedwe padziko lonse lapansi.”+ 18  Chotero, iye amachitira chifundo munthu amene wafuna kumuchitira chifundo,+ koma amalola anthu ena kuti aumitse mitima yawo.+ 19  Mwina unganene kwa ine kuti: “N’chifukwa chiyani Mulungu akupezabe anthu zifukwa? Kodi ndani angatsutse chifuniro chake chimene chinanenedwa?”+ 20  Munthu iwe!+ Iweyo ndiwe ndani kuti uziyankhana ndi Mulungu?+ Kodi chinthu choumbidwa chinganene kwa munthu amene anachiumba kuti, “Unandipangiranji motere?”+ 21  Kodi simudziwa kuti woumba mbiya+ ali ndi ufulu woumba chiwiya china cholemekezeka, china chonyozeka kuchokera pa dongo limodzi?+ 22  Bwanji ngati Mulungu analekerera moleza mtima kwambiri ziwiya za mkwiyo zoyenera kuwonongedwa ngakhale kuti akufuna kuonetsa mkwiyo wake ndi mphamvu zake?+ 23  Ndiponso bwanji ngati anachita zimenezo kuti asonyeze kukula kwa ulemerero wake+ kwa ziwiya+ zachifundo, zomwe anazikonzeratu kuti zikhale zaulemerero,+ 24  zimene ndi ifeyo amene anatiitana osati kuchokera mwa Ayuda okha komanso mwa mitundu ina?+ 25  Zilinso monga mmene ananenera m’buku la Hoseya kuti: “Anthu amene si anthu anga+ ndidzawatcha ‘anthu anga,’ ndipo mkazi amene sanali wokondedwa ndidzamutcha ‘wokondedwa.’+ 26  Ndipo pamalo pamene anauzidwapo kuti, ‘Inu sindinu anthu anga,’ pamalo omwewo adzatchedwa ‘ana a Mulungu wamoyo.’”+ 27  Komanso, Yesaya analankhula mofuula zokhudza Isiraeli kuti: “Ngakhale kuti ana a Isiraeli adzakhala ochuluka ngati mchenga wa m’nyanja,+ ndi ochepa okha amene adzapulumuke.+ 28  Pakuti Yehova adzazenga milandu padziko lapansi, ndi kuimaliza yonse mwachangu.”+ 29  Ndiponso, monga Yesaya ananeneratu kuti: “Yehova wa makamu+ akanapanda kutisiyira mbewu, tikanakhala ngati Sodomu, ndipo tikanafanana ndi Gomora.”+ 30  Ndiye tinene kuti chiyani? Tinene kuti, ngakhale kuti anthu a mitundu ina sanatsatire chilungamo, iwo anapeza chilungamo+ chimene chimapezeka chifukwa cha chikhulupiriro.+ 31  Koma ngakhale kuti Aisiraeli anali kutsatira lamulo la chilungamo, sanalipeze lamulolo.+ 32  Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti iwo sanalitsatire mwa chikhulupiriro, koma malinga ndi kuganiza kwawo, analitsatira mwa ntchito.+ Iwo anakhumudwa “pamwala wokhumudwitsa”+ 33  monga mmene Malemba amanenera kuti: “Inetu ndikuika mwala+ wopunthwitsa ndiponso mwala wokhumudwitsa+ m’Ziyoni, koma munthu wokhulupirira mwalawo sadzakhumudwa.”+

Mawu a M'munsi