Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Aheberi 4:1-16

4  Chotero, popeza lonjezo lolowa mu mpumulo wake lidakalipo, samalani kuopera kuti pa nthawi ina, wina wa inu angalephere kukwaniritsa zofunika kuti akalowe mu mpumulowo.+  Uthenga wabwino unalengezedwa kwa ife,+ monga mmenenso unalengezedwera kwa makolo athu. Koma mawu amene iwo anamva sanapindule nawo, chifukwa sanakhale ndi chikhulupiriro ngati cha amene anamvera mawuwo.+  Ife amene tasonyeza chikhulupiriro tikulowadi mu mpumulowo. Ponena za mpumulo umenewu iye anati: “Choncho ndinalumbira mu mkwiyo wanga kuti, ‘Sadzalowa mu mpumulo wanga,’”+ ngakhale kuti ntchito zake zinali zitatha kuyambira pamene dziko linakhazikitsidwa.*+  Pakuti penapake, ponena za tsiku la 7, anati: “Ndipo Mulungu anapuma pa ntchito zake zonse pa tsiku la 7.”  Panonso akunena kuti: “Sadzalowa mu mpumulo wanga.”+  Choncho, popeza kuti ena ayenerabe kulowa mu mpumulo umenewo, ndipo amene anali oyamba kuwalalikira uthenga wabwino sanalowemo chifukwa cha kusamvera,  iye wapatulanso tsiku lina chifukwa wagwiritsa ntchito mawu akuti “Lero” mu salimo la Davide, pambuyo pa nthawi yaitali kwambiri. Izi zikugwirizana ndi zimene tanena kale zija kuti: “Lero anthu inu mukamvera mawu a Mulungu,+ musaumitse mitima yanu.”+  Pakuti ngati Yoswa anawalowetsa m’malo ampumulo, Mulungu sakananenanso pambuyo pake+ za tsiku lina.  Chotero mpumulo wa sabata udakalipo kwa anthu a Mulungu.+ 10  Munthu amene walowa mu mpumulo wa Mulungu, ndiye kuti wapumanso pa ntchito zake,+ monga mmene Mulungu anapumira pa ntchito zake. 11  Chotero, tiyeni tichite chilichonse chotheka kuti tilowe mu mpumulo umenewo, kuopera kuti wina angagwe ndi kutengera chitsanzo cha kusamvera cha makolo athuwo.+ 12  Pakuti mawu+ a Mulungu ndi amoyo+ ndi amphamvu,+ ndipo ndi akuthwa kuposa lupanga lililonse lakuthwa konsekonse.+ Amalasa munthu mumtima mpaka kulekanitsa moyo+ ndi mzimu,+ komanso mfundo za mafupa ndi mafuta a m’mafupa. Mawu a Mulungu amathanso kuzindikira zimene munthu akuganiza komanso zolinga za mtima wake.+ 13  Palibe cholengedwa chimene Mulungu sangathe kuchiona.+ Chifukwa kwa iye zinthu zonse zili poonekera ndipo amatha kuziona bwinobwino. Ndipotu ife tikuyenera kudzayankha pa zochita zathu kwa Mulungu amene amaona zonseyo.+ 14  Chotero, popeza tili ndi mkulu wa ansembe wapamwamba, Yesu Mwana wa Mulungu,+ amene anapita kumwamba,+ tiyeni tipitirize kulengeza chikhulupiriro chathu mwa iye.+ 15  Pakuti mkulu wa ansembe amene tili naye si mkulu wa ansembe amene sangatimvere chisoni+ pa zofooka zathu. Koma tili ndi mkulu wa ansembe amene anayesedwa m’zonse ngati ifeyo, ndipo anakhalabe wopanda uchimo.+ 16  Choncho, tiyeni tiyandikire mpando wachifumu wa kukoma mtima kwakukulu ndipo tipemphere kwa Mulungu+ ndi ufulu wa kulankhula,+ kuti atichitire chifundo ndi kutisonyeza kukoma mtima kwakukulu pa nthawi imene tikufunika thandizo.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “kuponya mbewu pansi.” Mbewuzo zikutanthauza ana a Adamu ndi Hava.