Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Akolose 2:1-23

2  Ndikufuna kuti mudziwe nkhondo+ yaikulu imene ndikumenya chifukwa cha inuyo ndi anthu a ku Laodikaya,+ ndi onse amene sanandionepo maso ndi maso.  Ndikufuna kuti mtima wa aliyense ulimbikitsidwe,+ ndiponso kuti onse akhale ogwirizana m’chikondi.+ Achite zimenezi kuti onse alandire chuma chimene chimabwera chifukwa chomvetsa bwino zinthu,+ popanda kukayikira chilichonse, ndiponso chifukwa chodziwa molondola chinsinsi chopatulika cha Mulungu, chomwe ndi Khristu.+  Chuma chonse chokhudzana ndi nzeru ndiponso kudziwa zinthu+ chinabisidwa mosamala mwa iye.  Ndikunena zimenezi kuti munthu aliyense asakunyengeni ndi mfundo zokopa.+  Popeza ngakhale kuti sindili kumeneko, ndili nanu ndithu mumzimu.+ Ndine wosangalala poona kuti mumachita zinthu mwadongosolo,+ komanso kuti muli ndi chikhulupiriro+ cholimba mwa Khristu.  Tsopano popeza mwalandira Khristu Yesu Ambuye wathu, yendanibe mogwirizana+ naye.  Khalanibe ozikika mozama+ mwa iye, ndipo monga mmene munaphunzitsidwira, pitirizani kukula+ pamene mukumuona iye monga maziko anu, ndi kukhazikika m’chikhulupiriro.+ Sefukiranibe ndi chikhulupiriro popereka mapemphero oyamikira.+  Samalani: mwina wina angakugwireni+ ngati nyama, mwa nzeru za anthu+ ndi chinyengo chopanda pake,+ malinga ndi miyambo ya anthu, malinganso ndi mfundo zimene zili maziko a moyo wa m’dzikoli,+ osati malinga ndi Khristu,    chifukwa iye ndi wodzaza bwino kwambiri+ ndi makhalidwe+ a Mulungu.+ 10  Kudzera mwa iyeyo, inu simukusowa kalikonse. Iye ndiye mwini ulamuliro wonse ndi mphamvu zonse.+ 11  Popeza muli naye pa ubwenzi,+ mwadulidwa,+ osati ndi manja a anthu koma mwa kuvula thupi lauchimo,+ chifukwa mdulidwe wa atumiki a Khristu umakhala wotero. 12  Zinatero popeza munakwiriridwa naye limodzi mwa kubatizidwa ubatizo wofanana ndi wake,+ ndipo chifukwa choti muli naye pa ubwenzi, munaukitsidwa+ naye limodzi kudzera m’chikhulupiriro chimene muli nacho+ mu zinthu zimene zinachitika chifukwa cha mphamvu+ ya Mulungu, amene anamuukitsa kwa akufa.+ 13  Ndiponso, ngakhale kuti munali akufa m’machimo anu ndipo munali osadulidwa, Mulungu anakupatsani moyo kuti mukhale ogwirizana ndi Khristu,+ ndipo anatikhululukira machimo athu onse motikomera mtima.+ 14  Anafafanizanso+ chikalata cholembedwa ndi manja,+ chokhala ndi malamulo+ operekedwa monga malangizo, chimene chinali kutitsutsa.+ Ndipo Iye wachichotsa mwa kuchikhomera+ pamtengo wozunzikirapo.*+ 15  Pogwiritsa ntchito mtengo wozunzikirapowo, iye anavula maboma ndi olamulira n’kuwasiya osavala,+ ndipo anawaonetsa poyera pamaso pa anthu onse kuti aliyense aone kuti wawagonjetsa,+ n’kumayenda nawo ngati akaidi.+ 16  Choncho munthu asakuweruzeni+ pa nkhani ya kudya ndi kumwa+ kapena chikondwerero chinachake,+ kapenanso kusunga tsiku lokhala mwezi,+ ngakhalenso kusunga sabata,+ 17  pakuti zinthu zimenezo ndi mthunzi+ wa zimene zinali kubwera, koma zenizeni+ zake zili mwa Khristu.+ 18  Musalole kuti munthu aliyense amene amasangalala ndi kudzichepetsa kwachinyengo komanso ndi kulambira angelo akumanitseni+ mphotoyo.+ Anthu oterowo amaumirira zinthu zimene aona ndipo maganizo awo ochimwa amawachititsa kudzitukumula popanda chifukwa chomveka. 19  Amatero koma osagwira mwamphamvu amene ali mutu,+ amene kuchokera kwa iye, thupi lonselo, limene limapeza zonse zimene limafunikira ndipo ndi lolumikizika bwino+ mwa mfundo zake ndi minyewa, limakulabe mothandizidwa ndi Mulungu.+ 20  Ngati munafa+ limodzi ndi Khristu pa mfundo zimene ndi maziko+ a moyo wa m’dzikoli,+ n’chifukwa chiyani mukupitiriza kukhala ngati kuti mudakali mbali ya dzikoli, pogonjeranso malamulo+ akuti: 21  “Usatenge ichi, kapena usalawe ichi,+ kapena usakhudze ichi?”+ 22  Zinthu zimenezi zidzawonongedwa mwa kuzigwiritsa ntchito ndipo malamulo amenewa ndi ziphunzitso za anthu basi.+ 23  Ndithudi, zinthu zimenezo zimaonekera pa kulambira kochita kudzipangira, podzichepetsa mwachinyengo komanso pozunza thupi,+ ndipo zimaonekadi ngati zanzeru, koma n’zosathandiza kwa munthu polimbana ndi zilakolako za thupi.+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 9.