Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Aroma 11:1-36

11  Ndiye ndifunse kuti, kodi Mulungu anakana anthu ake?+ Ayi ndithu! Paja inenso ndine Mwisiraeli,+ wa mbewu ya Abulahamu, wa fuko la Benjamini.+  Mulungu sanakane anthu ake amene anali oyambirira kuwavomereza.+ Kodi ndithu simukudziwa kuti Lemba limati chiyani za Eliya, pamene anali kuchonderera Mulungu motsutsa Aisiraeli?+ Limati:  “Yehova, iwo apha aneneri anu, agumula maguwa anu ansembe, moti ine ndatsala ndekhandekha. Tsopano akufunafuna moyo wanga.”+  Koma kodi mawu a Mulungu+ anati chiyani kwa iyeyo? Anati: “Ndadzisungira anthu 7,000, amene sanagwadire Baala.”+  Chotero, pa nthawi ino alipo ena ochepa+ amene anasankhidwa+ mwa kukoma mtima kwakukulu.  Ndiyetu ngati anasankhidwa mwa kukoma mtima kwakukulu,+ sanasankhidwe chifukwa cha ntchito zawo ayi.+ Zitati zitero, kukoma mtima kumeneko sikungakhalenso kukoma mtima kwakukulu.+  Ndiye zili bwanji pamenepa? Chimene Aisiraeli akuchifunitsitsa sanachipeze,+ koma anthu osankhidwa+ ndi amene anachipeza. Enawo anaumitsa mitima yawo+  monga mmene Malemba amanenera kuti: “Mulungu wawapatsa mzimu wa tulo tatikulu,+ maso osaona ndi makutu osatha kumva, kufikira lero.”+  Ndiponso Davide anati: “Tebulo lawo likhale msampha, mbuna, chopunthwitsa ndi chilango kwa iwo.+ 10  Maso awo achite mdima kuti asaone, ndipo weramitsani msana wawo nthawi zonse.”+ 11  Ndiyeno ndifunse, Kodi anapunthwa mpaka kugweratu?+ Ayi! Koma chifukwa cha kulakwa kwawo+ pali chipulumutso kwa anthu a mitundu ina,+ kuti olakwawo achite nsanje.+ 12  Chotero ngati kulakwa kwawo kukutanthauza chuma ku dziko, ndipo kuchepa kwawo kukutanthauza chuma kwa anthu a mitundu ina,+ bwanji nanga za chiwerengero chawo chokwanira?+ Chidzatanthauzatu zazikulu kuposa pamenepo! 13  Tsopano ndikulankhula kwa inu ochokera m’mitundu ina. Malinga n’kuti ndine mtumwi+ weniweni wotumidwa kwa mitundu ina,+ ndimalemekeza+ utumiki wanga,+ 14  kuti mwina ndingapangitse anthu a mtundu wanga kuchita nsanje ndi kupulumutsapo+ ena a iwo.+ 15  Chifukwa ngati dziko layanjidwa ndi Mulungu chifukwa chakuti iwo anatayidwa,+ ndiye kuti akadzalandiridwa+ zidzatanthauza moyo kuchokera ku imfa. 16  Ndiponso, ngati mbali ya mtanda imene yadyedwa monga chipatso choyambirira+ ili yoyera, ndiye kuti mtanda wonse ndi woyeranso. Ngati muzu uli woyera,+ ndiye kuti nthambi nazonso ndi zoyera. 17  Ngati nthambi zina zinadulidwa, koma iwe ngakhale kuti ndiwe nthambi ya mtengo wa maolivi wam’tchire, unalumikizidwa pakati pa nthambi zotsala+ ndipo unayamba kugawana nawo muzu wamafuta+ wa mtengo wa maoliviwo,+ 18  usakondwere monyoza nthambi zimene zinadulidwazo. Koma ngati ukunyoza nthambizo,+ kumbukira kuti si iwe amene ukuchirikiza muzu,+ koma muzu ndi umene ukuchirikiza iweyo.+ 19  Komatu tsopano unganene kuti: “Nthambi zina zinadulidwa+ kuti alumikizepo ine.”+ 20  N’zoonadi! Iwo anadulidwa chifukwa chakuti analibe chikhulupiriro,+ koma iweyo waimirira chifukwa cha chikhulupiriro.+ Taya maganizo odzikuzawo,+ koma khala ndi mantha.+ 21  Pakuti ngati Mulungu sanalekerere nthambi zachilengedwe, sadzakulekereranso iweyo.+ 22  Choncho taona kukoma mtima+ komanso kusalekerera+ kwa Mulungu. Amene anagwa anaona kusalekerera+ kwake, koma iweyo ukuona kukoma mtima kwa Mulungu, malinga ngati ukukhalabe+ m’kukoma mtima kwake. Apo ayi, iwenso udzadulidwa.+ 23  Iwonso ngati angayambe kukhala ndi chikhulupiriro, adzalumikizidwa kumtengowo,+ pakuti Mulungu akhoza kuwalumikizanso. 24  Ngati iweyo unadulidwa kumtengo wa maolivi umene mwachilengedwe umamera m’tchire, ndipo mosemphana ndi chilengedwe, unalumikizidwa+ kumtengo wa maolivi wolimidwa, kodi si kwapafupi kulumikiza nthambi izi kumtengo wawo umene zinadulidwako?+ 25  Pakuti sindikufuna kuti mukhale osadziwa abale za chinsinsi chopatulika+ chimenechi, kuopera kuti mungadzione ngati ochenjera. Chinsinsi chopatulikacho n’chakuti ena mu Isiraeli aumitsa mitima yawo+ mpaka chiwerengero chonse+ cha anthu ochokera m’mitundu ina chitakwanira.+ 26  Mwa njira imeneyi, Aisiraeli onse+ adzapulumuka. Izi zikugwirizana ndi zimene Malemba amanena kuti: “Wolanditsa adzachokera m’Ziyoni+ ndi kuchotsera Yakobo zochita zonse zosalemekeza Mulungu.+ 27  Limeneli lidzakhala pangano langa ndi iwo,+ pamene ndidzawachotsera machimo awo.”+ 28  Zoonadi, pa nkhani ya uthenga wabwino iwo ndi adani a Mulungu, ndipo zimenezi zapindulitsa inu.+ Koma kunena za kusankha kwa Mulungu, iwo ndi okondedwa ake chifukwa cha makolo awo oyambirira.+ 29  Mulungu sadzadandaula+ chifukwa cha mphatso zake ndiponso chifukwa chakuti anawaitana. 30  Pakuti monga mmene inuyo munalili osamvera+ Mulungu koma tsopano mwasonyezedwa chifundo+ chifukwa cha kusamvera kwawo,+ 31  iwowa tsopano akhala osamvera, zimene zapangitsa kuti inuyo musonyezedwe chifundo,+ kuti iwonso tsopano asonyezedwe chifundo. 32  Popeza Mulungu walola onse kuti akhale akaidi a kusamvera,+ kuti onsewo awasonyeze chifundo.+ 33  Ndithudi, madalitso amene Mulungu amapereka ndi ochuluka kwambiri.+ Nzeru+ zake n’zozama, ndiponso iye ndi wodziwa zinthu kwambiri.+ Ziweruzo zake ndi zosasanthulika,+ ndipo ndani angatulukire njira zake? 34  Pakuti “ndani akudziwa maganizo a Yehova,+ kapena ndani angakhale phungu wake?”+ 35  Kapenanso, “Ndani anayamba kumupatsa kanthu, kuti amubwezere?”+ 36  Chifukwa zinthu zonse zimachokera kwa iye ndipo iye ndi amene anazipanga ndiponso ndi zake.+ Ulemerero ukhale wake kwamuyaya.+ Ame.

Mawu a M'munsi