Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Aroma 2:1-29

2  Choncho munthu iwe,+ kaya ukhale ndani, ulibe chifukwa chomveka chodzilungamitsira ngati umaweruza ena.+ Pakuti pa nkhani imene ukuweruza nayo wina, ukudzitsutsa wekha, chifukwa iwenso woweruzawe+ umachita zomwezo.+  Tikudziwa kuti Mulungu amaweruza anthu amene amachita zimenezi kuti ndi oyenera kulandira chilango ndipo chiweruzo chake ndi chogwirizana ndi choonadi.+  Koma tsopano, iwe+ amene umaweruza anthu amene amachita zinthu zimene iwenso umachita, kodi ukuganiza kuti udzazemba chiweruzo cha Mulungu?+  Kapena kodi ukunyoza kukoma mtima kwake kwakukulu,+ kusakwiya msanga+ kwake ndi kuleza mtima kwake,+ chifukwa chakuti sudziwa kuti cholinga cha kukoma mtima kwa Mulungu ndicho kukuthandiza kuti ulape?+  Koma chifukwa chakuti ndiwe wosafuna kusintha khalidwe+ ndiponso wa mtima wosalapa,+ ukudzisungira mkwiyo wa Mulungu.+ Mulungu adzasonyeza mkwiyo+ umenewu pa tsiku loulula+ chiweruzo chake cholungama.+  Iye adzaweruza aliyense malinga ndi ntchito zake motere:+  Moyo wosatha kwa anthu amene popirira m’ntchito yabwino akuyesetsa kupeza ulemerero, ulemu ndi moyo wosakhoza kuwonongeka.+  Koma adzapereka chilango ndi mkwiyo+ kwa okonda mikangano+ amenenso samvera choonadi+ koma amamvera zosalungama.  Aliyense wochita zoipa, kuyambira Myuda+ mpaka Mgiriki,+ adzaona nsautso ndi zowawa. 10  Koma aliyense wochita zabwino,+ choyamba Myuda+ kenako Mgiriki,+ adzalandira ulemerero, ulemu ndi mtendere. 11  Pakuti Mulungu alibe tsankho.+ 12  Mwachitsanzo, onse amene anachimwa popanda chilamulo adzawonongekanso popanda chilamulo.+ Koma onse amene anachimwa ali ndi chilamulo+ adzaweruzidwa ndi chilamulo.+ 13  Pajatu akumva chabe chilamulo si amene amakhala olungama pamaso pa Mulungu, koma otsatira+ chilamulo ndiwo adzayesedwa olungama.+ 14  Nthawi zonse anthu a mitundu+ amene alibe chilamulo+ akamachita mwachibadwa zinthu za m’chilamulo,+ amakhala chilamulo kwa iwo eni ngakhale kuti alibe chilamulo. 15  Amenewa ndiwo amasonyeza kuti mfundo za m’chilamulo zinalembedwa m’mitima mwawo,+ pamene chikumbumtima chawo+ chimachitira umboni pamodzi ndi iwowo, ndipo maganizo awo amawatsutsa+ ngakhalenso kuwavomereza. 16  Zimenezi zidzaonekera pa tsiku limene Mulungu, kudzera mwa Khristu Yesu, adzaweruze+ zinthu zobisika+ za anthu,+ mogwirizana ndi uthenga wabwino umene ndikulengeza.+ 17  Tsopano ngati ndiwe Myuda dzina lokha+ ndipo umadalira chilamulo+ ndi kunyadira Mulungu,+ 18  umadziwa chifuniro chake,+ umakondwera ndi zinthu zapamwamba kwambiri chifukwa chakuti unaphunzitsidwa Chilamulo ndi mawu a pakamwa,+ 19  komanso uli wotsimikiza kuti ndiwe wotsogolera akhungu,+ muuni wa anthu amene ali mu mdima,+ 20  wowongolera anthu opanda nzeru,+ wophunzitsa tiana,+ womvetsa+ zinthu zofunika kuzidziwa ndi choonadi+ zopezeka m’Chilamulo . . . 21  kodi iwe wophunzitsa enawe, sudziphunzitsa wekha?+ Iwe amene umalalikira kuti “Usabe,”+ umabanso kodi?+ 22  Iwe amene umanena kuti “Usachite chigololo,”+ kodi umachitanso chigololo? Iweyo amene umalankhula zosonyeza kuti umanyansidwa ndi mafano, umabanso+ za mu akachisi kodi? 23  Iwe wonyadira chilamulo, kodi umachitiranso Mulungu chipongwe mwa kuphwanya Chilamulo?+ 24  Pakuti “dzina la Mulungu likunyozedwa pakati pa anthu amitundu chifukwa cha inu”+ monga mmene Malemba amanenera. 25  Pajatu mdulidwe+ ndi waphindu pokhapokha ngati iweyo umatsatiradi chilamulo.+ Koma ngati umaphwanya chilamulo, ndiye kuti mdulidwe+ wako ndi wopanda tanthauzo.+ 26  Chotero ngati munthu wosadulidwa+ akusunga miyezo yolungama+ ya m’Chilamulo, kusadulidwa kwake kudzaonedwa ngati kudulidwa, kodi si choncho?+ 27  Munthu amene mwachibadwa ndi wosadulidwa, mwa kutsatira Chilamulo adzakuweruza iwe.+ Adzakuweruza iweyo amene umaphwanya malamulo, amene uli ndi malamulo olembedwa ndiponso ndiwe wodulidwa. 28  Pakuti iye amene ali Myuda kunja kokha si Myuda ayi,+ ndiponso mdulidwe wakunja kokha wochitidwa pathupi, si mdulidwe ayi.+ 29  Koma Myuda ndi amene ali wotero mkati,+ ndipo mdulidwe wake ndi wa mumtima+ wochitidwa ndi mzimu, osati ndi malamulo olembedwa.+ Munthu woteroyo satamandidwa+ ndi anthu koma ndi Mulungu.+

Mawu a M'munsi