Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Akolose 3:1-25

3  Komabe, ngati munaukitsidwa+ limodzi ndi Khristu, pitirizani kufuna zinthu zakumwamba,+ kumene Khristu wakhala kudzanja lamanja la Mulungu.+  Ikani maganizo anu pa zinthu zakumwamba,+ osati pa zinthu zapadziko.+  Pakuti munafa,+ ndipo moyo+ wanu wabisidwa mwa Khristu mogwirizana+ ndi Mulungu.  Khristuyo, amene ndiye moyo wathu,+ akadzaonetsedwa,+ inunso mudzaonetsedwa limodzi naye mu ulemerero.+  Choncho chititsani ziwalo za thupi+ lanu padziko lapansi kukhala zakufa+ ku dama, zinthu zodetsa, chilakolako cha kugonana,+ chikhumbo choipa, ndi kusirira kwa nsanje,+ kumene ndiko kulambira mafano.  Chifukwa cha zinthu zimenezi, mkwiyo wa Mulungu ukubwera.+  Inunso munayendapo m’zinthu zimenezi, pamene munali kukhalira kuchita zomwezo.+  Koma tsopano zonsezo muzitaye kutali ndi inu.+ Mutaye mkwiyo, kupsa mtima, kuipa, ndi mawu achipongwe,+ ndipo pakamwa panu pasatuluke nkhani zotukwana.+  Musamanamizane.+ Vulani umunthu+ wakale pamodzi ndi ntchito zake, 10  ndipo muvale umunthu watsopano+ umene Mulungu amapereka, kutanthauza kuti mwa kudziwa zinthu molondola, muchititse umunthu wanu kukhala watsopano mogwirizana ndi chifaniziro+ cha Mulungu. 11  Mukatero, sipadzakhala Mgiriki kapena Myuda, kudulidwa kapena kusadulidwa, mlendo, Msukuti, kapolo, kapena mfulu,+ koma Khristu ndiye zinthu zonse ndipo ali mwa onse.+ 12  Chotero monga ochita kusankhidwa ndi Mulungu,+ oyera ndi okondedwa, valani chifundo+ chachikulu, kukoma mtima, kudzichepetsa,+ kufatsa,+ ndi kuleza mtima.+ 13  Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse,+ ngati wina ali ndi chifukwa chodandaulira+ za mnzake. Monga Yehova* anakukhululukirani+ ndi mtima wonse, inunso teroni. 14  Koma kuwonjezera pa zonsezi, valani chikondi,+ pakuti chimagwirizanitsa anthu mwamphamvu+ kwambiri kuposa chinthu china chilichonse. 15  Komanso, mtendere+ wa Khristu ulamulire m’mitima+ yanu, popeza munaitanidwa ku mtenderewo monga ziwalo za thupi limodzi.+ Ndiponso, sonyezani kuti ndinu oyamikira. 16  Mawu a Khristu akhazikike mwa inu ndipo akupatseni nzeru zonse.+ Pitirizani kuphunzitsana+ ndi kulangizana mwa masalimo,+ nyimbo zotamanda Mulungu, ndi nyimbo zauzimu+ zogwira mtima. Pitirizani kuimbira Yehova+ m’mitima yanu. 17  Ndipo chilichonse chimene mukuchita m’mawu kapena mu ntchito,+ muzichita zonse m’dzina la Ambuye Yesu,+ ndipo muziyamika+ Mulungu Atate kudzera mwa iye. 18  Inu akazi, muzigonjera+ amuna anu, pakuti zimenezi ndiye zoyenera kwa anthu otsatira Ambuye. 19  Inu amuna, musaleke kukonda akazi+ anu ndipo musamawapsere mtima kwambiri.+ 20  Ananu, muzimvera+ makolo anu pa zinthu zonse, pakuti kuchita zimenezi kumakondweretsa Ambuye. 21  Inu abambo, musamakwiyitse ana+ anu, kuti angakhale okhumudwa. 22  Inu akapolo, muzimvera ambuye anu a padziko lapansi+ pa zinthu zonse, osati mwachiphamaso ngati ofuna kukondweretsa+ anthu, koma moona mtima ndiponso moopa Yehova.+ 23  Chilichonse chimene mukuchita, muzichichita ndi moyo wanu wonse+ ngati kuti mukuchitira Yehova,+ osati anthu, 24  chifukwa mukudziwa kuti mudzalandira cholowa+ kuchokera kwa Yehova+ monga mphoto yanu. Tumikirani Ambuye wanu, Khristu, monga akapolo.+ 25  Ndithudi, amene akuchita zolakwa adzalandiranso+ zolakwa zake zimene akuchitazo, chifukwa Mulungu sakondera.+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 2.