Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Akolose 1:1-29

1  Ine Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwa kufuna kwa Mulungu,+ pamene ndili limodzi ndi Timoteyo+ m’bale wathu,  ndikulembera oyera ndi abale okhulupirika amene ali ogwirizana+ ndi Khristu ku Kolose, kuti: Kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate wathu zikhale nanu.+  Nthawi zonse tikamakupemphererani,+ timayamika+ Mulungu, Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu.  Timatero chifukwa tinamva za chikhulupiriro chanu mwa Khristu Yesu, ndi chikondi chanu pa oyera onse,+  chimene muli nacho chifukwa cha chiyembekezo+ chodzalandira zimene akusungirani kumwamba.+ Munamva za chiyembekezo chimenechi pamene choonadi cha uthenga wabwino chinalengezedwa kwa inu.+  Uthenga wabwinowu unafika kwa inu popeza ukubala zipatso+ ndipo ukuwonjezeka+ m’dziko lonse.+ Ukuteronso pakati panu, kuyambira tsiku limene munamva ndi kudziwa molondola za kukoma mtima kwakukulu+ kwa Mulungu monga mmene kulilidi.+  Zimenezi mwaziphunzira kwa Epafura,+ kapolo mnzathu wokondedwa, amene ndi mtumiki wokhulupirika wa Khristu m’malo mwa ife.  Iye ndi amenenso anatidziwitsa za chikondi chanu+ chimene munachikulitsa mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu.  N’chifukwa chake ifenso, kuyambira tsiku limene tinamva zimenezo, sitinaleke kukupemphererani.+ Takhala tikupemphanso kuti mukhale odziwa molondola+ chifuniro chake, ndiponso kuti mukhale ndi nzeru+ zonse komanso muzimvetsetsa zinthu zauzimu.+   10  Tikupemphereranso kuti muziyenda mogwirizana ndi zimene Yehova+ amafuna,+ kuti muzimukondweretsa pa chilichonse,+ pamene mukupitiriza kubala zipatso m’ntchito iliyonse yabwino, ndi kuwonjezera kumudziwa Mulungu molondola.+ 11  Tikupemphereranso kuti mulandire mphamvu zazikulu chifukwa cha mphamvu zake zaulemerero,+ kuti muthe kupirira+ zinthu zonse ndi kukhala oleza mtima ndiponso achimwemwe, 12  komanso muziyamika Atate, amene anakuyeneretsani kuti mupatsidweko gawo pa cholowa+ cha oyerawo,+ amene ali m’kuwala.+ 13  Iye anatilanditsa ku ulamuliro+ wa mdima, n’kutisamutsira+ mu ufumu+ wa Mwana wake wokondedwa.+ 14  Mwa Mwana wakeyo, tinamasulidwa ndi dipo,* kutanthauza kuti machimo athu anakhululukidwa.+ 15  Iye ndiye chifaniziro+ cha Mulungu wosaonekayo,+ woyamba kubadwa+ wa chilengedwe chonse, 16  chifukwa kudzera mwa iye+ zinthu zina zonse zinalengedwa, zakumwamba ndi zapadziko lapansi. Inde, zinthu zooneka ndi zinthu zosaoneka, kaya ndi mipando yachifumu, kapena ambuye, kapena maboma, kapena maulamuliro.+ Zinthu zina zonse zinalengedwa kudzera mwa iye,+ ndiponso chifukwa cha iye. 17  Ndiponso, iye ali patsogolo pa zinthu zina zonse,+ ndipo zinthu zina zonse zinakhalapo kudzera mwa iye.+ 18  Iye ndiyenso mutu wa thupilo, lomwe ndi mpingo.+ Iye ndiye chiyambi, woyamba kubadwa kuchokera kwa akufa,+ kuti adzakhale woyamba+ pa zinthu zonse. 19  Zili motero chifukwa kunamukomera Mulungu kuti zinthu zonse+ zikhale mwa mwana wakeyo ndipo zidzazemo bwino. 20  Kuti kudzera mwa mwana wakeyo iye agwirizanitsenso+ zinthu zina zonse ndi iyeyo,+ pokhazikitsa mtendere+ mwa magazi+ amene iye anakhetsa pamtengo wozunzikirapo,*+ kaya zikhale zinthu zapadziko lapansi kapena zinthu zakumwamba. 21  Ndithudi, inu amene kale munali otalikirana+ naye ndiponso adani ake chifukwa maganizo anu anali pa ntchito zoipa,+ 22  tsopano wagwirizana+ nanunso pogwiritsa ntchito thupi lanyama la mwanayo kudzera mu imfa yake.+ Wachita izi kuti akuperekeni pamaso pa iyeyo, muli opatulika ndi opanda chilema,+ ndiponso opanda chifukwa chokunenezerani.+ 23  Adzaterodi, malinga ngati mupitirizabe m’chikhulupiriro,+ muli okhazikika pamaziko+ ndiponso olimba, osasunthika+ pa chiyembekezo cha uthenga wabwino umene munamva,+ umenenso unalalikidwa+ m’chilengedwe chonse+ cha pansi pa thambo. Uthenga wabwino umenewu ndi umene ineyo Paulo ndinakhala mtumiki wake.+ 24  Ndikusangalala tsopano ndi masautso amene ndikukumana nawo chifukwa cha inu.+ Ndipo inenso kumbali yanga, ndikuona kuti sindinazunzikebe mokwanira+ monga chiwalo cha thupi la Khristu, limene ndi mpingo.+ 25  Ndinakhala mtumiki+ wa mpingo umenewu mogwirizana ndi udindo+ umene Mulungu anandipatsa, woti ndilalikire mawu a Mulungu mokwanira, kuti inuyo mupindule. 26  Mawuwo ndi chinsinsi chopatulika+ chimene chinabisidwa nthawi* zakale,+ ndiponso kwa mibadwo yakale. Koma tsopano chaululidwa+ kwa oyera ake. 27  Mulungu anaululira anthu a mitundu ina chinsinsi chopatulikachi,+ chimene chili chodzaza ndi ulemerero ndi chuma chauzimu.+ Chinsinsicho n’chakuti Khristu+ ndi wogwirizana ndi inuyo, zimene zikutanthauza kuti muli ndi chiyembekezo chodzalandira ulemerero pamodzi naye.+ 28  Tikulengeza,+ kuchenjeza, ndi kuphunzitsa munthu aliyense za ameneyu mu nzeru zonse,+ kuti tipereke munthu aliyense kwa Mulungu ali wokhwima mwauzimu+ mogwirizana ndi Khristu. 29  Ineyo ndikugwira ntchito mwakhama kuti ndichite zimenezi, poyesetsa kwambiri+ mogwirizana ndi mphamvu+ yake imenenso ikugwira ntchito mwa ine.+

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Zakumapeto 9.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.