Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Aroma 3:1-31

3  Choncho, kodi Myuda+ ndi woposa ena motani? Kapena kodi phindu la mdulidwe n’chiyani?+  Iye amaposadi ena kwambiri m’njira iliyonse. Choyamba, chifukwa chakuti mawu opatulika a Mulungu+ anaikidwa m’manja mwa Ayuda.  Nanga ngati ena sanasonyeze chikhulupiriro,+ kodi chifukwa chakuti alibe chikhulupiriro+ ndiye kuti kukhala wokhulupirika kwa Mulungu n’kopanda pake?+  Ayi! Koma Mulungu akhale wonena zoona,+ ngakhale kuti munthu aliyense angapezeke kukhala wonama,+ monganso Malemba amanenera kuti: “Mukamalankhula mumalankhula zachilungamo, kuti mupambane pamene mukuweruzidwa.”+  Komabe, ngati kulungama kwa Mulungu+ kukuonekera chifukwa cha kusalungama kwathu, ndiye tinene kuti chiyani? Kodi tingati Mulungu ndi wosalungama+ poonetsa mkwiyo wake? (Ndikulankhula mmene anthu+ amalankhulira.)  Ayi! Chifukwa Mulungu akapanda kutero, kodi dziko adzaliweruza motani?+  Tsopano ngati chifukwa cha bodza langa choonadi cha Mulungu+ chaonekera kwambiri, ndipo zimenezo zamubweretsera ulemerero, n’chifukwa chiyaninso ndikuweruzidwabe kukhala wochimwa?+  Ndilekeranji kunena zimene amatinamizira zija,+ ndiponso zimene ena amati timanena zakuti: “Tiyeni tichite zoipa kuti pakhale zinthu zabwino”?+ Chiweruzo+ chowafikira anthu amenewo n’chogwirizana ndi chilungamo.+  Ndiye zikatero? Kodi tili pabwino kuposa ena?+ Ayi! Pakuti tanena kale poyamba paja kuti onse, Ayuda ndi Agiriki, ndi ochimwa+ 10  monga mmene Malemba amanenera kuti: “Palibe munthu wolungama ndi mmodzi yemwe.+ 11  Palibe amene ali wozindikira ngakhale pang’ono, palibiretu amene akuyesetsa kupeza Mulungu.+ 12  Anthu onse apanduka, onse pamodzi akhala opanda pake. Palibe amene akusonyeza kukoma mtima, palibiretu ndi mmodzi yemwe.”+ 13  “Mmero wawo ndi manda otseguka. Iwo amalankhula ndi lilime lachinyengo.”+ “M’milomo yawo muli poizoni wa njoka.”+ 14  “Ndipo m’kamwa mwawo mwadzaza mawu otukwana ndi opweteka.”+ 15  “Mapazi awo amathamangira kukhetsa magazi.”+ 16  “Kusakaza ndi kusautsa kuli m’njira zawo,+ 17  ndipo sadziwa njira ya mtendere.”+ 18  “Maso awo saona chifukwa choopera Mulungu.”+ 19  Tikudziwa kuti zinthu zonse zimene Chilamulo+ chimanena chimazinena kwa amene ali m’Chilamulo, kuti pakamwa paliponse patsekedwe+ ndipo dziko lonse likhale loyenera+ kulandira chilango cha Mulungu.+ 20  Chotero pamaso pake palibe munthu amene adzayesedwe wolungama+ mwa ntchito za chilamulo,+ popeza chilamulo chimachititsa kuti tidziwe uchimo molondola.+ 21  Koma tsopano, zaonekera kuti munthu akhoza kukhala wolungama kwa Mulungu+ popanda kutsatira Chilamulo. Zimenezi zinatchulidwanso+ m’Chilamulo+ ndi m’Zolemba za aneneri.+ 22  Kuoneka wolungama pamaso pa Mulungu kumeneku kungatheke mwa kukhulupirira Yesu Khristu,+ ndipo ndi kotheka kwa onse okhala ndi chikhulupiriro.+ Popeza palibe kusiyanitsa.+ 23  Pakuti onse ndi ochimwa+ ndipo ndi operewera pa ulemerero wa Mulungu.+ 24  Ndiponso, kuyesedwa olungama chifukwa cha kukoma mtima kwake kwakukulu+ kumene wakusonyeza, powamasula ndi dipo+ lolipiridwa ndi Khristu Yesu, kuli ngati mphatso yaulere.+ 25  Mulungu anam’pereka monga nsembe yachiyanjanitso,+ mwa kukhala ndi chikhulupiriro m’magazi ake.+ Mulungu anachita izi pofuna kuonetsa chilungamo chake pokhululuka machimo+ amene anachitika kale, pamene iye anali kusonyeza khalidwe losakwiya msanga,+ 26  ndipo akuonetsa chilungamo chake+ m’nyengo inoyo pakutcha munthu amene ali ndi chikhulupiriro mwa Yesu kuti ndi wolungama.+ 27  Chotero, kodi pamenepa palinso chifukwa chodzitama nacho?+ Palibiretu. Malinga ndi chilamulo chiti?+ Chija chofuna ntchito?+ Ndithudi ayi, koma mwa lamulo la chikhulupiriro.+ 28  Popeza tsopano taona kuti munthu amayesedwa wolungama mwa chikhulupiriro, osati mwa ntchito za chilamulo.+ 29  Kapena kodi iye ndi Mulungu wa Ayuda okha?+ Kodi salinso Mulungu wa anthu a mitundu ina?+ Inde, iye alinso Mulungu wa anthu a mitundu ina,+ 30  ngati Mulungu alidi mmodzi.+ Iye ndi amene adzayese anthu odulidwa+ kuti ndi olungama chifukwa cha chikhulupiriro, ndiponso anthu osadulidwa+ adzawayesa olungama mwa chikhulupiriro chawo. 31  Koma kodi tikuthetsa chilamulo mwa chikhulupiriro chathu?+ Ayi! M’malomwake, tikulimbikitsa chilamulo.+

Mawu a M'munsi