Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

2 Timoteyo 3:1-17

3  Koma dziwa kuti, masiku otsiriza+ adzakhala nthawi yapadera komanso yovuta.+  Pakuti anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzimva, odzikweza, onyoza, osamvera makolo, osayamika, osakhulupirika,+  osakonda achibale awo,+ osafuna kugwirizana ndi anzawo,+ onenera anzawo zoipa,+ osadziletsa, oopsa,+ osakonda zabwino,+  achiwembu,+ osamva za ena, odzitukumula ndiponso onyada,+ okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu,+  ndiponso ooneka ngati odzipereka kwa Mulungu+ koma amakana kuti mphamvu ya kudziperekako iwasinthe.+ Anthu amenewa uwapewe.+  Pakati pa anthu amenewa pamachokera anthu amene amalowerera mozemba m’mabanja,+ ndi kugwira amayi osiyanasiyana kuti akhale akapolo awo. Amayiwo amakhala ofooka, olemedwa ndi machimo, ndiponso otengeka ndi zilakolako zosiyanasiyana,+  amene amakhala akuphunzira nthawi zonse, koma satha kudziwa choonadi molondola.+  Tsopano monga mmene Yane ndi Yambure anatsutsira Mose, anthu amenewanso akupitiriza kutsutsa choonadi.+ Iwo ali ndi maganizo opotoka kwambiri,+ ndipo sakuyenerera chikhulupirirochi.+  Ngakhale zili choncho, iwo sadzapita patali, chifukwa misala yawo idzaonekera bwino kwa anthu onse, ngati mmene zinakhalira ndi misala ya anthu awiri aja. 10  Koma iwe wayesetsa kutsatira chiphunzitso changa, moyo wanga,+ cholinga changa, chikhulupiriro changa, kuleza mtima kwanga, chikondi changa, ndi kupirira kwanga. 11  Ukudziwanso mazunzo ndi masautso amene ndinakumana nawo ku Antiokeya,+ ku Ikoniyo,+ ndi ku Lusitara.+ Komabe, Ambuye anandipulumutsa m’mazunzo onsewa.+ 12  Pajatu onse ofuna kukhala ndi moyo wodzipereka kwa Mulungu mwa Khristu Yesu, nawonso adzazunzidwa.+ 13  Koma anthu oipa ndi onyenga adzaipiraipirabe. Iwo azidzasocheretsa ena ndiponso azidzasocheretsedwa.+ 14  Koma iwe, pitiriza kutsatira zimene unaphunzira ndi zimene unakhulupirira pambuyo pokhutira nazo,+ chifukwa ukudziwa anthu amene anakuphunzitsa.+ 15  Kuyambira pamene unali wakhanda,+ wadziwa malemba oyera amene angathe kukupatsa nzeru zokuthandiza kuti udzapulumuke+ kudzera m’chikhulupiriro chokhudza Khristu Yesu.+ 16  Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu,+ ndipo ndi opindulitsa pa kuphunzitsa,+ kudzudzula,+ kuwongola zinthu+ ndi kulangiza m’chilungamo,+ 17  kuti munthu wa Mulungu akhale woyenerera bwino+ ndi wokonzeka mokwanira kuchita ntchito iliyonse yabwino.+

Mawu a M'munsi