Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

2 Mbiri 9:1-31

9  Mfumukazi ya ku Sheba+ inamva za Solomo. Choncho inabwera ku Yerusalemu kuti idzamuyese Solomo pomufunsa mafunso ovuta.+ Mfumukaziyo inabwera ndi anthu oiperekeza ambiri, ndiponso ngamila+ zitanyamula mafuta a basamu,+ golide+ wambiri, ndi miyala yamtengo wapatali.+ Inafika kwa Solomo n’kuyamba kumuuza zonse zimene zinali kumtima kwake.+  Solomo anaiyankha mfumukaziyo mafunso ake onse.+ Panalibe chimene Solomo analephera kuyankha.+  Mfumukazi ya ku Sheba itaona nzeru za Solomo,+ nyumba imene anamanga,+  chakudya cha patebulo pake,+ mmene atumiki ake anali kukhalira pa nthawi ya chakudya, mmene atumiki ake operekera zakudya anali kuchitira, zovala zawo,+ anthu ake operekera zakumwa+ ndi zovala zawo, ndi nsembe zake zopsereza+ zimene ankapereka panyumba ya Yehova nthawi zonse,+ inazizira nkhongono ndipo inasowa chonena.  Choncho inauza mfumuyo kuti: “Nkhani za zochita zanu ndi nzeru zanu zimene ndinamva kudziko langa, n’zoonadi.+  Sindinakhulupirire+ mawuwo mpaka pamene ndabwera n’kuona ndi maso anga,+ ndipo ndaona kuti ndinangouzidwa hafu chabe ya nzeru zanu zochuluka.+ Mwaposa zinthu zimene ndinamva.+  Odala+ anthu anu, odala atumiki anuwa amene amatumikira pamaso panu nthawi zonse, n’kumamva nzeru zanu.+  Adalitsike Yehova Mulungu wanu,+ amene wasangalala+ nanu mwa kukuikani pampando wake wachifumu+ monga mfumu yolamulira m’malo mwa Yehova Mulungu wanu.+ Popeza Mulungu wanu anakonda+ Isiraeli kuti akhalepo mpaka kalekale, wakuikani kuti mukhale mfumu yawo,+ kuti muzipereka zigamulo+ ndi kuchita chilungamo.”+  Kenako mfumukaziyo inapatsa mfumuyo golide wokwana matalente* 120,+ mafuta a basamu+ ochuluka zedi, ndi miyala yamtengo wapatali.+ Mafuta a basamu amene mfumukazi ya ku Sheba inapatsa Mfumu Solomo, anali ochuluka kwambiri moti sipanakhalenso mafuta ochuluka ngati amenewo.+ 10  Kuwonjezera pamenepo, atumiki a Hiramu+ ndi atumiki a Solomo amene anabwera ndi golide+ kuchokera ku Ofiri, anabweretsanso matabwa a mtengo wa m’bawa+ ndi miyala yamtengo wapatali.+ 11  Mfumuyo inapanga masitepe a nyumba ya Yehova ndi a nyumba ya mfumu+ pogwiritsira ntchito matabwa a m’bawawo.+ Inapanganso azeze+ ndi zoimbira za zingwe+ n’kupatsa oimba.+ Zinthu zamtundu umenewu zinali zisanaonekepo m’dziko la Yuda. 12  Mfumu Solomo inapatsa mfumukazi+ ya ku Sheba zofuna zake zonse zimene inapempha. Solomo anapatsa mfumukaziyo zinthu zoposa zimene inabweretsa kwa iye. Pambuyo pake, mfumukaziyo inatembenuka n’kubwerera kudziko lake, pamodzi ndi antchito ake.+ 13  Golide amene ankabwera kwa Solomo chaka chimodzi, anali wolemera matalente 666,*+ 14  osawerengera golide wa amalonda oyendayenda,+ amalonda ena amene anali kubweretsa katundu, mafumu onse a Aluya,+ ndi abwanamkubwa a m’dzikolo amene anali kubweretsa golide ndi siliva kwa Solomo. 15  Mfumu Solomo inapanga zishango 200 zikuluzikulu zagolide wosakaniza ndi zitsulo zina.+ (Chishango chachikulu chilichonse anachikuta ndi golide wosakaniza ndi zitsulo zina wolemera masekeli 600.)+ 16  Inapanganso zishango 300 zing’onozing’ono zagolide wosakaniza ndi zitsulo zina. (Chishango chaching’ono chilichonse anachikuta ndi golide wolemera ma mina* atatu.)+ Kenako mfumuyo inaika zishangozi m’nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni.+ 17  Itatero, mfumuyo inapanga mpando wachifumu waukulu wa minyanga ya njovu, n’kuukuta ndi golide woyenga bwino.+ 18  Panali masitepe 6 okafika kumpando wachifumuwo. Mpando wachifumuwo unali ndi chopondapo mapazi chagolide (ziwirizi zinali zolumikizana). Mpandowo unali ndi moika manja mbali zonse ziwiri. M’mphepete mwake munali zifaniziro ziwiri za mikango+ itaimirira.+ 19  Pamasitepe 6 amenewo, panali zifaniziro 12 za mikango+ itaimirira, mbali iyi ndi iyi. Panalibenso ufumu wina umene unali ndi mpando wachifumu ngati umenewo.+ 20  Ziwiya zonse zomweramo+ Mfumu Solomo zinali zagolide,+ ndipo ziwiya zonse za m’nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni+ zinali zagolide woyenga bwino. Panalibe chiwiya chasiliva. Siliva sankaoneka ngati kanthu+ m’masiku a Solomo, 21  pakuti zombo za mfumu zinkapita ku Tarisi+ limodzi ndi atumiki a Hiramu.+ Kamodzi pa zaka zitatu zilizonse, zombo za ku Tarisizo zinkabweretsa golide, siliva,+ minyanga ya njovu,+ anyani, ndi mbalame zotchedwa pikoko.+ 22  Chotero Mfumu Solomo inali yolemera kwambiri+ ndiponso yanzeru kwambiri+ kuposa mafumu ena onse a padziko lapansi. 23  Mafumu onse a padziko lapansi ankafuna kuonana+ ndi Solomo, kuti amve nzeru zake+ zimene Mulungu woona anaika mumtima mwake.+ 24  Aliyense anali kubweretsa mphatso+ chaka chilichonse monga zinthu zasiliva, zinthu zagolide,+ zovala,+ zida zankhondo, mafuta a basamu, mahatchi, ndi nyulu.*+ 25  Solomo anakhala ndi makola 4,000 a mahatchi.+ Analinso ndi magaleta+ ndi mahatchi ankhondo okwana 12,000. Zimenezi anali kuzisunga m’mizinda yosungiramo magaleta+ ndiponso pafupi ndi mfumuyo ku Yerusalemu. 26  Solomo anakhala wolamulira wa mafumu onse kuyambira ku Mtsinje* mpaka kudziko la Afilisiti, n’kukafika kumalire ndi Iguputo.+ 27  Kuwonjezera apo, mfumuyo inachititsa kuti ku Yerusalemu siliva akhale wochuluka kwambiri ngati miyala, ndiponso kuti matabwa a mkungudza+ akhale ochuluka kwambiri+ ngati mitengo ya mkuyu ya ku Sefela.+ 28  Anthu anali kubweretsa mahatchi+ kwa Solomo kuchokera ku Iguputo+ ndi mayiko ena onse. 29  Nkhani zina zokhudza Solomo,+ zoyambirira ndi zomalizira, zinalembedwa m’mawu a mneneri Natani.+ Zalembedwanso mu ulosi wa Ahiya+ Msilo,+ ndiponso m’buku la masomphenya a Ido+ wamasomphenya, lonena za Yerobowamu+ mwana wa Nebati.+ 30  Solomo analamulira Isiraeli yense ku Yerusalemu zaka 40. 31  Pomalizira pake Solomo anagona pamodzi ndi makolo ake, ndipo anaikidwa m’manda mu Mzinda wa Davide bambo ake.+ Kenako mwana wake Rehobowamu,+ anayamba kulamulira m’malo mwake.+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 12.
Onani Zakumapeto 12.
Onani Zakumapeto 12.
Onani mawu a m’munsi pa 2Sa 13:29.
Umenewu ndi mtsinje wa Firate.