Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

2 Petulo 1:1-21

1  Ine Simoni Petulo, kapolo+ ndi mtumwi+ wa Yesu Khristu, ndikulembera anthu amene apeza chikhulupiriro chofanana ndi chathu,+ mwa chilungamo+ cha Mulungu wathu ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.+  Ndikufuna kuti mulandire kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere wowonjezereka.+ Kuti muchite zimenezi, mumudziwe molondola+ Mulungu ndi Yesu Ambuye wathu.  Pakuti Mulungu, mwa mphamvu yake, watipatsa kwaulere zinthu zonse zofunika kuti munthu akhale moyo+ wodzipereka kwa Mulungu.+ Talandira zinthu zimenezi kudzera mwa kudziwa molondola za iye amene anatiitana,+ kudzera mu ulemerero+ ndi ubwino wake.  Kudzera mwa zimenezi, iye watilonjeza zinthu zamtengo wapatali ndi zazikulu kwambiri,+ kuti mwa malonjezo amenewa mukhale ndi makhalidwe+ a Mulungu.+ Iye watipatsa kwaulere malonjezo amenewa chifukwa tapulumuka ku khalidwe loipa limene lili m’dzikoli,+ limene limayamba chifukwa cha chilakolako choipa.  Pa chifukwa chimenechi, inunso yesetsani mwakhama+ kuwonjezera pa chikhulupiriro chanu makhalidwe abwino,+ pa makhalidwe anu abwino muwonjezerepo kudziwa zinthu,+  pa kudziwa zinthu kudziletsa, pa kudziletsa+ kupirira, pa kupirira kudzipereka kwa Mulungu,+  pa kudzipereka kwa Mulungu kukonda abale, pa kukonda abale, chikondi.+  Ngati zinthu zimenezi zili mwa inu ndipo zikusefukira, zidzakutetezani kuti musakhale ozilala kapena osabala zipatso+ pa zimene mukuchita mogwirizana ndi kumudziwa molondola Ambuye wathu Yesu Khristu.  Munthu amene alibe zinthu zimenezi ndi wakhungu, wotseka maso ake kuti asaone kuwala,+ ndipo waiwala+ kuti anayeretsedwa+ ku machimo ake akale. 10  Pa chifukwa chimenechi abale, chitani chilichonse chotheka kuti mukhalebe okhulupirika, n’cholinga choti mupitirizebe kukhala pakati pa anthu amene Mulungu wawaitana+ ndi kuwasankha,+ pakuti mukapitiriza kuchita zinthu zimenezi simudzalephera ngakhale pang’ono.+ 11  Ndipo mukatero, adzakutsegulirani khomo kuti mulowe+ mwaulemerero mu ufumu wosatha+ wa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.+ 12  Pa chifukwa chimenechi, nthawi zonse ndizikukumbutsani+ zinthu zimenezi, ngakhale kuti mukuzidziwa kale ndipo ndinu olimba m’choonadi+ chimene munachilandira.+ 13  Chotero ndikuona kuti n’koyenera kumakugwedezani mwa kukukumbutsani+ pamene ndidakali mumsasa uno,+ 14  popeza ndikudziwa kuti ndatsala pang’ono kutuluka mumsasa wangawu,+ monga momwe Ambuye wathu Yesu Khristu anandisonyezera.+ 15  Choncho nthawi zonse ndizichita chilichonse chotheka, kuti ndikadzachoka+ mudzathe kukumbukira zinthu zimenezi. 16  Ndithudi, pamene ifeyo tinakudziwitsani za mphamvu ya Ambuye wathu Yesu Khristu ndi za kukhalapo* kwake,+ sitinatengere nkhani zabodza zopekedwa mochenjera ndi anthu,+ koma tinachita zimenezo chifukwa tinachita kuona ndi maso athu ulemerero wake.+ 17  Pakuti iye analandira ulemu ndi ulemerero kuchokera kwa Mulungu Atate,+ pamene mawu anamveka kwa iye kuchokera mu ulemerero waukulu, kuti: “Uyu ndiye mwana wanga wokondedwa, amene ndikukondwera naye.”+ 18  Zoonadi, mawu amenewa tinawamva+ kuchokera kumwamba tili naye limodzi m’phiri loyera.+ 19  Choncho mawu aulosiwa+ ndi odalirika kwambiri,+ ndipo mukuchita bwino kuwaganizira mozama. Mawu amenewo ali ngati nyale+ imene ikuwala mu mdima, m’mitima yanu, mpaka m’bandakucha, nthanda*+ ikadzatuluka. 20  Choyamba, mukudziwa kuti ulosi wa m’Malemba suchokera m’maganizo a munthu.+ 21  Chifukwa ulosi sunayambe wanenedwapo mwa kufuna kwa munthu,+ koma anthu analankhula mawu ochokera kwa Mulungu+ motsogoleredwa ndi mzimu woyera.+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 8.
“Nthanda” ndi nyenyezi yomalizira kutuluka imene imaonekera dzuwa likangotsala pang’ono kutuluka.