Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Aroma 15:1-33

15  Ife olimba tiyenera kunyamula zofooka za osalimba,+ osati kumadzikondweretsa tokha ayi.+  Aliyense wa ife azikondweretsa mnzake pa zinthu zabwino zomulimbikitsa.+  Pakuti ngakhale Khristu sanadzikondweretse yekha,+ koma anachita mmene Malemba amanenera kuti: “Mnyozo wa anthu amene anali kukutonzani wagwa pa ine.”+  Zinthu zonse zimene zinalembedwa+ kalekale zinalembedwa kuti zitilangize.+ Malembawa amatipatsa chiyembekezo+ chifukwa amatithandiza kupirira+ ndiponso amatilimbikitsa.+  Tsopano, Mulungu amene amatipatsa mphamvu kuti tithe kupirira ndiponso amene amatitonthoza, achititse nonsenu kukhala ndi maganizo+ amene Khristu Yesu anali nawo,  kuti nonse pamodzi,+ ndi pakamwa pamodzi, mulemekeze Mulungu, Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu.  Chotero landiranani,+ monga mmene Khristu anatilandirira,+ kuti ulemerero upite kwa Mulungu.  Kunena zoona,+ Khristu anakhaladi mtumiki+ kwa anthu odulidwa+ kuti atsimikizire kuti Mulungu ndi wokhulupirika. Komanso iye anasonyeza kuti malonjezo+ amene Mulunguyo anapatsa makolo awo ndi otsimikizirika,  kuti mitundu ina+ ipereke ulemerero kwa Mulungu chifukwa cha chifundo+ chake, monga mmene Malemba amanenera kuti: “N’chifukwa chake ndidzakuvomerezani poyera pakati pa mitundu. Ndipo ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu.”+ 10  Komanso Malemba amati: “Kondwerani, mitundu inu, pamodzi ndi anthu ake.”+ 11  Ndiponso amati: “Tamandani Yehova, inu mitundu yonse ya anthu, ndipo anthu onse amutamande.”+ 12  Komanso Yesaya anati: “Padzakhala muzu wa Jese,+ ndipo padzatuluka wina wodzalamulira mitundu.+ Mitundu idzayembekezera iye.”+ 13  Mulungu amene amapereka chiyembekezo akudzazeni ndi chimwemwe chonse ndi mtendere wonse chifukwa cha kukhulupirira kwanu, kuti mukhale ndi chiyembekezo chachikulu mwa mphamvu ya mzimu woyera.+ 14  Tsopano abale anga, ine ndine wotsimikiza mtima za inu kuti ndinu okonzeka kuchita zabwino, monga mmene mwakhalira odziwa zinthu zonse.+ Ndine wotsimikizanso mtima kuti mukhoza kulangizana.+ 15  Komabe, ndakulemberani mfundo zina mosapita m’mbali kuti ndikukumbutseninso.+ Ndachita zimenezi chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu kumene Mulungu wandipatsa.+ 16  Ndinapatsidwa kukoma mtima kumeneku kuti ndigwire ntchito yolengeza uthenga wabwino wa Mulungu monga wantchito wa Khristu Yesu, wotumikira anthu a mitundu ina.+ Cholinga changa pogwira ntchito yopatulikayi+ n’chakuti mitundu ina ya anthu iperekedwe+ kwa Mulungu ngati mphatso yovomerezeka+ imene yayeretsedwa ndi mzimu woyera.+ 17  Chotero ndili ndi chifukwa chokhalira wokondwa mwa Khristu Yesu+ pa zinthu zokhudza Mulungu.+ 18  Pakuti sindidzayesa m’pang’ono pomwe kulankhula kanthu ngakhale kamodzi kokha ngati sikanachokere m’zinthu zimene Khristu anachita mwa ine+ kuti mitundu ina ikhale yomvera.+ Anachita zimenezi pogwiritsa ntchito mawu anga+ ndi zochita zanga, 19  ndiponso pogwiritsa ntchito mphamvu yochita zizindikiro ndi zinthu zodabwitsa zolosera zam’tsogolo,+ mwa mphamvu ya mzimu woyera. Chotero ndalalikira mokwanira uthenga wabwino wonena za Khristu+ kuyambira ku Yerusalemu, kuzungulira+ mpaka ku Iluriko. 20  Ndithudi, pochita zimenezi ndinatsimikiza mtima kuti ndisalengeze uthenga wabwino kumene Khristu anatchulidwa kale, ndi cholinga chakuti ndisamange pamaziko+ a munthu wina, 21  koma ndichite monga mmene Malemba amanenera kuti: “Amene chilengezo chonena za iye sichinawapeze adzaona, ndipo amene sanamve adzazindikira.”+ 22  Choncho, pa chifukwa chimenechinso ndinalephera kufika kwa inu.+ 23  Koma tsopano popeza kulibenso gawo limene sindinafikeko m’madera amenewa, ndiponso popeza kuti kwa zaka zambiri ndakhala ndikulakalaka kufika kwanuko,+ 24  ndili ndi chikhulupiriro kuti mulimonse mmene zingakhalire, pa ulendo wanga wa ku Sipaniya+ nthawi ina iliyonse, ndidzaonana nanu. Ndikadzacheza nanu mpaka kukhutira, mudzandiperekeza+ pa ulendo wangawo. 25  Koma tsopano ndatsala pang’ono kupita ku Yerusalemu kukatumikira oyera.+ 26  Abale amene ali ku Makedoniya ndi ku Akaya+ akhala ali ofunitsitsa kupereka+ mphatso kwa oyera osauka a ku Yerusalemu. 27  Ndi zoona kuti achita zimenezo mwa kufuna kwawo, komabe iwo anali ndi ngongole kwa oyerawo. Pakuti ngati anthu a mitundu ina alandirako zinthu zauzimu+ kuchokera kwa oyerawo, ndiye kuti anthu a mitundu inawo ayeneranso kutumikira oyera amenewa mwa kuwapatsa zinthu zofunika pa moyo wawo wa tsiku ndi tsiku.+ 28  Choncho ndikakamaliza zimenezi ndipo ndikakafika bwino ndi zopereka zimenezi+ kwa iwo, ndidzadzera kwanuko popita ku Sipaniya.+ 29  Komanso, ndikudziwa kuti ndikadzafika kwanuko ndidzafika ndi dalitso lonse lochokera kwa Khristu.+ 30  Chotero ndikukudandaulirani abale, kudzera mwa Ambuye wathu Yesu Khristu ndi mwa chikondi cha mzimu,+ kuti mulimbikire limodzi ndi ine popemphera kwa Mulungu za ineyo.+ 31  Tilimbikire kupemphera kuti ndikalanditsidwe+ kwa anthu osakhulupirira a ku Yudeya, ndi kutinso utumiki wanga wa ku Yerusalemu+ ukakhale wolandirika kwa oyerawo,+ 32  kuti ndikadzafika kwa inu ndi chisangalalo mwa kufuna kwa Mulungu, tidzalimbikitsidwe pamodzi.+ 33  Mulungu amene amapatsa mtendere akhale ndi nonsenu.+ Ame.

Mawu a M'munsi