Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

2 Samueli 22:1-51

22  Davide analankhula ndi Yehova mawu a nyimbo iyi,+ pa tsiku limene Yehova anamulanditsa kwa adani ake+ onse ndiponso m’manja mwa Sauli.+  Iye anati: “Yehova ndiye thanthwe langa,+ malo anga achitetezo+ ndiponso Wopereka chipulumutso kwa ine.+   Mulungu wanga ndiye thanthwe langa.+ Ine ndidzathawira kwa iye, Iye ndi chishango changa,+ nyanga* yanga+ ya  chipulumutso ndi malo anga okwezeka achitetezo.+ Iye ndi malo anga  othawirako,+  Mpulumutsi wanga.+  Mumandipulumutsa  ku chiwawa.+   Ndidzaitanira pa Yehova, Iye woyenera kutamandidwa,+ Ndipo adzandipulumutsa kwa adani anga.+   Pakuti mafunde akupha anandizungulira.+ Panali chikhamu cha anthu opanda pake amene anali kundiopseza.+   Zingwe za Manda* zinandizungulira.+ Ndinakumana ndi misampha ya imfa.+   Pa nthawi ya zowawa zanga ndinaitana Yehova,+ Ndinaitana Mulungu wanga.+ Pamenepo iye anamva mawu anga ali m’kachisi wake,+ Makutu ake anamva kulira kwanga kopempha thandizo.+   Dziko lapansi linayamba kugwedezekera uku ndi uku ndiponso kutekeseka.+ Maziko a kumwamba anagwedezeka.+ Anagwedezekera uku ndi uku chifukwa Mulungu anakwiya.+   Utsi unatuluka m’mphuno mwake, ndipo moto wotuluka m’kamwa mwake unanyeketsa.+ Makala onyeka anatuluka mwa iye.+ 10  Iye anaweramitsa kumwamba n’kutsika.+ Mdima wandiweyani unali kunsi kwa mapazi ake.+ 11  Iye anafika atakwera pakerubi+ wouluka. Anaonekera pamapiko a cholengedwa chauzimu.*+ 12  Kenako anaika mdima momuzungulira ngati misasa,+ Anaika madzi akuda ndi mtambo wakuda.+ 13  M’kuwala kochokera pamaso pake munatuluka makala oyaka moto.+ 14  Ali kumwamba, Yehova anayamba kugunda ngati mabingu,+ Wam’mwambamwamba anayamba kutulutsa mawu ake.+ 15  Anayamba kuponya mivi kuti awabalalitse.+ Anaponya mphezi kuti awasokoneze.+ 16  Ndipo ngalande za pansi pa nyanja zinaonekera,+ Maziko a dziko lapansi+ anakhala poonekera, Zinatero chifukwa cha kudzudzula kwa  Yehova, chifukwa  cha mphamvu  ya mpweya wa  m’mphuno mwake.+ 17  Anatambasula dzanja lake kuchokera kumwamba ndi kunditenga,+ Anandivuula m’madzi akuya.+ 18  Anandilanditsa kwa mdani wanga wamphamvu,+ Anandilanditsa kwa odana nane chifukwa anali amphamvu kuposa ine.+ 19  Adaniwo anandifikira m’tsiku la tsoka langa,+ Koma Yehova  anandichirikiza.+ 20  Ananditenga ndi kundiika pamalo otakasuka.+ Anandipulumutsa chifukwa anakondwera nane.+ 21  Yehova amandipatsa mphoto mogwirizana ndi chilungamo changa.+ Amandibwezera mogwirizana ndi kuyera kwa manja anga.+ 22  Pakuti ndasunga njira za Yehova,+ Sindinachoke kwa Mulungu wanga.+ Ndikanatero, ndikanachita chinthu choipa. 23  Pakuti zigamulo+ zake zonse zili pamaso panga. Ndipo sindidzapatuka pa malamulo ake.+ 24  Ndidzakhalabe wopanda cholakwa+ pamaso pake, Ndipo ndidzayesetsa kupewa cholakwa.+ 25  Yehova andibwezere mogwirizana ndi chilungamo changa,+ Andibwezere mogwirizana ndi kukhala kwanga woyera pamaso pake.+ 26  Munthu wokhulupirika, mudzamuchitira mokhulupirika.+ Munthu wamphamvu wopanda cholakwa, mudzamuchitira mwachilungamo.+ 27  Kwa munthu wokhalabe woyera, mudzadzisonyeza kuti ndinu woyera,+ Kwa munthu wopotoka maganizo mudzachita zinthu ngati wopusa.+ 28  Anthu odzichepetsa mudzawapulumutsa.+ Koma mumatsutsa odzikweza, kuti muwatsitse.+ 29  Inu Yehova ndinu nyale yanga,+ Ndipo Yehova ndiye amandiunikira pamene ndili mu mdima.+ 30  Pakuti ndi thandizo lanu ndingathamangitse  gulu la achifwamba.+ Ndi thandizo la Mulungu wanga ndingakwere khoma.+ 31  Njira ya Mulungu woona ndi yangwiro.+ Mawu a Yehova ndi oyengeka bwino.+ Iye ndi chishango kwa onse othawira kwa iye.+ 32  Kodi pali Mulungu winanso woposa Yehova?+ Kodi pali thanthwe linanso loposa Mulungu wathu?+ 33  Mulungu woona ndiye malo anga otetezeka kwambiri,+ Ndipo adzasalaza njira yanga.+ 34  Iye adzachititsa mapazi anga kukhala aliwiro ngati a mbawala zazikazi,+ Ndipo adzandiimiritsabe pamalo okwezeka kwa ine.+ 35  Iye akuphunzitsa manja anga kumenya nkhondo.+ Ndipo manja anga akukunga uta wamkuwa.+ 36  Inu mudzandipatsa chishango chanu cha chipulumutso,+ Ndipo kudzichepetsa kwanu n’kumene kumandikweza.+ 37  Mudzakulitsa malo opondapo mapazi anga.+ Ndipo mapazi anga sadzagwedezeka.+ 38  Ndidzathamangitsa adani anga kuti ndiwafafanize, Ndipo sindidzabwerera kufikira nditawawononga onse.+ 39  Ndidzawawononga onse ndi kuwaphwanya zibenthuzibenthu+ kuti asadzukenso.+ Iwo adzagwa pansi ndipo ndidzawapondaponda ndi mapazi anga.+ 40  Inu mudzandiveka mphamvu kuti ndithe kumenya nkhondo.+ Mudzakomola ondiukira.+ 41  Koma mudzachititsa adani anga kugonja* pamaso panga,+ Anthu odana nane kwambiri, ndidzawakhalitsa chete.+ 42  Adzafuula kupempha thandizo, koma sipadzapezeka wowapulumutsa,+ Adzafuulira Yehova, koma sadzawayankha.+ 43  Ndidzawapera kukhala ngati fumbi la padziko lapansi. Ndidzawapondaponda ngati matope a mumsewu,+ Ndipo ndidzawasasantha. 44  Inu mudzandipulumutsa kwa anthu a mtundu wanga onditola zifukwa.+ Mudzanditeteza kuti ndikhale mtsogoleri wa mitundu yonse.+ Anthu amene sindikuwadziwa adzanditumikira.+ 45  Alendo adzabwera kwa ine akunthunthumira.+ Anthu adzamvetsera mawu anga ndi kuwatsatira.+ 46  Alendo adzatha mphamvu, Ndipo adzatuluka m’malo awo achitetezo akunjenjemera.+ 47  Yehova ndi wamoyo.+ Lidalitsike Thanthwe langa.+ Mulungu wanga, thanthwe limene limandipulumutsa likhale lokwezeka.+ 48  Mulungu woona ndiye Wobwezera adani anga,+ Iye amaika mitundu ya anthu kunsi kwa mapazi anga.+ 49  Iye amandichotsa pakati pa adani anga.+ Ndipo mudzandikweza pamwamba pa anthu amene amandiukira.+ Mudzandilanditsa kwa munthu wochita zachiwawa.+ 50  N’chifukwa chake ndidzayamika inu Yehova pakati pa mitundu.+ Ndipo ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu.+ 51  Ndidzaimbira Iye wochita ntchito zazikulu zachipulumutso kwa mfumu yake,+ Iye wosonyeza kukoma mtima kosatha kwa wodzozedwa wake,+ Kwa Davide ndi mbewu yake mpaka kalekale.”+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa 1Sa 2:1.
Onani Zakumapeto 5.
Kapena kuti “mapiko a mphepo.”
Kapena kuti, “Mudzandipatsa kumbuyo kwa khosi la adani anga.”