Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Aheberi 13:1-25

13  Mupitirize kukonda abale.+  Musaiwale kuchereza alendo,+ pakuti potero, ena anachereza angelo mosadziwa.+  Kumbukirani amene ali m’ndende+ ngati kuti mwamangidwa nawo limodzi.+ Kumbukiraninso amene akuzunzidwa,+ popeza inunso mudakali m’thupi lanyama.  Ukwati ukhale wolemekezeka kwa onse, ndipo pogona pa anthu okwatirana pakhale posaipitsidwa,+ pakuti Mulungu adzaweruza adama ndi achigololo.+  Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama,+ koma mukhale okhutira+ ndi zimene muli nazo pa nthawiyo.+ Pakuti Mulungu anati: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.”+  Moti tikhale olimba mtima ndithu+ ndipo tinene kuti: “Yehova* ndiye mthandizi wanga. Sindidzaopa. Munthu angandichite chiyani?”+  Kumbukirani amene akutsogolera pakati panu.+ Amenewa anakuphunzitsani mawu a Mulungu. Ndipo pamene mukuonetsetsa zotsatira zabwino za khalidwe lawo, tsanzirani+ chikhulupiriro chawo.+  Yesu Khristu ali chimodzimodzi dzulo ndi lero, ndiponso mpaka muyaya.+  Musatengeke ndi ziphunzitso zosiyanasiyana zachilendo.+ Ndi bwino kuti mtima ukhale wolimba chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu,+ osati chifukwa cha zakudya.+ Pakuti amene amatanganidwa ndi zakudyazo sakupindula nazo. 10  Ife tili ndi guwa lansembe limene ochita utumiki wopatulika kuchihema, alibe ulamuliro wodya za paguwapo.+ 11  Pakuti nyama zimene magazi ake, mkulu wa ansembe amalowa nawo m’malo oyera chifukwa cha machimo, amakazitentha kunja kwa msasa.+ 12  Zinalinso chimodzimodzi ndi Yesu. Kuti ayeretse+ anthu ndi magazi ake,+ anakavutikira kunja kwa chipata.+ 13  Chotero, tiyeni timutsatire kunja kwa msasako, titasenza chitonzo chimene iye anasenza.+ 14  Pakuti pamene tili pano, tilibe mzinda wokhazikika,+ koma ndi mtima wonse tikufunitsitsa mzinda umene ukubwerawo.+ 15  Kudzera mwa iye, tiyeni nthawi zonse tizitamanda Mulungu. Tizichita zimenezi monga nsembe imene tikupereka kwa Mulungu,+ yomwe ndi chipatso cha milomo yathu.+ Timagwiritsa ntchito milomo imeneyi polengeza dzina lake kwa anthu ena.+ 16  Komanso, musaiwale kuchita zabwino+ ndi kugawana zinthu ndi ena, pakuti nsembe zotero Mulungu amakondwera nazo.+ 17  Muzimvera amene akutsogolera pakati panu+ ndipo muziwagonjera.+ Iwo amayang’anira miyoyo yanu monga anthu amene adzayankhe mlandu.+ Muziwamvera ndi kuwagonjera kuti agwire ntchito yawo mwachimwemwe, osati modandaula, pakuti akatero zingakhale zokuvulazani.+ 18  Pitirizani kutipempherera,+ pakuti tikukhulupirira kuti tili ndi chikumbumtima choona, popeza tikufuna kuchita zinthu zonse moona mtima.+ 19  Koma makamaka ndikukulimbikitsani kuchita zimenezi, kuti ndibwerere kwa inu mwamsanga.+ 20  Tsopano, Mulungu wamtendere,+ amene anaukitsa kwa akufa+ m’busa wamkulu+ wa nkhosa+ wokhala ndi magazi a pangano losatha,+ Ambuye wathu Yesu, 21  akukonzekeretseni ndi chilichonse chabwino kuti muchite chifuniro chake. Ndipo kudzera mwa Yesu Khristu, achite mwa ife zimene zili zokondweretsa pamaso pake.+ Kwa iye kukhale ulemerero kwamuyaya.+ Ame. 22  Tsopano, ndikukudandaulirani abale, chonde khalani oleza mtima pamene mukuwerenga mawu olimbikitsawa, chifukwa ndakulemberani kalatayi m’mawu ochepa.+ 23  Dziwani kuti m’bale wathu Timoteyo+ wamasulidwa, ndipo ngati angabwere posachedwapa, ndibwera naye limodzi kudzakuonani. 24  Mundiperekere moni kwa onse amene akutsogolera pakati panu,+ ndiponso kwa oyera ena onse. A ku Italiya+ akukupatsani moni. 25  Kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye wathu+ kukhale nanu nonsenu.

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 2.