Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Aroma 10:1-21

10  Ndithu abale, chimene ndikufunitsitsa mumtima mwanga ndiponso pembedzero langa kwa Mulungu ndi lakuti Aisiraeli apulumutsidwe.+  Pakuti ndikuwachitira umboni kuti ndi odzipereka+ potumikira Mulungu, koma samudziwa molondola.+  Ndipo posadziwa chilungamo cha Mulungu,+ iwo sanagonjere chilungamocho+ koma anayesetsa kukhazikitsa chawochawo.+  Pakuti Khristu ndiye kutha kwa Chilamulo,+ kuti aliyense wokhulupirira akhale wolungama.+  Pajatu Mose analemba kuti munthu wochita chilungamo cha m’Chilamulo adzakhala ndi moyo chifukwa cha chilungamo chimenecho.+  Koma za chilungamo chimene chimabwera chifukwa cha chikhulupiriro, Malemba amati: “Mumtima mwako usanene kuti,+ ‘Kodi ndani adzakwera kumwamba?’+ kuti akatsitse Khristu.+  Kapena, ‘Kodi ndani adzatsikira kuphompho?’+ kuti akaukitse Khristu kwa akufa.”+  Koma kodi Lemba limati chiyani? Limati: “Mawu a chilamulowo ali pafupi ndi iwe, ali m’kamwa mwako ndi mumtima mwako,”+ amenewa ndi “mawu”+ a chikhulupiriro, amene tikulalikira.+  Pakuti ngati ukulengeza kwa anthu ‘mawu amene ali m’kamwa mwakowo,’+ akuti Yesu ndiye Ambuye,+ ndipo mumtima mwako ukukhulupirira kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa,+ udzapulumuka.+ 10  Munthu amakhala ndi chikhulupiriro mumtima mwake+ kuti akhale wolungama, koma ndi pakamwa pake amalengeza poyera+ chikhulupiriro chake kuti apulumuke. 11  Paja Lemba limati: “Palibe wokhulupirira iye,+ amene adzakhumudwe.”+ 12  Palibe kusiyana pakati pa Myuda ndi Mgiriki,+ popeza kwa onsewo Ambuye ndi mmodzi, amene amapereka mowolowa manja+ kwa onse oitana pa dzina lake. 13  Pakuti “aliyense amene adzaitana pa dzina la Yehova* adzapulumuka.”+ 14  Komabe, kodi angaitane bwanji munthu amene samukhulupirira?+ Angakhulupirire bwanji munthu amene sanamvepo za iye? Angamve bwanji za iye popanda wina kulalikira?+ 15  Ndipo angalalikire bwanji ngati sanatumidwe?+ Zili monga muja Malemba amanenera kuti: “Mapazi a anthu olengeza uthenga wabwino wa zinthu zabwino, ndi okongola kwabasi!”+ 16  Ngakhale zili choncho, si onse amene analabadira uthenga wabwino.+ Pakuti Yesaya anati: “Yehova, kodi ndani wakhulupirira zimene anamva kwa ife?”+ 17  Chotero munthu amakhala ndi chikhulupiriro chifukwa cha zimene wamva.+ Ndipo zimene wamvazo zimachokera m’mawu onena za Khristu.+ 18  Koma ndifunsebe kuti, Kodi kumva sanamve? Pajatu “liwu lawo linamveka padziko lonse lapansi,+ ndipo mawu awo anamveka kumalekezero a dziko lapansi kumene kuli anthu.”+ 19  Komabe ndifunse kuti, Kodi si zoona kuti Aisiraeli anadziwa?+ Choyamba Mose anati: “Ndidzakuchititsani nsanje kudzera mwa anthu omwe si mtundu. Ndidzaputa mkwiyo wanu woopsa kudzera mwa mtundu wopusa.”+ 20  Koma Yesaya analankhula molimba mtima kwambiri kuti: “Anthu amene anandipeza ndi amene sanali kundifunafuna.+ Ndinaonekera kwa anthu amene sanafunse za ine kuti andipeze.”+ 21  Koma za Aisiraeli iye anati: “Ndatambasula manja anga tsiku lonse kwa anthu osamva+ komanso otsutsa.”+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 2.