Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Aroma 14:1-23

14  Landirani munthu wokhala ndi zofooka m’chikhulupiriro+ chake, koma osagamula pa zoganiza za mumtima mwake.+  Wina ali ndi chikhulupiriro chakuti angadye china chilichonse,+ koma munthu wofooka amadya zamasamba.  Amene amadya, asanyoze amene sadya,+ ndipo wosadyayo asaweruze amene amadya, popeza ameneyo analandiridwa ndi Mulungu.  Ndiwe ndani kuti uweruze wantchito wapakhomo wa mnzako?+ Ndi udindo wa bwana wake kumuweruza kuti ndi wolakwa kapena wosalakwa.+ Komatu Yehova akhoza kumukomera mtima chifukwa angathe kumuthandiza.+  Wina amaona tsiku lina ngati loposa linzake,+ koma wina amaona tsiku lina mofanana ndi masiku ena onse.+ Choncho munthu aliyense akhale wotsimikiza ndi mtima wonse m’maganizo mwake.  Amene amasunga tsiku amalisungira kulemekeza Yehova. Amene amadya, amadya kuti alemekeze Yehova,+ chifukwa amayamika Mulungu.+ Amene sadya, sadya pofuna kulemekeza Yehova,+ chifukwa nayenso amayamika Mulungu.+  Kunena zoona, palibe aliyense wa ife amene amakhala ndi moyo kuti adzilemekeze yekha,+ ndipo palibe amene amafa kuti adzilemekeze yekha.  Pakuti tikakhala ndi moyo, timakhalira moyo Yehova,*+ ndipo tikafa, timafera Yehova.+ Chotero kaya tikhale ndi moyo kapena tife, ndife a Yehova.+  Ndiye chifukwa chake Khristu anafa n’kukhalanso ndi moyo,+ kuti akhale Ambuye wa akufa+ ndiponso wa amoyo.+ 10  Nanga n’chifukwa chiyani umaweruza m’bale wako?+ Kapenanso n’chifukwa chiyani umanyoza m’bale wako? Pakuti tonse tidzaimirira patsogolo pa mpando woweruzira milandu+ wa Mulungu. 11  Malembatu amati: “‘Pali ine Mulungu wamoyo,’ watero Yehova,+ ‘bondo lililonse lidzandigwadira ine, ndipo lilime lililonse lidzavomereza poyera kwa Mulungu.’”+ 12  Chotero aliyense wa ife adzayankha yekha kwa Mulungu.+ 13  Pa chifukwa chimenechi, tisamaweruzane,+ koma m’malomwake tsimikizani mtima+ kuti simuikira m’bale wanu+ chokhumudwitsa+ kapena chopunthwitsa. 14  Ndikudziwa ndipo ndikukhulupirira mwa Ambuye Yesu kuti palibe chakudya chodetsedwa mwa icho chokha.+ Koma ngati munthu akuona chinachake monga chodetsedwa, kwa iyeyo ndi chodetsedwa.+ 15  Chifukwa ngati m’bale wako akuvutika maganizo chifukwa cha chakudya, ndiye kuti simukuyendanso m’chikondi.+ Musawononge* munthu amene Khristu anamufera+ chifukwa cha zakudya zanu. 16  Choncho musalole kuti anthu akunenereni zoipa pa zabwino zimene mukuchita. 17  Pakuti ufumu wa Mulungu+ si kudya ndi kumwa ayi,+ koma chilungamo,+ mtendere+ ndi chimwemwe+ zobwera ndi mzimu woyera. 18  Chifukwa aliyense wotumikira Khristu motere ali wovomerezeka kwa Mulungu ndipo anthu amakondwera naye.+ 19  Choncho, tiyeni titsatire zinthu zobweretsa mtendere+ ndiponso zolimbikitsana.+ 20  Siyani kuwononga ntchito ya Mulungu chifukwa cha zakudya basi.+ Zoonadi, zinthu zonse ndi zoyera, koma munthu amene amadya ngakhale pamene akukhumudwitsa ena, amalakwa.+ 21  Ndi bwino kusadya nyama kapena kusamwa vinyo kapena kusachita kalikonse kamene kamakhumudwitsa m’bale wako.+ 22  Chikhulupiriro chimene uli nacho, khala nacho pakati pa iweyo ndi Mulungu.+ Wodala munthu amene sakudziika pa chiweruzo ndi zinthu zimene wasankha kuchita. 23  Koma ngati akudya ndipo akukayikira, ameneyo watsutsidwa kale,+ chifukwa sakudya mwa chikhulupiriro. Ndithu, chilichonse chochitidwa mosemphana ndi chikhulupiriro ndi tchimo.+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 2.
Kutanthauza kuwononga chikhulupiriro kapena chiyembekezo cha moyo wosatha wa m’tsogolo.