Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Aroma 4:1-25

4  Popeza zili choncho, kodi tinene chiyani za Abulahamu kholo lathu?+  Mwachitsanzo, chikhala kuti Abulahamu anayesedwa wolungama chifukwa cha ntchito,+ akanakhala ndi chifukwa chodzitamandira, koma osati kwa Mulungu.  Kodi lemba limati chiyani paja? Limati: “Abulahamu anakhulupirira mwa Yehova, ndipo anaonedwa ngati wolungama.”+  Chifukwa munthu amene wagwira ntchito+ saona malipiro ake ngati kukoma mtima kwakukulu,+ koma ngati ngongole.+  Munthu amene sadalira ntchito zake koma amakhulupirira+ Mulungu, amayesedwa wolungama chifukwa cha chikhulupiriro chake,+ pakuti Mulungu amatha kuona munthu wosatsatira malamulo ake kukhala wolungama.  Davide ananena kuti munthu amene Mulungu amamuyesa wolungama popanda munthuyo kuchita ntchito ndi wodala. Iye anati:  “Odala ndi amene akhululukidwa zochita zawo zosamvera malamulo+ ndipo machimo awo aphimbidwa.+  Wodala ndi munthu amene Yehova sadzawerengera tchimo lake.”+  Chotero, kodi anthu odulidwa okha ndi amene amakhala odala choncho? Kapena kodi osadulidwa nawonso amakhala odala?+ Popeza timati: “Abulahamu anaonedwa ngati wolungama chifukwa cha chikhulupiriro chake.”+ 10  Koma kodi iye anali wotani pamene anayesedwa wotero? Kodi anali wodulidwa kapena wosadulidwa?+ Sanali wodulidwa, koma wosadulidwa. 11  Ndipo Mulungu anapatsa Abulahamu mdulidwe monga chizindikiro.+ Chizindikiro chimenechi chinali chosonyeza kuti, chifukwa cha chikhulupiriro, Mulungu anamuyesa wolungama asanadulidwe, kuti adzakhale tate+ wa onse osadulidwa okhala ndi chikhulupiriro,+ kuti anthuwo adzaonedwe kuti ndi olungama. 12  Kutinso adzakhale tate wa ana odulidwa, osati wa okhawo ochita mdulidwe, komanso wa amene amayenda moyenerera m’mapazi a chikhulupiriro chimene bambo wathu+ Abulahamu anali nacho asanadulidwe. 13  Pakuti Abulahamu kapena mbewu yake sanalonjezedwe kuti adzalandira dziko monga cholowa chawo chifukwa cha chilamulo ayi.+ Analandira lonjezolo chifukwa chakuti anali wolungama mwa chikhulupiriro.+ 14  Chifukwa ngati anthu oumirira kusunga chilamulo ndiwo adzalandire cholowacho, ndiye kuti chikhulupiriro chilibenso ntchito ndipo lonjezo lija lathetsedwa.+ 15  Kwenikweni, Chilamulo chimabala mkwiyo,+ koma pamene palibe lamulo, palibenso kulakwa.+ 16  Chotero iye anapatsidwa lonjezolo+ chifukwa cha chikhulupiriro, kuti likhale mwa kukoma mtima kwakukulu,+ ndiponso kuti likhale lotsimikizika kwa mbewu yake yonse,+ osati yotsatira Chilamulo yokha ayi, komanso yotsatira chikhulupiriro cha Abulahamu. (Iye ndiye tate+ wa ife tonse, 17  monga mmene Malemba amanenera kuti: “Ndakuika kuti ukhale tate wa mitundu yambiri.”)+ Izi zinali choncho pamaso pa Uyo amene Abulahamu anam’khulupirira, inde pamaso pa Mulungu, amene amapereka moyo kwa akufa+ ndipo amanena za zinthu zimene palibe ngati kuti zilipo.+ 18  Anali ndi chiyembekezo ndiponso chikhulupiriro+ chakuti adzakhala tate wa mitundu yambiri,+ ngakhale kuti zimenezi zinkaoneka kuti n’zosatheka. Anakhulupirira zimenezi mogwirizana ndi zimene zinanenedwa kuti: “Umu ndi mmene mbewu yako idzakhalire.”+ 19  Ndiponso, ngakhale kuti chikhulupiriro chake sichinafooke, anaganizira za thupi lake, limene linali lakufa tsopano,+ popeza anali ndi zaka pafupifupi 100.+ Anaganiziranso zakuti Sara anali wosabereka.+ 20  Koma chifukwa cha lonjezo+ la Mulungu, iye sanagwedezeke pa chikhulupiriro chake+ ndipo chikhulupiriro chakecho chinamulimbitsa.+ Mwa kutero, anapereka ulemerero kwa Mulungu 21  ndipo anali wotsimikiza kuti zimene Mulungu analonjeza anali ndi mphamvu yozichita.+ 22  Ndiye chifukwa chake “anaonedwa ngati wolungama.”+ 23  Komabe, zonena kuti “anayesedwa+ wolungama” sizinalembedwere iye yekha,+ 24  komanso ife amene tidzayesedwa otero, chifukwa chakuti timakhulupirira iye amene anaukitsa Yesu Ambuye wathu kwa akufa.+ 25  Iye anaperekedwa chifukwa cha machimo athu+ ndipo anaukitsidwa kuti tiyesedwe olungama.+

Mawu a M'munsi