Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Aheberi 5:1-14

5  Mkulu wa ansembe aliyense wotengedwa mwa anthu amaikidwa kuti achite utumiki wa Mulungu m’malo mwa anthu,+ kuti azipereka mphatso ndi nsembe zophimba machimo.+  Amakhala woleza mtima pochita zinthu ndi anthu osadziwa kanthu ndi olakwa, chifukwa iyenso ndi wofooka.+  Ndipo chifukwa cha zimenezo, amafunika kupereka nsembe za machimo ake, monga mmene amaperekera nsembe za machimo a anthu onse.+  Komanso, munthu amalandira ulemu umenewu, osati mwa kufuna kwake,+ koma mwa kuchita kuitanidwa ndi Mulungu,+ monga mmene anaitanira Aroni.+  Zilinso chimodzimodzi ndi Khristu. Iye sanadzipatse yekha ulemerero+ mwa kudziika yekha kukhala mkulu wa ansembe.+ Koma amene anamupatsa+ ulemerero umenewo ndi amene analankhula zokhudza iyeyu kuti: “Iwe ndiwe mwana wanga. Lero ine ndakhala atate wako.”+  Monga mmene akuneneranso penapake kuti: “Iwe ndiwe wansembe mpaka muyaya monga mwa unsembe wa Melekizedeki.”+  Pamene anali munthu, Khristu anapereka mapemphero opembedzera ndi opempha,+ kwa amene anali wokhoza kumupulumutsa ku imfa. Anapereka mapempherowa mofuula+ komanso akugwetsa misozi, ndipo anamumvera chifukwa chakuti anali kuopa Mulungu.+  Ngakhale kuti anali Mwana wa Mulungu, anaphunzira kumvera chifukwa cha mavuto amene anakumana nawo.+  Ndipo atakhala wangwiro,+ anakhala ndi udindo wopereka chipulumutso chamuyaya+ kwa onse omumvera,+ 10  chifukwa watchulidwa mwachindunji ndi Mulungu kuti ndi mkulu wa ansembe monga mwa unsembe wa Melekizedeki.+ 11  Tili ndi zambiri zoti tinene zokhudza iyeyu koma zovuta kuzifotokoza chifukwa chakuti inu mumachedwa kumvetsa zinthu.+ 12  N’zoona kuti munayenera kukhala aphunzitsi+ pofika nthawi ino. Koma sizili choncho, ndipo mukufunikanso wina woti akuphunzitseni mfundo zoyambirira+ za m’mawu opatulika a Mulungu,+ kuyambira pa chiyambi. Inu mwakhala ngati munthu wofunika mkaka, osati chakudya chotafuna.+ 13  Pakuti aliyense woyamwa mkaka sadziwa mawu a chilungamo, chifukwa adakali kamwana.+ 14  Koma chakudya chotafuna ndi cha anthu okhwima mwauzimu, amene pogwiritsa ntchito mphamvu zawo za kuzindikira,+ aphunzitsa mphamvuzo kusiyanitsa choyenera ndi chosayenera.+

Mawu a M'munsi