Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

2 Samueli 23:1-39

23  Mawu omaliza amene Davide ananena ndi awa:+ “Mawu a Davide mwana wa Jese,+ Mawu a munthu wamphamvu amene anakwezedwa pamwamba,+ Wodzozedwa+ wa Mulungu wa Yakobo, Munthu wosangalatsa wotchulidwa m’nyimbo zokoma+ za Isiraeli.   Mzimu wa Yehova unandilankhulitsa,+ Ndipo mawu ake anali palilime langa.+   Mulungu wa Isiraeli analankhula, Thanthwe la Isiraeli linandiuza kuti,+ ‘Munthu wolamulira anthu akakhala wolungama,+ N’kumalamulira moopa Mulungu,+   Ulamuliro wake umakhala ngati kuwala kwa m’mawa pamene dzuwa lawala,+ M’mawa wopanda mitambo. Umakhala ngati msipu womera padziko mvula ikakata, dzuwa n’kuwala.’+   Kodi si mmene nyumba yanga ilili kwa Mulungu?+ Chifukwa chakuti anachita nane pangano lomwe lidzakhalapo mpaka kalekale,+ Analikonza bwino ndipo n’lotetezeka.+ Chifukwa ndilo chipulumutso changa+ ndi chondikondweretsa, Kodi chimenechi sindicho chifukwa chake adzakulitsa panganoli?+   Koma anthu onse opanda pake+ amawakankhira kutali+ ngati zitsamba zaminga.+ Pakuti zitsamba zamingazo sizigwiridwa ndi manja pozichotsa.   Munthu akamazigwira Ayenera kukhala ndi zida zachitsulo ndi mkondo, Ndipo zidzatenthedwa ndi moto n’kupseratu.”+  Mayina a amuna amphamvu+ a Davide ndi awa: Yosebu-basebete+ Mtahakemoni, mtsogoleri wa amuna atatu. Iye anatenga mkondo wake n’kupha anthu 800 ulendo umodzi.  Womutsatira anali Eleazara+ mwana wa Dodo+ mwana wa Ahohi. Iye anali mmodzi mwa amuna atatu amphamvu amene anali ndi Davide pamene anatonza Afilisiti. Iwo anasonkhana kumeneko kuti amenye nkhondo, ndipo amuna a Isiraeli anali atathawa.+ 10  Eleazara ndi amene anaimirira ndipo anali kupha Afilisiti mpaka dzanja lake linatopa, koma anagwirabe lupanga+ moti Yehova anapereka chipulumutso chachikulu pa tsiku limenelo.+ Koma anthu ena onse anamutsatira pambuyo pake kuti avule zovala za anthu ophedwawo.+ 11  Womutsatira anali Shama, mwana wamwamuna wa Age Mharari.+ Tsopano Afilisiti anasonkhana pamodzi ku Lehi, kumene kunali munda wodzaza ndi mphodza.+ Kumeneko anthu anali atathawa chifukwa choopa Afilisitiwo. 12  Koma iye anaima pakati pa kachigawo ka mundako ndi kukalanditsa ndipo anapitiriza kupha Afilisiti, moti tsiku limenelo Yehova anapereka chipulumutso chachikulu.+ 13  Ndiyeno pa nthawi yokolola, atatu mwa atsogoleri 30+ anapita kwa Davide kuphanga la Adulamu.+ Apa n’kuti Afilisiti atamanga msasa wa mahema m’chigwa cha Arefai.+ 14  Pamenepo n’kuti Davide ali m’malo ovuta kufikako,+ ndiponso n’kuti mudzi wa asilikali+ a Afilisiti uli ku Betelehemu. 15  Patapita nthawi, Davide anafotokoza zimene anali kulakalaka kuti: “Ndikanakonda ndikanamwa madzi a m’chitsime cha ku Betelehemu chimene chili pachipata!”+ 16  Pamenepo amuna atatu amphamvu aja anakalowa mwamphamvu mumsasa wa Afilisiti, n’kutunga madzi m’chitsime cha ku Betelehemu chimene chinali pachipata. Atatero ananyamula madziwo n’kupita nawo kwa Davide.+ Koma iye anakana kumwa madziwo. M’malomwake anawapereka kwa Yehova mwa kuwathira pansi.+ 17  Ndiyeno iye anati: “Sindingachite zimenezo+ inu Yehova! Kodi ndimwe magazi+ a amuna amene anaika miyoyo yawo pangozi kuti akatunge madziwa?” Choncho iye sanavomere kumwa madziwo. Izi n’zimene amuna atatu amphamvuwo anachita. 18  Koma Abisai,+ m’bale wake wa Yowabu mwana wa Zeruya+ anali mtsogoleri wa anthu 30 amenewo. Iye ananyamula mkondo ndi kupha nawo anthu 300. Abisai anali wotchuka ngati amuna atatu aja.+ 19  Ngakhale kuti anali wolemekezeka kwambiri kuposa amuna ena 30 aja, ndipo anali mtsogoleri wawo, komabe sanafanane ndi amuna atatu oyamba aja.+ 20  Benaya+ mwana wa Yehoyada,+ mwana wa munthu wolimba mtima, anachita zinthu zambiri ku Kabizeeli.+ Iye anapha ana awiri a Ariyeli wa ku Mowabu, ndipo analowanso m’chitsime chopanda madzi n’kupha mkango+ umene unali m’chitsimemo pa tsiku limene kunagwa chipale chofewa.+ 21  Benaya ndiye anaphanso Mwiguputo wa msinkhu waukulu modabwitsa.+ Ngakhale kuti Mwiguputoyo anali ndi mkondo m’manja mwake, Benaya anapitabe kukakumana naye atanyamula ndodo, n’kulanda mkondowo ndipo anamupha ndi mkondo wake womwewo.+ 22  Zimenezi n’zimene Benaya+ mwana wa Yehoyada anachita. Iye anali wotchuka ngati amuna atatu amphamvu aja.+ 23  Ngakhale kuti anali wolemekezeka kwambiri kuposa amuna ena 30 aja, sanafanane ndi amuna atatu aja. Koma Davide anamuika kukhala msilikali wake womulondera.+ 24  Asaheli+ m’bale wake wa Yowabu anali m’gulu la amuna 30 aja. M’gululi munalinso Elihanani+ mwana wa Dodo wa ku Betelehemu, 25  Shama+ Mharodi, Elika Mharodi, 26  Helezi+ Mpaliti, Ira+ mwana wa Ikesi+ Mtekowa, 27  Abi-ezeri+ Muanatoti,+ Mebunai Mhusati,+ 28  Zalimoni Mwahohi,+ Maharai+ Mnetofa, 29  Helebi+ mwana wa Bana Mnetofa, Itai+ mwana wa Ribai wa ku Gibeya wa fuko la ana a Benjamini, 30  Benaya+ Mpiratoni, Hidai wa kuzigwa* za Gaasi,+ 31  Abi-aliboni Mwaraba, Azimaveti+ M’bahurimu, 32  Eliyaba Msaaliboni, ana a Yaseni, Yonatani,+ 33  Shama Mharari, Ahiyamu+ mwana wa Sarari Mharari, 34  Elifeleti mwana wa Ahasibai, mwana wa Mmaakati, Eliyamu mwana wa Ahitofeli+ Mgilo, 35  Heziro+ wa ku Karimeli, Paarai Mwarabu, 36  Igali mwana wa Natani+ wa ku Zoba, Bani Mgadi, 37  Zeleki+ Muamoni, Naharai M’beeroti, onyamula zida za Yowabu mwana wa Zeruya, 38  Ira Muitiri,+ Garebi+ Muitiri, 39  ndi Uriya+ Mhiti, onse pamodzi 37.

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.