Amosi 4:1-13

4  “Tamverani mawu awa, inu ng’ombe zazikazi za ku Basana,+ zokhala m’phiri la Samariya,+ inu amene mukuchitira zachinyengo anthu onyozeka,+ amene mukuphwanya anthu osauka ndipo mukuuza ambuye anu kuti, ‘Tipatseni chakumwa kuti timwe!’  Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, walumbira mwa kuyera kwake+ kuti, ‘“Taonani! Masiku adzafika pamene mudzanyamulidwa ndi ngowe zokolera nyama ndipo otsala anu adzawakola ndi mbedza za nsomba.+  Aliyense wa inu adzatulukira pachibowo cha mpanda+ chimene ali nacho pafupi ndipo mudzaponyedwa kunja, ku Harimoni,” watero Yehova.’  “‘Bwerani ku Beteli anthu inu kuti mudzachite zolakwa.+ Muzichita zolakwa mobwerezabwereza ku Giligala+ ndipo muzibweretsa nsembe zanu m’mawa. Pa tsiku lachitatu, muzibweretsa chakhumi* chanu.+  Perekani nsembe zoyamikira zautsi kuchokera pa zinthu zokhala ndi chofufumitsa+ ndipo lengezani ndi kufalitsa za nsembe zaufulu+ pakuti ndi zimene mukukonda, inu ana a Isiraeli,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.  “‘Komanso ine ndinakupatsani njala*+ m’mizinda yanu yonse ndipo munali kusowa chakudya m’malo anu onse okhala,+ koma simunabwerere kwa ine,’+ watero Yehova.  “‘Ine ndinakumanani mvula kutatsala miyezi itatu kuti mukolole.+ Ndinagwetsa mvula pamzinda umodzi koma pamzinda wina sindinagwetsepo mvula. Mvula inagwa pamunda umodzi koma pamunda wina sindinagwetsepo mvula ndipo unauma.+  Anthu a m’mizinda iwiri kapena itatu anayenda movutikira kupita kumzinda wina kuti akamwe madzi+ ndipo ludzu lawo silinathe, koma simunabwerere kwa ine,’+ watero Yehova.  “‘Ndinawononga mbewu zanu ndi mphepo yotentha komanso ndi matenda a chuku.+ Munachulukitsa minda yanu ya mpesa ndi ya mbewu zina ndipo mbozi zinawononga mitengo yanu ya mkuyu ndi ya maolivi,+ komabe inu simunabwerere kwa ine,’+ watero Yehova. 10  “‘Anthu inu ndinakutumizirani mliri wofanana ndi umene unachitika ku Iguputo.+ Ndinapha anyamata anu ndi lupanga+ ndipo mahatchi anu analandidwa.+ Ndinachititsa fungo lonunkha lotuluka m’misasa yanu kufika kumphuno zanu,+ koma inu simunabwerere kwa ine,’+ watero Yehova. 11  “‘Ndinabweretsa chiwonongeko pakati pa anthu inu chofanana ndi chimene Mulungu anabweretsa pa Sodomu ndi Gomora.+ Pamenepo inu munakhala ngati chitsa cholanditsidwa pamoto+ koma simunabwerere kwa ine,’+ watero Yehova. 12  “Tsopano zinthu zofanana ndi zimenezi ndi zimene ndidzakuchitira, iwe Isiraeli. Ndipo chifukwa chakuti ndidzakuchitira zimenezi, konzekera kukumana ndi Mulungu wako,+ iwe Isiraeli. 13  Taona! Yehova Mulungu wa makamu ndilo dzina+ la amene anapanga mapiri,+ analenga mphepo,+ amene amafotokozera munthu zimene akuganiza,+ amene amachititsa kuwala kwa m’bandakucha kukhala mdima+ ndiponso amene amaponda malo okwezeka a dziko lapansi.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “gawo limodzi mwa magawo 10.”
Mawu ake enieni, “ndinakupatsani mano oyera.”