Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Aroma 7:1-25

7  Kodi mwina simukudziwa abale, (popeza ndikulankhula ndi anthu odziwa chilamulo,) kuti Chilamulo chimakhala mbuye wa munthu pamene munthuyo ali moyo?+  Mwachitsanzo, mkazi wokwatiwa amakhala womangidwa kwa mwamuna wake mwalamulo pamene mwamunayo ali moyo. Koma mwamuna wake akamwalira, mkazi amamasuka ku lamulo la mwamuna wake.  Ngati angakwatiwe ndi mwamuna wina, mwamuna wake ali moyo, mkaziyo adzatchedwa wachigololo.+ Koma ngati mwamuna wake wamwalira, mkaziyo wamasuka ku lamulo lake, chotero si wachigololo ngati atakwatiwa ndi mwamuna wina.+  Choncho abale anga, thupi la Khristu linakupangani kukhala akufa ku Chilamulo,+ kuti mukhale a winawake,+ a iye amene anaukitsidwa kwa akufa,+ kuti tibale zipatso+ kwa Mulungu.  Chifukwa pamene tinali kukhala mogwirizana ndi thupi,+ zilakolako za uchimo zimene zinaonekera chifukwa cha Chilamulo zinali kugwira ntchito m’ziwalo zathu kuti tibale zipatso za imfa.+  Koma tsopano tamasulidwa ku Chilamulo,+ chifukwa tafa+ ku chilamulo chimene chinali kutimanga chija, kuti tikhale akapolo+ m’njira yatsopano motsogoleredwa ndi mzimu,+ osati m’njira yakale motsogoleredwa ndi malamulo olembedwa.+  Ndiye tinene kuti chiyani? Kodi Chilamulo ndi uchimo?+ Ayi m’pang’ono pomwe! Kunena zoona, sindikanadziwa uchimo+ zikanakhala kuti panalibe Chilamulo. Ndiponso, mwachitsanzo, sindikanadziwa kusirira kwa nsanje+ zikanakhala kuti Chilamulo sichinanene kuti: “Usasirire mwansanje.”  Koma chifukwa cha lamulo,+ uchimo unapeza njira yondichititsa kukhala wosirira chinthu chilichonse mwansanje. Chifukwa popanda chilamulo, uchimo unali wakufa.+  Ndinalitu wamoyo chilamulo chisanabwere.+ Koma pamene malamulo anafika,+ uchimo unakhalanso ndi moyo, koma ineyo ndinafa.+ 10  Tsopano ine ndinaona lamulo lopatsa moyolo kuti ndi lobweretsa imfa.+ 11  Pakuti chifukwa cha lamulo, uchimo unapeza njira yondinyenga+ ndipo unandipha. 12  Choncho, Chilamulo kumbali yake n’choyera,+ ndipo malamulo ndi oyera, olungama+ ndi abwino. 13  Ndiye kodi chinthu chabwino chinakhala imfa kwa ine? Ayi ndithu! Koma uchimo ndiwo unakhala imfa kwa ine, kuti uonekere kuti ndi umene ukubala imfa mwa ine kudzera m’chinthu chabwinocho,+ kuti kudzera m’malamulo, uchimowo uonekere kuti ndi woipa kwambiri.+ 14  Pakuti tikudziwa kuti Chilamulo n’chauzimu,+ koma ine ndine wakuthupi, wogulitsidwa ku uchimo.+ 15  Sindimvetsetsa kuti n’chifukwa chiyani ndimachita zinthu motere. Chifukwa zimene ndimafuna kuchita, sindizichita. Koma zimene ndimadana nazo ndi zimene ndimachita. 16  Komabe, ngati zimene sindifuna kuchita ndi zimene ndimachita,+ ndikuvomereza kuti Chilamulo ndi chabwino.+ 17  Koma tsopano amene akuchita zimenezo si inenso ayi, koma uchimo umene uli mwa ine. 18  Ndikudziwa kuti mwa ine, ndikunenatu za m’thupi langa, simukhala kanthu kabwino. Pakuti ndimafuna+ kuchita zabwino, koma sinditha kuzichita.+ 19  Chinthu chabwino chimene ndimafuna kuchita sindichita,+ koma choipa chimene sindifuna kuchita ndi chimene ndimachita. 20  Tsopano ngati zimene sindifuna ndi zimene ndikuchita, amene akuchita zimenezo si inenso ayi, koma uchimo umene ukukhala mwa ine.+ 21  Chotero kwa ine, ndimapeza lamulo ili lakuti: Pamene ndikufuna kuchita chinthu chabwino,+ choipa chimakhala chili ndi ine.+ 22  Mumtima mwanga+ ndimasangalala kwambiri+ ndi chilamulo cha Mulungu, 23  koma ndimaona chilamulo china m’ziwalo zanga+ chikumenyana+ ndi chilamulo cha m’maganizo mwanga+ n’kundipanga kukhala kapolo wa chilamulo cha uchimo+ chimene chili m’ziwalo zanga. 24  Munthu wovutika ine! Ndani adzandipulumutse ku thupi limene likufa imfa imeneyi?+ 25  Mulungu adzatero kudzera mwa Yesu Khristu Ambuye wathu.+ Chotero, m’maganizo mwanga ineyo ndine kapolo wa chilamulo cha Mulungu,+ koma m’thupi langa ndine kapolo wa chilamulo cha uchimo.+

Mawu a M'munsi