Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Aheberi 8:1-13

8  Ndiye kunena za zinthu zimene tikukambiranazi, mfundo yaikulu ndi iyi: Tili ndi mkulu wa ansembe+ ngati ameneyu, ndipo iye wakhala pansi kumwamba, kudzanja lamanja la mpando wachifumu wa Wolemekezeka.+  Iye ndi wantchito wotumikira ena wa m’malo oyerawo+ komanso m’chihema chenicheni, chomangidwa ndi Yehova,+ osati munthu.+  Pakuti mkulu wa ansembe aliyense amaikidwa kuti azipereka zonse ziwiri, mphatso ndi nsembe.+ Ndiye chifukwa chake kunali kofunika kuti uyunso akhale ndi chinachake chopereka.+  Choncho, iye akanakhalabe padziko lapansi, sakanakhala wansembe,+ popeza amuna opereka mphatsozo malinga ndi Chilamulo, alipo kale.  Koma amuna amenewo akuchita utumiki wopatulikawo m’chifaniziro+ ndi mu mthunzi+ wa zinthu zakumwamba. Izi zinaonekera mu lamulo limene Mulungu anapatsa Mose, atatsala pang’ono kumanga chihema.+ Lamulo lake linali lakuti:+ “Uonetsetse kuti wapanga zinthu zonse motsatira chitsanzo chimene wasonyezedwa m’phiri.”+  Koma tsopano Yesu walandira ntchito yapamwamba kwambiri yotumikira ena, moti wakhalanso mkhalapakati+ wa pangano labwino kwambiri,+ limene lakhazikitsidwa mwalamulo pa malonjezo abwinonso.+  Pangano loyamba lija likanakhala lopanda zolakwika, sipakanafunikanso pangano lachiwiri.+  Pakuti iye akuimba anthu mlandu pamene akunena kuti: “‘Taonani! Masiku adzafika, pamene ndidzachita pangano latsopano ndi nyumba ya Isiraeli komanso ndi nyumba ya Yuda,’ watero Yehova.+  ‘Koma pangano+ limeneli si lofanana ndi limene ndinapangana ndi makolo awo pamene ndinagwira dzanja lawo kuti ndiwatulutse m’dziko la Iguputo,+ chifukwa iwo sanapitirize kusunga pangano+ langalo moti ndinasiya kuwasamalira,’ watero Yehova.”+ 10  “‘Pangano limene ndidzapangana ndi nyumba ya Isiraeli pambuyo pa pangano loyamba lija ndi ili: Ndidzaika malamulo anga m’maganizo mwawo ndi kuwalemba m’mitima yawo.+ Ine ndidzakhala Mulungu wawo+ ndipo iwo adzakhala anthu anga,’+ watero Yehova. 11  “‘Munthu sadzaphunzitsa nzika inzake kapena m’bale wake kuti: “Um’dziwe Yehova!”+ Pakuti aliyense wa iwo adzandidziwa,+ kuyambira wamng’ono mpaka wamkulu. 12  Ine ndidzawachitira chifundo pa zochita zawo zosalungama, ndipo sindidzakumbukiranso machimo awo.’”+ 13  Ponena kuti “pangano latsopano,” iye wapanga loyambalo kukhala lotha ntchito.+ Tsopano pangano limene latha ntchito ndipo likukalamba, latsala pang’ono kufafanizika.+

Mawu a M'munsi