Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

2 Mbiri 7:1-22

7  Tsopano Solomo atangomaliza kupemphera,+ moto unatsika kuchokera kumwamba.+ Motowo unanyeketsa nsembe yopsereza+ pamodzi ndi nsembe zina, ndipo ulemerero wa Yehova+ unadzaza nyumbayo.  Chotero ansembe sanathe kulowa m’nyumba ya Yehova+ chifukwa ulemerero wa Yehova unadzaza nyumba ya Yehova.  Ana onse a Isiraeli anali kuonerera pamene moto unali kutsika, ndiponso pamene ulemerero wa Yehova unaonekera pamwamba pa nyumbayo. Ataona zimenezi, nthawi yomweyo anagwada+ n’kuwerama mpaka nkhope zawo pansi+ ndi kuyamika Yehova, “chifukwa iye ndi wabwino,+ pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhala mpaka kalekale.”+  Kenako mfumuyo ndi anthu onse anapereka nsembe pamaso pa Yehova.+  Mfumu Solomo inapereka nsembe ya ng’ombe 22,000 ndi nkhosa 120,000.+ Choncho mfumuyo ndi anthu onse anatsegulira+ nyumba ya Mulungu woona.  Ansembe+ anali ataimirira m’malo awo a ntchito pamodzi ndi Alevi,+ onse atanyamula zipangizo zoimbira+ Yehova nyimbo zimene Davide+ mfumu anapanga kuti aziyamikira Yehova. Aleviwo anali kunena kuti “pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhala mpaka kalekale.” Iwo ankanena zimenezi paliponse pamene Davide akanatamanda Mulungu kudzera mwa iwo. Ansembe anali kuimba malipenga+ mokweza patsogolo pawo, Aisiraeli onse ataimirira.  Solomo anapatula+ malo a pakati pa bwalo la nyumba ya Yehova, chifukwa pamenepo anaperekerapo nsembe zopsereza,+ ndi mafuta a nsembe zachiyanjano. Anatero popeza guwa lansembe lamkuwa+ limene iye anamanga linachepa, ndipo sipakanakwana nsembe yopsereza, nsembe yambewu,+ ndi mafuta oundana.+  Pa nthawi imeneyo Solomo anachita chikondwerero+ masiku 7 pamodzi ndi Aisiraeli onse.+ Unali mpingo waukulu+ wa anthu amene anachokera kumadera osiyanasiyana, kuyambira polowera ku Hamati+ n’kutsetsereka mpaka kukafika kuchigwa* cha Iguputo.+  Koma pa tsiku la 8 anachita msonkhano wapadera+ chifukwa kwa masiku 7 anali kutsegulira guwa lansembe ndipo kwa masiku 7 ena anali kuchita chikondwerero. 10  Pa tsiku la 23 la mwezi wa 7, Solomo anauza anthuwo kuti azipita kwawo. Iwo anapita akusangalala+ komanso akumva bwino mumtima, chifukwa cha zabwino+ zimene Yehova anachitira Davide, Solomo, ndiponso zimene anachitira anthu ake Aisiraeli.+ 11  Choncho Solomo anamaliza kumanga nyumba ya Yehova+ ndi nyumba ya mfumu.+ Zilizonse zimene iye anaganiza kuchita mumtima mwake zokhudza nyumba ya Yehova ndi nyumba yake zinayenda bwino. 12  Kenako Yehova anaonekera+ kwa Solomo usiku n’kumuuza kuti: “Ndamva pemphero lako+ ndipo ndasankha+ malo ano kukhala nyumba yanga yoperekeramo nsembe.+ 13  Ndikatseka kumwamba kuti mvula isagwe,+ ndikalamula dzombe kuti lidye zomera za m’dzikoli,+ ndikatumiza mliri pakati pa anthu anga,+ 14  ndipo anthu anga+ otchedwa ndi dzina langa+ akadzichepetsa+ n’kupemphera,+ n’kufunafuna nkhope yanga,+ n’kusiya njira zawo zoipa,+ ine ndidzamva ndili kumwamba+ n’kuwakhululukira tchimo lawo+ ndipo ndidzachiritsa dziko lawo.+ 15  Tsopano maso anga+ akhala otseguka ndipo makutu anga+ azimvetsera mapemphero onenedwa pamalo ano. 16  Ndasankha+ ndi kuyeretsa nyumba ino kuti dzina langa+ likhale pamenepa mpaka kalekale,+ ndipo maso anga ndi mtima wanga zidzakhala pamenepa nthawi zonse.+ 17  “Iweyo ukayenda pamaso panga monga momwe Davide+ bambo ako anayendera, mwa kuchita zonse zimene ndakulamula+ ndi kusunga malangizo anga+ ndi zigamulo zanga,+ 18  inenso ndidzakhazikitsa mpando wako wachifumu,+ monga momwe ndinapanganirana ndi Davide bambo ako+ kuti, ‘Munthu wa m’banja lako sadzachoka pampando wachifumu wa Isiraeli.’+ 19  Koma inuyo mukadzabwerera+ n’kusiya kutsatira malamulo anga+ amene ndakupatsani, komanso mukadzapita kukatumikira milungu ina+ ndi kuigwadira,+ 20  ineyo ndidzakuchotsani padziko langa limene ndakupatsani+ ndipo nyumba iyi yomwe ndaiyeretsa+ chifukwa cha dzina langa, ndidzaichotsa pamaso panga.+ Ndidzachititsa anthu kuipekera mwambi+ ndi kuitonza pakati pa mitundu yonse ya anthu.+ 21  Ndipo nyumba iyi ikadzakhala bwinja,+ aliyense wodutsa pafupi nayo adzayang’ana modabwa,+ ndipo ndithu adzati, ‘N’chifukwa chiyani Yehova anachita zimenezi padzikoli ndi panyumbayi?’+ 22  Ndipo adzati, ‘N’chifukwa chakuti anasiya Yehova+ Mulungu wa makolo awo amene anawatulutsa m’dziko la Iguputo.+ M’malomwake anatenga milungu ina+ n’kumaigwadira ndi kuitumikira.+ N’chifukwa chake iye anawabweretsera tsoka lonseli.’”+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.