Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

2 Mbiri 36:1-23

36  Kenako anthu a m’dzikolo anatenga Yehoahazi+ mwana wa Yosiya n’kumulonga ufumu ku Yerusalemu m’malo mwa bambo ake.+  Yehoahazi anali ndi zaka 23 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira miyezi itatu ku Yerusalemu.+  Koma mfumu ya Iguputo inamuchotsa pa udindo wake ku Yerusalemu,+ n’kulamula dzikolo kuti limupatse matalente 100 a siliva*+ ndi talente imodzi ya golide.*  Kuwonjezera apo, mfumu+ ya Iguputo inaika Eliyakimu+ m’bale wa Yehoahazi kukhala mfumu ya Yuda ndi Yerusalemu n’kumusintha dzina kuti akhale Yehoyakimu. Koma Yehoahazi m’bale wakeyo, Neko+ anam’tenga n’kupita naye ku Iguputo.+  Yehoyakimu+ anali ndi zaka 25 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira zaka 11 ku Yerusalemu.+ Iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova Mulungu wake.+  Kenako Nebukadinezara+ mfumu ya Babulo anabwera+ kudzam’manga ndi zomangira ziwiri zamkuwa n’kupita naye ku Babulo.+  Ziwiya zina+ za m’nyumba ya Yehova, Nebukadinezara+ anapita nazo ku Babulo n’kukaziika m’nyumba yake yachifumu.+  Nkhani zina+ zokhudza Yehoyakimu ndi zonyansa+ zimene anachita, ndiponso zoipa zimene zinapezedwa zokhudza iye, zinalembedwa m’Buku+ la Mafumu a Isiraeli ndi Yuda. Kenako Yehoyakini+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.  Yehoyakini+ anali ndi zaka 18 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira miyezi itatu+ ndi masiku 10 ku Yerusalemu. Iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova.+ 10  Kumayambiriro+ kwa chaka, Mfumu Nebukadinezara inatuma+ asilikali ake omwe anakamutenga n’kubwera naye ku Babulo+ limodzi ndi zinthu zabwinozabwino za m’nyumba ya Yehova.+ Kuwonjezera apo, Nebukadinezara analonga ufumu Zedekiya+ yemwe anali m’bale wa bambo ake kukhala mfumu ya Yuda ndi Yerusalemu.+ 11  Zedekiya+ anali ndi zaka 21 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira zaka 11 ku Yerusalemu.+ 12  Iye anapitiriza kuchita zoipa+ pamaso pa Yehova Mulungu wake, ndipo sanadzichepetse+ pamaso pa mneneri+ Yeremiya+ yemwe anapita kwa iye molamulidwa ndi Yehova. 13  Kuwonjezera pamenepo, Zedekiya anapandukira Mfumu Nebukadinezara+ yomwe inali itamulumbiritsa kwa Mulungu,+ ndipo anapitiriza kuumitsa khosi lake ndi mtima wake+ kuti asabwerere kwa Yehova Mulungu wa Isiraeli. 14  Komanso, anthu ndi atsogoleri onse a ansembe+ anachita zosakhulupirika zochuluka kwambiri mofanana ndi zonyansa zonse+ za anthu a mitundu ina. Choncho iwo anaipitsa nyumba ya Yehova imene iye anaiyeretsa ku Yerusalemu.+ 15  Yehova Mulungu wa makolo awo anapitiriza kuwatumizira machenjezo kudzera mwa amithenga ake.+ Anawatumiza mobwerezabwereza chifukwa ankamvera chisoni anthu akewo+ ndiponso malo ake okhala.+ 16  Koma iwo ankangonyogodola+ amithenga a Mulungu woona, kunyoza mawu ake+ ndi kuseka+ aneneri ake, mpaka kufika poti panalibenso chiyembekezo choti angathe kuchiritsidwa.+ Kenako mkwiyo+ wa Yehova unawagwera. 17  Choncho anawabweretsera mfumu ya Akasidi+ yomwe inapha anyamata awo ndi lupanga+ m’nyumba yopatulika.+ Sinachitire chisoni mnyamata kapena namwali, wachikulire kapena nkhalamba yotheratu.+ Mulungu anapereka zonse m’manja mwake. 18  Mfumuyo inatenga ziwiya zonse,+ zazikulu+ ndi zazing’ono, za m’nyumba ya Mulungu woona. Inatenganso chuma+ cha m’nyumba ya Yehova, chuma cha mfumu+ ndi cha akalonga ake. Inatenga chilichonse n’kupita nacho ku Babulo. 19  Iyo inatentha nyumba ya Mulungu woona+ ndi kugwetsa mpanda+ wa Yerusalemu. Ababulowo anatenthanso ndi moto nyumba zonse zokhala ndi mipanda yolimba kwambiri za mzindawo ndi zinthu zake zonse zabwinozabwino,+ mpaka zonse zinawonongedwa.+ 20  Kuwonjezera apo, Nebukadinezara anagwira anthu amene sanaphedwe ndi lupanga ndipo anawatenga kupita nawo ku Babulo.+ Anthuwo anakakhala antchito+ ake ndi a ana ake kufikira pamene ufumu wa Perisiya+ unayamba kulamulira. 21  Zimenezi zinachitika pokwaniritsa mawu a Yehova amene ananena kudzera mwa Yeremiya,+ mpaka pamene dzikolo linalipira masabata ake.+ Masiku onse amene dzikolo linali bwinja linali kusunga sabata mpaka linakwaniritsa zaka 70.+ 22  M’chaka choyamba cha Koresi+ mfumu ya Perisiya,+ Yehova analimbikitsa mtima+ wa Koresi mfumu ya Perisiya kuti mawu a Yehova+ kudzera mwa Yeremiya+ akwaniritsidwe. Pamenepo Koresiyo anatumiza mawu amene analengezedwa mu ufumu wake wonse. Mawuwo analembedwanso m’makalata,+ kuti: 23  “Koresi mfumu ya Perisiya+ wanena kuti, ‘Yehova Mulungu wakumwamba wandipatsa+ maufumu onse a padziko lapansi. Iye wandituma kuti ndim’mangire nyumba ku Yerusalemu m’dziko la Yuda.+ Aliyense amene ali pakati panu mwa anthu onse amene amamutumikira,+ Yehova Mulungu wake akhale naye.+ Choncho apite.’”+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 12.
Onani Zakumapeto 12.