Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Agalatiya 4:1-31

4  Tsopano ndikuuzeni kuti, wolandira cholowa akakhala kamwana, iye sasiyana konse ndi kapolo,+ ngakhale ali mwini zinthu zonse.  Amakhalabe pansi pa amuna oyang’anira ana+ ndiponso anthu oyang’anira zinthu za mbuye wawo, kufikira tsiku limene bambo ake anaikiratu.  N’chimodzimodzinso ifeyo. Pamene tinali tiana, tinali akapolo a mfundo zachibwanabwana+ zimene anthu a m’dzikoli amayendera.  Koma nthawi itakwana,+ Mulungu anatumiza Mwana wake,+ amene anadzabadwa kwa mkazi+ ndipo anadzakhala pansi pa chilamulo.+  Zinatero kuti amasule anthu okhala pansi pa chilamulo mwa kuwagula,+ kutinso Mulungu atitenge ife kukhala ana ake.+  Tsopano pakuti ndinu ana ake, Mulunguyo watitumizira mzimu+ wa Mwana wake m’mitima yathu ndipo mzimuwo ukufuula kuti: “Abba,* Atate!”+  Chotero si iwenso kapolo, koma mwana ndipo ngati uli mwana, ndiwenso wolandira cholowa kudzera mwa Mulungu.+  Ngakhale zili choncho, pamene munali osadziwa Mulungu,+ munali akapolo a zinthu zimene mwachilengedwe si milungu.+  Koma tsopano pamene mwadziwa Mulungu, kapena tinene kuti tsopano pamene mwadziwidwa ndi Mulungu,+ mukubwereranso bwanji ku mfundo zachibwanabwana,+ zomwe ndi zosathandiza ndiponso zopanda pake,+ n’kumafuna kukhalanso akapolo ake?+ 10  Mukusunga mwakhama masiku,+ miyezi,+ nyengo ndi zaka. 11  Ndikuda nkhawa, kuti mwina ntchito imene ndaigwira pa inu ipita pachabe.+ 12  Ndikukupemphani abale anga, khalani monga ine+ chifukwa inenso ndinali ngati inuyo kale.+ Simunandilakwire ayi.+ 13  Koma mukudziwa kuti nthawi yoyamba imene ndinalengeza uthenga wabwino kwa inu chifukwa chakuti ndinali kudwala,+ 14  inuyo simunanyansidwe ndi matenda anga, amene anali mayesero kwa inu, ndipo simunalavule malovu ponyansidwa nawo, koma munandilandira ngati mngelo+ wa Mulungu, ngati Khristu Yesu.+ 15  Chili kuti nanga chimwemwe chimene munali nacho poyamba chija?+ Pakuti ndikunenetsa kuti, zikanakhala zotheka, mukanakolowola maso anu n’kundipatsa.+ 16  Kodi ndakhala mdani+ wanu tsopano chifukwa ndakuuzani zoona?+ 17  Anthu ena akuyesetsa kwambiri kuti akukopereni kwa iwowo,+ osati ndi zolinga zabwino, koma kuti akutsekerezeni kuti musabwere kwa ine, kuti inuyo muyesetse kuwatsatira.+ 18  Ngati munthu akukufunani kwambiri pa chifukwa chabwino, n’zabwino kwa inu.+ Zimenezi zikachitika osati pa nthawi imene ine ndili nanu limodzi yokha,+ komanso nthawi zonse, 19  ndiye kuti n’zabwino kwa inu ana anga.+ Ine ndayambanso kumva zopweteka zimene ndinamva pokuberekani, mpaka Khristu adzakhazikike mwa inu.+ 20  Panopa ndikanakonda kukhala pakati panu+ kuti ndilankhule mosiyanako, chifukwa mwandithetsa nzeru.+ 21  Tandiuzani, inu amene mukufuna kutsatira chilamulo,+ Kodi simukumva zimene Chilamulocho chikunena?+ 22  Mwachitsanzo, Malemba amati Abulahamu anabereka ana aamuna awiri, wina kwa mdzakazi*+ ndipo wina kwa mkazi amene anali mfulu.+ 23  Koma mwana amene anabadwa kwa mdzakazi uja anabadwa monga mmene ana onse amabadwira,+ pamene mwana winayo amene anabadwa kwa mkazi amene anali mfulu anabadwa mwa lonjezo.+ 24  Zinthu zimenezi zili ndi tanthauzo lophiphiritsira,+ pakuti azimayi amenewa akuimira mapangano awiri.+ Loyamba ndi pangano la paphiri la Sinai,+ limene limabereka ana oti akhale akapolo. Pangano limenelo ndiye Hagara uja. 25  Tsopano, Hagara ameneyu akutanthauza Sinai,+ phiri la ku Arabiya, ndipo masiku ano akufanana ndi Yerusalemu, pakuti ali mu ukapolo+ pamodzi ndi ana ake. 26  Koma Yerusalemu+ wam’mwamba ndi mfulu, ndipo ndiye mayi wathu.+ 27  Pakuti Malemba amati: “Kondwera, mkazi wosabereka iwe amene sunaberekepo mwana. Kuwa ndipo fuula mokondwa, iwe mkazi amene sunamvepo zowawa za pobereka, pakuti ana a mkazi wosiyidwa ndi ambiri kuposa ana a mkazi amene ali ndi mwamuna.”+ 28  Tsopano ifeyo abale, ndife ana a lonjezo monga mmene analili Isaki.+ 29  Koma monga mmene zinalili pa nthawiyo, kuti wobadwa monga mmene ana onse amabadwira anayamba kuzunza+ wobadwa mwa mzimu, ndi mmenenso zilili masiku ano.+ 30  Ngakhale zili choncho, kodi Malemba amati chiyani? “Thamangitsani mdzakaziyu pamodzi ndi mwana wakeyu pano, pakuti sizingatheke mwana wa mdzakazi kudzakhala wolandira cholowa pamodzi ndi mwana wa mkazi waufulu.”+ 31  Chotero abale, ife ndife ana a mkazi waufulu,+ osati a mdzakazi.+

Mawu a M'munsi

“Abba” ndi mawu achiaramu otanthauza “ababa,” kapena, “Inu bambo anga!”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.