Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Aheberi 2:1-18

2  Ndiye chifukwa chake n’kofunika kuti tiganizire mozama, kuposa nthawi zonse, zinthu zimene tinamva,+ kuti tisatengeke pang’onopang’ono n’kusiya chikhulupiriro.+  Pakuti ngati mawu amene angelo ananena+ analidi osagwedezeka, ndipo pa tchimo lililonse ndi kusamvera kulikonse, chilango chinaperekedwa mogwirizana ndi chilungamo,+  tidzapulumuka bwanji+ ngati tanyalanyaza+ chipulumutso chachikulu chonchi?+ Ambuye wathu ndi amene anayamba kunena za chipulumutso chimenechi,+ ndipo anthu amene anamumva anatitsimikizira zimenezo.+  Mulungu nayenso anachitira umboni za chipulumutsocho ndi zizindikiro, zinthu zodabwitsa, ntchito zamphamvu zosiyanasiyana+ komanso mwa kupereka mphatso zosiyanasiyana+ za mzimu woyera malinga ndi chifuniro chake.+  Pakuti dziko lapansi lokhalamo anthu limene likubweralo,+ limene ife tikunena, sanaliike pansi pa ulamuliro wa angelo.  Koma mboni ina inachitira umboni penapake, kuti: “Munthu ndani kuti muzimuganizira,+ kapena mwana wa munthu ndani kuti muzimusamalira?+  Munamutsitsa pang’ono poyerekeza ndi angelo. Munamuveka ulemerero ndi ulemu+ monga chisoti chachifumu, ndipo munamuika kuti alamulire ntchito za manja anu.+  Zinthu zonse munaziika pansi pa mapazi ake.”+ Popeza kuti anaika zinthu zonse pansi pa mwana wake,+ Mulungu sanasiye kanthu kalikonse, osakaika pansi pa mwana wakeyo.+ Komabe, padakali pano sitikuona kuti zinthu zonse zili pansi pake.+  Koma tikuona Yesu, amene pa nthawi ina anamutsitsa pang’ono poyerekeza ndi angelo.+ Tikumuona atamuveka ulemerero+ ndi ulemu ngati chisoti chachifumu chifukwa chakuti anazunzika mpaka imfa.+ Zimenezi zinamuchitikira kuti mwa kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, alawe imfa m’malo mwa munthu aliyense.+ 10  Zinthu zonse zilipo kuti zipereke ulemerero kwa Mulungu ndipo zinakhalapo kudzera mwa iye.+ Choncho pamene akuika ana ambiri pa ulemerero,+ n’koyenera kuti achititse Mtumiki Wamkulu+ wa chipulumutso chawo kukhala wangwiro kudzera m’masautso.+ 11  Pakuti onse, woyeretsayo ndi amene akuyeretsedwawo,+ amachokera kwa mmodzi.+ Pa chifukwa chimenechi, iye sachita manyazi kuwatcha “abale,”+ 12  pamene akunena kuti: “Ndidzalengeza dzina lanu kwa abale anga. Ndidzakutamandani mwa kuimba nyimbo pakati pa mpingo.”+ 13  Komanso pamene akunena kuti: “Ndidzadalira iye.”+ Ndi kutinso: “Taonani! Ine ndi ana amene Yehova anandipatsa.”+ 14  Chotero, popeza kuti “ana” amenewo onse ndi amagazi ndi mnofu, iyenso anakhala wamagazi ndi mnofu.+ Anachita izi kuti kudzera mu imfa yake,+ awononge+ Mdyerekezi,+ amene ali ndi njira yobweretsera imfa.+ 15  Anachitanso zimenezi kuti amasule+ onse amene poopa imfa,+ anali mu ukapolo moyo wawo wonse.+ 16  Pakuti iye sakuthandiza angelo ngakhale pang’ono, koma akuthandiza mbewu ya Abulahamu.+ 17  Chotero, iye anayenera ndithu kukhala ngati “abale” ake m’zonse,+ kuti akhale mkulu wa ansembe wachifundo ndi wokhulupirika pa zinthu za Mulungu.+ Cholinga chake chinali choti apereke nsembe yophimba machimo+ kuti tikhalenso ogwirizana ndi Mulungu.+ 18  Popeza kuti iye mwini anavutika pamene anali kuyesedwa,+ amatha kuthandiza anthu amene akuyesedwa.+

Mawu a M'munsi