Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

2 Samueli 8:1-18

8  Pambuyo pake, Davide anapha Afilisiti+ ndi kuwagonjetsa,+ ndipo anawalanda mzinda wa Metege-ama.  Davide anagonjetsanso Amowabu+ ndi kuwayeza ndi chingwe. Iye anawagoneka pansi kuti ayeze zingwe ziwiri ndi kuwapha, ndiponso chingwe chimodzi chathunthu n’kuwasiya amoyo.+ Choncho Amowabu anakhala atumiki a Davide+ ndipo anali kukhoma msonkho kwa iye.+  Davide anapha Hadadezeri,+ mwana wa Rehobu mfumu ya Zoba,+ pamene Hadadezeriyo anali kupita kumtsinje wa Firate+ kukabwezeretsa ulamuliro wake kumeneko.  Davide anagwira amuna 1,700 okwera pamahatchi ndi amuna 20,000 oyenda pansi+ a Hadadezeri. Kenako Davide anapundula*+ mahatchi onse a magaleta+ kusiyapo mahatchi a magaleta okwana 100.  Pamene Asiriya a ku Damasiko+ anabwera kudzathandiza Hadadezeri mfumu ya Zoba, Davide anapha amuna 22,000 a ku Siriya.+  Kenako Davide anamanga midzi ya asilikali+ m’dera la Asiriya a ku Damasiko ndipo Asiriyawo anakhala akapolo a Davide moti anali kukhoma msonkho+ kwa iye. Yehova anapitiriza kupulumutsa Davide kulikonse kumene wapita.+  Komanso Davide anatenga zishango zozungulira+ zagolide zimene zinali ndi atumiki a Hadadezeri ndipo anabwera nazo ku Yerusalemu.  Mfumu Davide inatenga mkuwa wochuluka kwambiri+ ku Beta ndi Berota, mizinda ya Hadadezeri.  Tsopano Toi, mfumu ya Hamati+ anamva kuti Davide wapha gulu lonse lankhondo la Hadadezeri.+ 10  Choncho Toi anatumiza Yoramu mwana wake kwa Mfumu Davide kukamufunsa za moyo wake+ ndi kumuyamikira chifukwa chomenyana ndi Hadadezeri ndi kumugonjetsa (pakuti Hadadezeri ndi Toi anali kumenyana kawirikawiri). Popita kwa Davide, Yoramu anatenga zinthu zasiliva, zagolide ndi zamkuwa.+ 11  Zinthu zimenezi Mfumu Davide inazipatulira Yehova pamodzi ndi siliva ndi golide wochokera ku mitundu yonse imene inagonjetsa.+ 12  Inapatula siliva ndi golide wochokera ku Siriya, Mowabu,+ kwa ana a Amoni, Afilisiti,+ Aamaleki+ ndiponso siliva ndi golide amene anafunkha kwa Hadadezeri mwana wa Rehobu mfumu ya Zoba.+ 13  Ndipo Davide anadzipangira dzina atabwerako kumene anapha Aedomu 18,000+ m’chigwa cha Mchere.+ 14  Davide anakhazikitsa midzi ya asilikali mu Edomu.+ Mu Edomu yense anaikamo midzi ya asilikali, moti Aedomu anakhala antchito a Davide+ ndipo Yehova anali kupulumutsa Davide kulikonse kumene anali kupita.+ 15  Davide anapitiriza kulamulira Isiraeli+ yense ndipo nthawi zonse anali kupereka zigamulo ndi kuchita chilungamo+ kwa anthu ake onse.+ 16  Yowabu+ mwana wa Zeruya anali mkulu wa asilikali, ndipo Yehosafati+ mwana wa Ahiludi anali wolemba zochitika. 17  Zadoki+ mwana wa Ahitubu ndi Ahimeleki+ mwana wa Abiyatara anali ansembe, pamene Seraya anali mlembi. 18  Benaya+ mwana wa Yehoyada anali mtsogoleri wa Akereti+ ndi Apeleti.+ Ana aamuna a Davide anakhala ansembe.*+

Mawu a M'munsi

Anali kuzipundula mwa kudula mtsempha wakuseri kwa mwendo wam’mbuyo.
Kapena kuti “nduna zazikulu zotumikira mfumu.”