Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Amosi 6:1-14

6  “Tsoka kwa anthu amene akukhala mwamtendere+ mu Ziyoni ndiponso anthu amene akumva kuti ndi otetezeka m’phiri la Samariya. Iwo ndiwo anthu olemekezeka a mtundu wotchuka pakati pa mitundu ina, ndipo nyumba yonse ya Isiraeli imabwera kwa anthu amenewa.  Pitani mukaone ku Kaline ndipo kuchokera kumeneko mukapite ku Hamati+ kumene kuli anthu ambiri, kenako mukapite ku Gati+ wa Afilisiti. Kodi mizinda imeneyi imaposa maufumu anu awiriwa?* Kapena kodi malo awo ndi aakulu kuposa malo anu?+  Kodi inu simukufuna kuganizira za tsiku latsoka?+ Kodi mukufuna kuti chiwawa chizichitika pakati panu?+  Anthu inu mukugona pamipando ya minyanga ya njovu+ ndi kudziwongola pamabedi, ndiponso mukudya nyama ya ana a nkhosa ndi ana amphongo onenepa a ng’ombe zanu.+  Inu mukupeka nyimbo zoti muziimba ndi zipangizo za zingwe,+ ndipo mofanana ndi Davide, mukupanga zipangizo zoimbira.+  Inu mukumwera vinyo m’makapu akuluakulu+ ndipo mukudzola mafuta apamwamba kwambiri+ komanso simunamve ululu pamene tsoka linagwera Yosefe.+  “Anthu amenewa adzakhala oyambirira kupita ku ukapolo,+ ndipo phwando laphokoso la anthu ogona modziwongola pamabedi lidzatha.  “Yehova, Mulungu wa makamu, wanena kuti: ‘Ine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, ndalumbira pa dzina langa kuti,+ “Ndikunyasidwa ndiponso ndikudana ndi kunyada kwa Yakobo+ ndi nsanja zake zokhalamo,+ chotero ndidzapereka mzindawu ndi zinthu zake zonse kwa adani ake.+  Ngati pangadzatsale anthu 10 m’nyumba imodzi, nawonso adzafa.+ 10  Ndipo m’bale wa bambo ake a mwamuna mmodzi mwa amuna ophedwawo adzawatulutsa ndi kuwatentha mmodzi ndi mmodzi kuti atulutse mafupa onse m’nyumbamo.+ Ndiyeno adzafunsa aliyense amene ali m’chipinda chamkatikati kuti, ‘Kodi muli anthu enanso mmenemo?’ Pamenepo amene ali m’chipindayo adzayankha kuti, ‘Mulibe!’ Kenako adzamuuza kuti, ‘Khala chete! Pakuti ino si nthawi yotchula dzina la Yehova.’”+ 11  “‘Tsopano Yehova akalamula,+ nyumba zikuluzikulu zigwetsedwa n’kusanduka mulu wa dothi ndipo nyumba zing’onozing’ono zisanduka zibuma zokhazokha.+ 12  “‘Kodi mahatchi angathamange pathanthwe, kapena kodi munthu angalime pathanthwe ndi ng’ombe? Anthu inu mwakana chilungamo,+ choncho mwachititsa moyo wa anthu kukhala wowawa. 13  Inu mukusangalala ndi chinthu chimene palibe+ ndipo mukunena kuti: “Tadzipezera tokha mphamvu.”’*+ 14  Tsopano Yehova, Mulungu wa makamu wanena kuti, ‘Inu a m’nyumba ya Isiraeli, ine ndikukudzutsirani mtundu wa anthu+ umene udzakuponderezani kuyambira kumalire ndi Hamati+ mpaka kuchigwa cha Araba.’”

Mawu a M'munsi

Amenewa ndi maufumu a Yuda ndi Isiraeli.
Mawu ake enieni, “Tadzitengera nyanga.”