Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

2 Mbiri 6:1-42

6  Panali pa nthawi imeneyi pamene Solomo anati:+ “Yehova anati adzakhala mumdima wandiweyani.+  Koma ine ndakumangirani nyumba yomwe ndi malo anu okhalamo okwezeka,+ malo okhazikika oti mukhalemo mpaka kalekale.”+  Kenako mfumu inatembenuka n’kuyang’ana anthuwo. Ndiyeno inayamba kudalitsa+ mpingo wonse wa Isiraeli. Pamenepo n’kuti mpingo wonse wa Isiraeli utaimirira.+  Mfumuyo inapitiriza kuti: “Adalitsike Yehova Mulungu wa Isiraeli,+ amene analankhula ndi pakamwa pake kwa Davide bambo anga,+ ndipo ndi manja ake wakwaniritsa+ zimene ananena, kuti,  ‘Kuchokera tsiku limene ndinatulutsa anthu anga m’dziko la Iguputo, sindinasankhe mzinda m’mafuko onse a Isiraeli woti iwo amangeko nyumba ya dzina langa+ kuti likhale kumeneko, ndipo sindinasankhe munthu woti akhale mtsogoleri wa anthu anga Aisiraeli.+  Koma ndidzasankha Yerusalemu+ kuti dzina langa likhale kumeneko, ndiponso ndidzasankha Davide kuti alamulire anthu anga Aisiraeli.’+  Ndipo bambo anga Davide, anafuna mumtima mwawo kumanga nyumba ya dzina la Yehova Mulungu wa Isiraeli.+  Koma Yehova anauza Davide bambo anga kuti, ‘Popeza unafuna mumtima mwako kumanga nyumba ya dzina langa, unachita bwino chifukwa unafuna mumtima mwako kuchita zimenezi.+  Koma iweyo sumanga nyumbayi,+ m’malomwake mwana wako wamwamuna wotuluka m’chiuno mwako ndi amene adzamange nyumba ya dzina langa.’+ 10  Yehova anakwaniritsa mawu+ amene ananena, kuti ineyo ndilowe m’malo mwa Davide bambo anga+ n’kukhala pampando wachifumu+ wa Isiraeli, monga momwe Yehova ananenera,+ ndiponso kuti ndimange nyumba ya dzina la Yehova Mulungu wa Isiraeli.+ 11  Komanso kuti m’nyumbamo ndiikemo Likasa,+ lomwe muli pangano la Yehova limene anapangana ndi ana a Isiraeli.”+ 12  Tsopano Solomo anaimirira patsogolo pa guwa lansembe la Yehova patsogolo pa mpingo wonse wa Isiraeli.+ Kenako anatambasula manja ake.+ 13  (Pakuti Solomo anapanga nsanja+ yamkuwa n’kuiika pakati pa bwalo lamkati.+ Nsanjayo inali yaikulu mikono isanu m’litali, mikono isanu m’lifupi, ndipo kuchokera pansi kufika pamwamba inali yaitali mikono itatu. Iye anaimirira pansanjayo.) Atatero anagwada+ patsogolo pa mpingo wonse wa Isiraeli. Kenako anatambasula manja ake n’kuwakweza kumwamba.+ 14  Ndiyeno anayamba kulankhula kuti: “Inu Yehova Mulungu wa Isiraeli,+ palibe Mulungu wina wofanana ndi inu+ kumwambako kapena pansi pano. Atumiki anu amene akuyenda pamaso panu ndi mtima wawo wonse, inu mumawasungira pangano+ ndi kuwasonyeza kukoma mtima kosatha.+ 15  Mwakwaniritsa lonjezo limene munalonjeza mtumiki wanu Davide bambo anga.+ Munalonjeza ndi pakamwa panu ndipo lero mwakwaniritsa ndi dzanja lanu.+ 16  Tsopano inu Yehova Mulungu wa Isiraeli, sungani lonjezo limene munalonjeza mtumiki wanu Davide bambo anga lakuti, ‘Anthu a m’banja lako sadzasiya kukhala pamaso panga pampando wachifumu wa Isiraeli.+ Chofunika n’choti ana ako+ asamale mayendedwe awo mwa kuyenda motsatira malamulo anga+ monga momwe iwe wayendera pamaso panga.’+ 17  Tsopano inu Yehova Mulungu wa Isiraeli,+ lonjezo lanu+ limene munalonjeza mtumiki wanu Davide likwaniritsidwe.+ 18  “Koma kodi Mulungu angakhaledi ndi anthu padziko lapansi?+ Taonani! Kumwamba, ngakhale kumwambamwamba, simungakwaneko.+ Kuli bwanji nyumba imene ndamangayi?+ 19  Mutembenukire ku pemphero la mtumiki wanu+ ndi pempho lake lopempha chifundo,+ inu Yehova Mulungu wanga. Mverani kulira kwanga kochonderera+ ndi pemphero limene ine mtumiki wanu ndikupemphera pamaso panu.+ 20  Maso anu akhale akuyang’ana+ nyumba ino usana ndi usiku. Akhale akuyang’ana malo amene munanena kuti mudzaikako dzina lanu,+ mwa kumvetsera pemphero limene mtumiki wanu akupemphera atayang’ana malo ano.+ 21  Mumve mapemphero ochonderera a mtumiki+ wanu ndi a anthu anu Aisiraeli, pamene akupemphera atayang’ana malo ano.+ Inuyo mumve muli kumalo anu okhala, kumwamba,+ ndipo mumve n’kukhululuka.+ 22  “Munthu akachimwira mnzake+ n’kuchita lumbiro lokhala ndi temberero+ potsimikiza kuti sanachimwe, iye n’kubwera pamaso pa guwa lansembe m’nyumba ino ali pansi pa tembererolo,+ 23  inu mumve muli kumwamba+ ndipo muchitepo kanthu+ mwa kusonyeza amene ali wolakwa pom’bwezera temberero lake,+ ndi kusonyeza amene ali wolungama+ pom’patsa mphoto malinga ndi chilungamo chake.+ 24  “Anthu anu Aisiraeli akagonja kwa mdani wawo+ chifukwa choti anali kukuchimwirani,+ ndiyeno akabwerera+ kwa inu n’kutamanda dzina lanu+ ndi kupemphera+ ndiponso kupempha kuti muwachitire chifundo pamaso panu m’nyumba ino,+ 25  inuyo mumve muli kumwamba+ ndipo mukhululuke+ tchimo la anthu anu Aisiraeli, ndi kuwabwezeretsa+ kudziko limene munapatsa iwo ndi makolo awo.+ 26  “Kumwamba kukatsekeka, mvula n’kumakanika kugwa+ chifukwa choti anali kukuchimwirani,+ ndiyeno iwo n’kupemphera atayang’ana malo ano,+ ndi kutamanda dzina lanu ndiponso kusiya tchimo lawo chifukwa choti mwakhala mukuwasautsa,+ 27  inuyo mumve muli kumwamba ndipo mukhululuke tchimo la atumiki anu, anthu anu Aisiraeli, popeza mumawaphunzitsa+ njira yabwino+ yoti ayendemo. Mubweretse mvula+ padziko lanu, limene mwapatsa anthu anu monga cholowa.+ 28  “M’dzikomo mukagwa njala,+ mliri,+ mphepo yotentha yowononga mbewu,+ matenda a mbewu a chuku,+ dzombe,+ mphemvu,+ komanso adani+ awo akawaukira m’zipata za mizinda yawo,+ ndiponso kukagwa mliri wamtundu wina uliwonse, nthenda yamtundu wina uliwonse,+ 29  ndiyeno anthuwo akapereka pemphero lililonse,+ pempho lililonse lopempha chifundo+ limene munthu aliyense kapena anthu anu onse Aisiraeli+ angapemphe, chifukwa aliyense wa iwo akudziwa mliri wake+ ndi ululu wake, ndipo aliyense akatambasula manja ake kuwalozetsa kunyumba ino,+ 30  inuyo mumve muli kumwamba, malo anu okhala okhazikika,+ ndipo mukhululuke+ ndi kuchitapo kanthu. Mupatse aliyense malinga ndi njira zake zonse,+ popeza mukudziwa mtima wake+ (popeza inu nokha ndiye mumadziwa bwino mtima wa ana a anthu).+ 31  Muchite zimenezi n’cholinga choti iwo akuopeni,+ mwa kuyenda m’njira zanu masiku onse amene angakhale ndi moyo padziko limene munapatsa makolo athu.+ 32  “Komanso mlendo amene sali mmodzi wa anthu anu Aisiraeli,+ amene wabwera kuchokera kudziko lakutali chifukwa cha dzina lanu lalikulu,+ ndi dzanja lanu lamphamvu+ ndi mkono wanu wotambasuka,+ ndipo iwo abwera n’kupemphera atayang’ana nyumba ino,+ 33  inuyo mumve muli kumwamba, malo anu okhala okhazikika,+ ndipo muchite mogwirizana ndi zonse zimene mlendoyo wakupemphani.+ Mutero n’cholinga choti anthu a mitundu yonse ya padziko lapansi adziwe dzina lanu,+ kuti akuopeni+ mofanana ndi mmene anthu anu Aisiraeli amachitira, ndiponso kuti adziwe kuti dzina lanu lili panyumba imene ndamangayi.+ 34  “Anthu anu akapita ku nkhondo+ kukamenyana ndi adani awo kumene inuyo mwawatumiza,+ ndipo akapemphera+ kwa inu atayang’ana kumzinda umene mwasankha ndi kunyumba ya dzina lanu imene ndamanga,+ 35  inuyo mumve muli kumwamba pemphero lawo ndi pempho lawo lopempha chifundo,+ ndipo muwachitire chilungamo.+ 36  “Anthu anu akakuchimwirani+ (popeza palibe munthu amene sachimwa)+ inu n’kuwakwiyira, n’kuwapereka kwa mdani, adani awowo n’kuwagwira kupita nawo kudziko lakutali kapena lapafupi,+ 37  ndiyeno iwo akazindikira kulakwa kwawo m’dziko limene anawatengeralo n’kulapa, ndipo akapempha chifundo kwa inu m’dziko limene akukhalamo monga anthu ogwidwa,+ n’kunena kuti, ‘Tachimwa,+ tachita zolakwa,+ ndiponso tachita zinthu zoipa,’+ 38  n’kubwerera kwa inu ndi mtima wawo wonse+ ndi moyo wawo wonse, m’dziko limene akukhalamo monga anthu ogwidwa,+ m’dziko la adani awo amene anawagwira ndiponso akapemphera kwa inu atayang’ana kudziko lawo limene munapatsa makolo awo, kumzinda umene mwasankha+ ndiponso kunyumba ya dzina lanu imene ndamangayi,+ 39  inuyo mumve muli kumwamba, malo anu okhala okhazikika.+ Mumve pemphero lawo ndi pempho lawo lopempha chifundo,+ ndipo muwachitire chilungamo.+ Mukhululukire+ anthu anu amene akuchimwirani. 40  “Tsopano Mulungu wanga, chonde, maso anu aone,+ ndipo makutu anu+ akhale tcheru kumvetsera pemphero lokhudza malo ano. 41  Tsopano inu Yehova Mulungu nyamukani+ mulowe mu mpumulo wanu,+ inuyo ndi Likasa limene mumasonyezera mphamvu zanu.+ Ansembe anu, inu Yehova Mulungu, avale chipulumutso ndipo okhulupirika anu asangalale chifukwa cha zabwino.+ 42  Inu Yehova Mulungu, musakane wodzozedwa wanu.+ Musaiwale kukoma mtima kosatha kumene munasonyeza Davide mtumiki wanu.”+

Mawu a M'munsi