Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

2 Timoteyo 2:1-26

2  Choncho iwe mwana wanga,+ pitiriza kupeza mphamvu+ m’kukoma mtima kwakukulu+ kumene kuli mwa Khristu Yesu.  Zinthu zimene unazimva kwa ine ndi kwa mboni zambiri+ zokhudza ine, zimenezo uziphunzitse kwa anthu okhulupirika amene nawonso, adzakhala oyenerera bwino kuphunzitsa ena.+  Monga msilikali wabwino+ wa Khristu Yesu, khala wokonzeka kumva zowawa.+  Msilikali amene ali pa nkhondo+ sachita nawo zamalonda zimene anthu wamba amachita,+ pofuna kukondweretsa amene anamulemba usilikali.  Komanso, ngati munthu akuchita nawo mpikisano ngakhale pa masewera,+ savekedwa nkhata yaulemerero kumutu akapanda kupikisana nawo motsatira malamulo.  Mlimi wogwira ntchito molimbikira ndiye ayenera kukhala woyamba kudya zipatso zimene anabzala.+  Uziganizira zimene ndikukuuzazi nthawi zonse. Ndithudi, Ambuye adzakuthandiza kuzindikira+ zinthu zonse.  Kumbukira kuti, malinga ndi uthenga wabwino umene ndikulalikira,+ Yesu Khristu anauka kwa akufa+ ndipo anali mbewu ya Davide.+  Chifukwa cha uthengawu, ndikumva zowawa mpaka kutsekeredwa m’ndende+ ngati wochita zoipa. Komabe, mawu a Mulungu samangika.+ 10  Pa chifukwa chimenechi, ndikupirirabe zinthu zonse chifukwa cha anthu osankhidwa ndi Mulungu,+ kuti iwonso alandire chipulumutso chimene chimabwera chifukwa chokhala ogwirizana ndi Khristu Yesu, ndiponso alandire ulemerero wosatha.+ 11  Mawu awa ndi oona,+ akuti: Ndithudi, ngati tinafa naye limodzi, tidzakhalanso ndi moyo limodzi naye.+ 12  Tikapitiriza kupirira, tidzalamuliranso limodzi ndi iye monga mafumu.+ Tikamukana,+ iyenso adzatikana, 13  ndipo tikakhala osakhulupirika,+ iye adzakhalabe wokhulupirika, pakuti sangadzikane. 14  Uziwakumbutsa+ zimenezi nthawi zonse. Uziwachenjeza mwamphamvu+ pamaso pa Mulungu,+ kuti asamakangane pa mawu.+ Kuchita zimenezo kulibe phindu m’pang’ono pomwe chifukwa kumawononga chikhulupiriro cha omvetsera. 15  Chita chilichonse chotheka kuti usonyeze kuti ndiwe wovomerezeka+ pamaso pa Mulungu, wantchito+ wopanda chifukwa chochitira manyazi+ ndi ntchito imene wagwira, ndiponso wophunzitsa ndi kufotokoza bwino mawu a choonadi.+ 16  Koma pewa nkhani zopeka zimene zimaipitsa zinthu zoyera,+ pakuti kusaopa Mulungu kudzachulukirachulukira+ mwa anthu olankhula zotero, 17  ndipo mawu awo adzafalikira ngati chilonda chonyeka.+ Ena mwa anthu amenewo ndi Hemenayo ndi Fileto.+ 18  Anthu amenewa apatuka pa choonadi,+ ponena kuti kuuka kwa akufa kunachitika kale+ ndipo akuwononga chikhulupiriro cha ena.+ 19  Komabe, maziko olimba a Mulungu adakali chikhalire,+ ndipo ali ndi chidindo cha mawu akuti: “Yehova* amadziwa anthu ake,”+ ndiponso akuti: “Aliyense wotchula dzina la Yehova+ aleke kuchita zosalungama.”+ 20  M’nyumba yaikulu simukhala ziwiya zagolide ndi zasiliva zokha ayi, koma mumakhalanso zamtengo ndi zadothi. Ziwiya zina zimakhala za ntchito yolemekezeka koma zina zimakhala za ntchito yonyozeka.+ 21  Choncho, ngati munthu akupewa ziwiya za ntchito yonyozekazo, adzakhala chiwiya cha ntchito yolemekezeka, choyera, chofunika kwa mwiniwake, ndi chokonzeka kugwira ntchito iliyonse yabwino.+ 22  Chotero, thawa zilakolako zaunyamata,+ koma tsatira chilungamo,+ chikhulupiriro, chikondi, ndi mtendere+ limodzi ndi anthu oitana pa Ambuye ndi mtima woyera.+ 23  Ndiponso, uzikana mafunso opusa ndi opanda nzeru,+ podziwa kuti amayambitsa mikangano.+ 24  Kapolo wa Ambuye sayenera kukangana ndi anthu,+ koma ayenera kukhala wodekha kwa onse.+ Ayeneranso kukhala woyenerera kuphunzitsa,+ wougwira mtima pokumana ndi zoipa,+ 25  ndi wolangiza mofatsa anthu otsutsa+ kuti mwina Mulungu angawalole kulapa,+ kuti adziwe choonadi molondola.+ 26  Komanso kuti mwina nzeru zawo zingabwereremo kuti awonjoke mumsampha+ wa Mdyerekezi, poona kuti wawagwira amoyo+ pofuna kukwaniritsa cholinga chake.

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 2.