Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Amosi 7:1-17

7  Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, anandionetsa masomphenya awa: Ndinamuona akutumiza dzombe, anthu atatsala pang’ono kubzala mbewu zomaliza.+ Nthawi imeneyi inali yobzala mbewu zomaliza, anthu atamweta udzu wopita kwa mfumu.  Ndiyeno dzombelo litamaliza kudya zomera zonse za m’dziko, ine ndinati: “Inu Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, chonde khululukani.+ Kodi Yakobo adzapulumuka bwanji, pakuti ndi wamng’ono?”+  Yehova anamva chisoni ndipo Yehova anati, “Zimenezi sizidzachitika.”  Kenako, Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, anandionetsanso masomphenya awa: Ndinaona Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, akuuza anthu ake kuti alimbane naye pogwiritsira ntchito moto.+ Motowo unaumitsa madzi akuya ndiponso unawononga kachigawo ka dziko.  Ndiyeno ine ndinati: “Inu Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, chonde musatero. Kodi Yakobo adzapulumuka bwanji, pakuti ndi wamng’ono?”+  Pamenepo Yehova anamva chisoni ndipo Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, anati, “Zimenezinso sizidzachitika.”  Kenako, iye anandionetsanso masomphenya awa: Ndinaona Yehova ataima pamwamba pa khoma limene linamangidwa pogwiritsa ntchito chingwe chowongolera,+ ndipo iye anali ndi chingwe chowongolera m’dzanja lake.  Ndiyeno Yehova anandifunsa kuti: “Kodi ukuona chiyani Amosi?” Ndinamuyankha kuti: “Ndikuona chingwe chowongolera.” Pamenepo Yehova anati: “Ine ndiika chingwe chowongolera pakati pa anthu anga Aisiraeli,+ ndipo sindidzawakhululukiranso.+  Malo okwezeka a Isaki adzawonongedwa, ndipo malo opatulika a Isiraeli nawonso adzasakazidwa.+ Ine ndidzaukira nyumba ya Yerobowamu* ndi lupanga.” 10  Ndiyeno Amaziya wansembe wa ku Beteli, anatumiza uthenga kwa Yerobowamu mfumu ya Isiraeli kuti: “Amosi wakukonzerani chiwembu mkati mwenimweni mwa Isiraeli,+ ndipo anthu atopa nawo mawu akewo.+ 11  Amosi wanena kuti, ‘Yerobowamu adzaphedwa ndi lupanga, ndipo mosalephera Isiraeli adzagwidwa m’dziko lake ndi kutengedwa kupita ku ukapolo.’”+ 12  Ndiyeno Amaziya anauza Amosi kuti: “Iwe wamasomphenya,+ choka, thawira kudziko la Yuda, ndipo kumeneko uzikadya mkate ndi kunenera. 13  Koma usapitirize kunenera ku Beteli kuno,+ pakuti ndi malo opatulika a mfumu, ndiponso Beteli ndi nyumba ya ufumu uno.” 14  Pamenepo Amosi anayankha Amaziya kuti: “Ine sindinali mneneri kapena mwana wa mneneri, koma ndinali m’busa+ ndiponso woboola nkhuyu. 15  Koma Yehova ananditenga kumene ndinali kuweta nkhosa, ndipo Yehova anandiuza kuti, ‘Pita ukanenere kwa anthu anga Aisiraeli.’+ 16  Tsopano mvera mawu a Yehova, ‘Kodi iwe ukundiuza kuti: “Usanenere zinthu zoipa zokhudza Isiraeli,+ ndipo usatchule mawu alionse oipa okhudza nyumba ya Isaki”? 17  Yehova wanena kuti: “Mkazi wako adzakhala hule mumzindawu.+ Ana ako aamuna ndi ana ako aakazi adzaphedwa ndi lupanga. Anthu adzagawana dziko lako mochita kuyeza ndi chingwe, ndipo iweyo udzafera m’dziko lodetsedwa. Ndithudi, Isiraeli adzagwidwa m’dziko lake ndi kutengedwa kupita ku ukapolo.”’”

Mawu a M'munsi

Ameneyu ndi Yerobowamu Wachiwiri, mwana wa Yowasi (Yehowasi). Onani Amo 1:1.